Mkumano wa Ndani?

Malingaliro a Mkumano

Ndi ntchito yakeMonga tikuonera mu

Kalata Yoyamba

yopita ku Akorinto

MALONJE

Buku ili likuperekedwa kwapadera kwa

mkazi wanga wokondedwa, Gladys,

ana athu, Phillip ndi Juliet,

ndi anthu onse a Mulungu.

Mau Oyamba Olembedwa monga mwa buku loyamba

Alipo malingaliro ambiri komanso osiyanasiyana okhudza chikhalidwe ndi udindo wa Mpingo wa Mulungu.

Malingaliro ena ndi okhazikika ngati mapiri ndipo ena akhala akukonzedwabe kufuna kupereka mpata ku maganizo a umunthu mokhudzana ndi zaka zawo.

Malingaliro ochuluka ngakhale kuti ali ndi mfundo za uzimu, amangovumbulutsira poyera umbuli wopitilira umene umunthu unakonza pokhudzana ndi ‘Mpingo wa Mulungu’.

Kunena zoona, mafotokozedwe ake okhawo ndi osokeretsa, matanthauzo ochititsa chisoni ochokera ku mau a Chigiriki.

Mau akuti, /ekklesia/, amatanthauzo oitanidwa, kapena mkumano.

Amakamba za gulu la anthu, amene anapatulidwa kapena kuitanidwa ndi cholinga chapadera onse pamodzi kusiyanitsidwa ku chizolowezi cha kachitidwe ka zinthu, ndi kuikidwa pamodzi ndi cholinga chomangilirika.

Tikawerenga ku Machitidwe 7:38; 19:32, 39, 41 zimaonetsa kuti mau amenewa simau odabwitsa kapena mau a chipembedzo.

Komabe ngati munthu aliyense pakulankhula afanizira chimene chimatchulidwa kuti Mpingo ndi tanthauzo lenileni la Chigiriki, mafunso ochulukirapo amafika m’malingaliro a anthu akumvawo:

Ndani amene anaitana gulu limeneli? Analiyitanira kuchokera ku chiyani? Kupita ku chiyani? Pa cholinga chotani ndi zotsatira zotani?” Amenewa ndi ena mwa mafunso ochepa.

Iwo onse amene akufuna kudziwa mayankho a mafunsowa komanso mafunso ena onse okhudzana ndi Mkumano wa Mulungu akuyenera kutembenukira kwa Iye amene amamanga Mkumanowo.

Iye anapereka mfundo zake pokhudzana ndi Mkumano “m’buku Lake” Baibulo, Mau a Mulungu.

Umenewu ndi “Mkumano/Eklesia wa Mulungu wa moyo” (1 Tim. 3:15), womangidwa ndi Ambuye Yesu Khristu (Mat. 16:18) wa anthu amene “anaitanidwa kuchoka mu mdima ndi kulowa mu kuunika Kwake kodabwitsa” (1 Pet. 2:9).

Unapangidwa ndi iwo amene ali “obadwanso mwa Mau a Mulungu” (1 Pet. 1:23), iwo amene ali “miyala ya moyo” (1 Pet. 2:5), “kuitanidwa kutuluka” pakati pa “Ayuda kapena Ahelene, anthu a malemekezo ndi ulemerero wa dzina lake” (Akol. 3:11; Agal. 3:28; Mach. 15:14)

Ntchito yonse yomanga Mkumano imachitika ndi Mulungu Mwini, kugwiritsa ntchito atumiki amene Iye anawaitana ndi kuwakonzekeretsa (Mach. 26:18).

Malo ena zimaonetsa kuti Mkumano uli ndi maitanidwe akumwamba amene amalekanitsa Mkumanowo ndi magulu ena onse amene umunthu unakhadzikitsa.

Komatu umenewu ndi mutu wina wosiyana.

Umene tikukambawu umangodziwika kuti Mkumano wa Mulungu Wamoyo; ulibenso dzina lina.

Umakhala ndi maumboni ku madera osiyanasiyana, monga chikuonetsera Chipangano Chatsopano (ku Korinto, Galatiya, Kolose, Filipi, ndi kwina kotere), komatu imeneyi si mikumano ya Korinto, Galatiya, kapena Kolose.

Imeneyi si mipingo ya dziko kapena mipingo ya woyera mtima wina aliyense, koma iwo amene akupezeka m’menemu ndi omwe ali oyera mtima kale lonse.

Iwowa kunena zoona ndi gawo la mbali imodzi ya Mkumano wa Mulungu.

Kuonjezera apa, ndi koyenera kuti momwe Mkumano wa Mulungu ukuyendera zikhale moyenera ndi momwe m’Misiri akuganizira.

Aliyense amene amakonza zinthu amadziwa kuti akuyenera kukhala ndi kabuku kofotokozera bwino chokonzedwacho kuti chikagwire bwino ntchito yake.

Pakuyenera kumveka bwino kuti kabuku ka Mkumano kamapezeka m’Buku la m’Misiri, Buku Loyera.

Munjira yaikulu yoposa imene timavomerezera ndondomeko za mukabuku ka wokonza zinthu, tikuyenera kutsatira Mau a Mulungu.

Moyo wathu padziko lino lapansi komanso dziko limene likubwera umadalira pa kumvera kwathu ku Choonadi.

Sitikuloledwa kudzikonzera ndondomeko zathu pamene tikukhala.

Kapenanso kusankha magawo amene tikufuna kutsata kuchokera m’Mau a Mulungu.

Kupezeka kwa Mzimu Woyera padziko lapansi ndiko kukakhala mwa iwo amene amapanga Mkumano ndi kuwatsogolera iwo mwa dongosolo molingana ndi malingaliro Ake Oyera kukachita zimene Mulungu wakonza.

Iye yekha amapereka mphamvu yofunikira ndi anthu a Mulungu.

Chomwecho pofuna kuyankha mafunso okhudza Mkumano wa Mulungu komanso kudziwa kuti mfundo zotsogolera ndi ziti kwa ife okhulupirira mwa Ambuye Yesu Khristu, amene amakonza Mkumano, mosakaika konse timatembenukira ku Mau a Mulungu ndi kukana ulamuliro wina ulionse.

Zochitika zambiri padziko ili la uzimu zikupitilira kudabwitsa iwo ofuna kupeza choonadi.

Mu zaka izi za kumapeto taona kuchuluka pa kukana choonadi chenicheni.

Phunziro lotsogolera ndi ili: ‘choonadi chonse ndi chofanana’.

Komatu Mulungu sanasinthe, umunthu sunasinthe; zenizenizo sizinasinthe komanso choonadi sichinasinthe.

Mafunso okhudza Mkumano wa Mulungu amene amasokoneza umunthu lerolino ndi omwewonso amene amazunguza malingaliro nthawi yakale komanso zaka zotsatira.

Mafunso amenewa akuphatikizirapo udindo wa amai, utsogoleri, mwambo, milandu, malankhulidwe a wina ndi mzake, ukwati ndi kulekana ukwati, banja, kufa ndi kuukanso, kunyema mkate, kupembedza mafano, njira za vumbulutso la Mulungu, ndi zina zotere.

Kalata woyamba wa Paulo mtumwi kwa oyera mtima ku Korinto ikukamba za zimenezi ndi mafunso ena.

Chimenechi ndi chilolezo cha Mkumano wa Mulungu.

Mu kalata imeneyi, mfundo zoyambilira koma zofunika kwambiri zokhudza Mpingo zayalidwa:

Ambuye Yesu Khristu ndi Mutu.

Mzimu Woyera ndi Mtsogoleri.

Mau a Mulungu ndiwo Ulamuliro.

Pali thupi limodzi, Mkumano (gulu la okhulupirira).

Chiyero ndi ntchito ya Mkumano.

Kalatayi ikuvumbulutsira poyera maonekedwe awiri ofunikira a Mkumano mogwirizana ndi “maukulu ndi maulamuliro m’zakumwamba” (Aef. 3:10), komanso dziko lapansi.

Mulungu akuonetsera nzeru zake komanso Mphamvu zake mwa kudabwa kwa onse mu Mkumano wake.

Pakuti Mulungu anaonetsera mu chikondi chake kwa munthu (Yohane 3:16), nzeru ndi mphamvu za umulungu zimenezi, kuti zikamamatilidwe pakuti angelo kumwamba amayang’ana pa Mkumano mu ubale wake ndi Ambuye Yesu.

Umunthu padziko lapansi umangoona mwa chizimezime za chimenechi, ngakhale zimakhala kunja kwa malingaliro awo.

Kuyamikira kwa umunthu pa nzeru ya umulungu ndi mphamvu kumadikira chitetezo cha Mzimu Woyera.


Buku limeneli ndi kuphatikizana kwa malingaliro a Kalata Woyamba kwa Akorinto.

Likuonetsera chikhalidwe cha Mau a Mulungu monga a moyo ndi omangilirika kwamuyaya.

Anali Mau a Mulungu amene anali ofunikira pakati pa okhulupirira mzaka zoyambilira kuti akhale chitsogozo chawo.

Ndi omwewanso amene okhulupilira mzaka zotsatira akuwafuna.

Pasakhalepo kuphatikizira, kuchotsera kapena kuwakonzanso.

Chimenechi ndicho chikhalidwe cha Mau a Mulungu – imene kalatayi ndiyo mbali yake.

Amenewa “aikika kumwamba, kosatha ………….” (Mas. 119:89),

Ambuye wathu alemekezeke komanso owerenga adalitsike ndi buku limeneli.

MBALI YOYAMBA: KUTSUTSANA NDI ZA M’DZIKO

GAWO 1 1:1-9 CHISOMO NDI KUKHULUPIRIKA KWA MULUNGU

1:1, 2 Ulamuliro wa Ndani?

Chifungulo cha kalata woyamba amene Paulo mtumwi analembera kwa oyera mtima a ku Korinto chili pachitseko polowera.

Kalatayi ili ndi chizindikiro cha mtumwi – amene ali ndi ulamuliro wa Mulungu.

Chikhalidwe cha ulamuliro wotere ndiko “kuperekedwa [kwa anthu] kwa Satana” (1 Tim. 1:20).

Tikakumbukira kuti Satana anapeza njira ya kufikira ndi kuzunza Yobu kudzera mu chilolezo cha Mulungu (Yobu 1:6-12; 2:1-7), tili nako kuzindikira ku zimene chitsindikizocho chikutanthauza: ulamuliro wa Mulungu, ulamuliro umenewu ukuyenera kumveredwa popanda kufunsa kwina kulikonse.

Maziko a utumwi wake komanso zotsatira za ulamulirowo ndi chifuniro cha Mulungu.


Sichinali chifuniro cha anthu kapena gulu, kapena kupempha kwa Paulo mwini, kapena ‘bungwe la akuluakulu oyang’anira mpingo’, kapenanso malo a za maphunziro ayi.

Utumwi wake ndi mphatso yochokera kwa Mulungu ndipo kwa Mulungu yekha (Agal. 1:1; 1 Akor. 12:28).

Pamene amalemba kalata imeneyi, Paulo amadziphatika pamodzi ndi Sositene.

Asanatembenuke mtima, Sositene anakwapulidwapo pamaso pa mkulu wa sunagoge, mkulu wa chiweruzo ku Roma (Mach. 18:17).

Mu chipembedzo cha masiku ano, kugwirizana kotere sikungayembekezeke maka pa mtumwi, makamakanso pamene akulemba kalata yofunikira ngati imeneyi.

Koma Paulo akumuona iye monga m’bale, mwana wa Mulungu.

Maimidwe ake, iye ali pafupi ndi mtima wa Mulungu monganso Paulo mwini.

Kuonjezerapo, iye ndi mboni yachiwiri monga mwa zolembedwa m’kalata, mboni yodalirika molingana ndi mfundo za Mau a Mulungu.


Anthu ambiri amavomereza kuti kunali kofunika kuwalembera Akorinto kalatayi nthawi imeneyo, koma amakana kufunikira kwake lerolino.

Amakhulupirira kuti anthu makamaka Akhristu sakuyeneranso kukhudzidwa ndi zomwe zinalembedwa m’kalatayi.

Iwo amanena kuti nkhani zake ndi zokhudza kwambiri chikhalidwe.

Ngakhale kuti kalatayi imakhudzadi nkhani za chikhalidwe cha nthawi imeneyo, Mzimu wa Mulungu amachitira umboni za kufunikira kwake nthawi imeneyo, lerolino komanso mtsogolo, kwa mkumano ku Korinto komanso kwa okhulupirira onse.

Kotero, Iye akulemberanso “kwa onse akuitana padzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, m’malo monse, ndiye wawo ndi wathu” (1:2).

Kusonyeza kuti kalatayo ili ndi phindu lokhalitsa kwa iwo amene ndi oyera mtima a Mulungu, amene amavomereza Yesu Khristu ngati Ambuye.

Kulikonse kumene aliko kaya ndi ndani koma ngati aitanira pa Ambuye Yesu, iwo ali pansi pa ulamuliro Wake kulandira zolembedwa m’kalata imeneyi ndi kuchita mopanda kunfunsa zolembedwa mkalatayi.


1:3-6 Malonje a Chisomo

Mtumwi akupereka malonje kwa oyera mtima kufunitsitsa kuti chisomo chiwafikire kuchokera pa chiyambi chake cha chisomo, “Mulungu wa Chisomo chonse” (1 Petro 5:10).

Iye ndi Atate wathu komanso Wopereka “mphatso iliyonse yabwino” (Yak. 1:17).

Ambuye Yesu ndiye amene amagawa chisomo.

Chisomo chinaonekera kwa anthu onse mwa munthu Khristu, (Tito 2; 2 Akor. 8:9).

Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu amadziwa kuti ife okhulupilira timafuna kukonderedwa kwa umulungu wake, ndipo Iwowa ndi amene angathe kutipatsa ife.

Ndi kudzera mu chisomo cha Mulungu chokha kuti tingathe kukhala ndi mtendere Wake.

Ife tili pansi pa ulamuliro wa umbuye wa Khristu.
Kotero ife timatsatira malamulo Ake.


Mtumwi akutchulapo za kuyamika Mulungu chifukwa cha chisomo chotere.

Pakuyamika Mulungu akutchulapo maka za kulemera kwa mphatso pakati pa oyera mtima – anali nako kuzindikira ndi mphatso.

Zimenezi zinachitika chonchi ndi chisomo cha Mulungu, komanso kupezeka kwa kukonderedwa kwa Mulungu kumeneku kunawatsimikizira iwo monga mboni za Khristu.

Chinthu chachikulu pamenepa ndi lingaliro lakuti kukonderedwa kwa Mulungu kumeneku kumatikonzekeretsa ife za Iye amene akubwerayo, osati pa Katikisima kapena malamulo.

1:7-9 Cholinga cha Chisomo Chimenechi

Kuonjezera apo, kukonzekeretsedwa kwa Umunthu wa Khristu kumatanthauza kuti lingaliro la vumbulutso Lake ku dziko lapansi kumapereka chimwemwe mu mtima, chifukwa Iye akulandira zake zomwe.

Zimenezi zimalimbikitsa kagwiritsidwe ntchito ka mphatso.

Osati ine, koma Khristu’ chimasanduka cholinga cha kutumikira.

Mwa chikondi Khristu amalimbikitsa ndi kugwirizitsa atumiki otere kufikira Iye atawapatsa mphoto pa tsiku Lake.

Mwa kukhulupirika kwa Iye yekha ndi Mwana Wake, Mulungu waitana oyera mtima kwa Mwana Wake mwa chiyanjano, kutipatsa kufanana pa lingaliro ndi mau, komanso kupeza chimwemwe chimene makamaka chili cha Mwana.

Umenewu ndiwo mtenderedi, pakuti tapatsidwa kukondwera naye amene Mulungu akondwera naye: Mwana.

gawo 2 1:10- 3:3 magawano kuvumbulutsidwa poyera

1:10-17 Choyambitsa Magawano - Thupi

Mtumwi, ngakhale kuti anali ndi mphamvu kuchokera kwa Mulungu ya kulamulira (Filemoni 8), anasankha kudandaulira padzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, dzina limene chiyanjano cha okhulupilira onse aitanidwirapo, pamene akulimbana ndi mavuto a magawano.

Pamenepa pakuonekera lingaliro la Khristu mwa mtumwi.


Iye ali “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima” (Mat. 11:29).

Ife amene timadziwa za Umbuye wa Khrisu sitichita chifuniro chathu, pakuti tili pansi pa ulamuliro wake.

Khristu yekha ndiye chida cha mitima yathu.

Kodi ndi chiyani chimene chingaletse magawano kubwera pakati pathu?

Tikuyenera kumugwiritsitsa monga chida cha mitima yathu ndipo tisaonetsere chifuniro chathu.

Za chisoni, kuti sizinali chomwechi pakati pa Akorinto.

Nyengo zimenezi zikufanana ndi nyengo zimene timakumana nazo ife amene timaitanira padzina la Yesu Khristu Ambuye wathu lerolino komanso mnyengo ino!

Kuonjezera apa, Paulo ali ndi umboni weniweni kuti cholinga cha Mulungu sichikuchitika chifukwa kuti pali kugawanikana pakati pawo.

Chimene chimayambitsa magawano onse (mkwiyo ndi kusagwirizana) ndi kudzikuza, “kudzikudza kupikisanitsa” (Miy. 13:10).

Choonadi chomvetsa chisoni ndi chakuti iwo achotsa maso awo pa Khristu ndipo akuyang’anira pa iwo okha, kuiwala kuti zonse zapatsidwa ndi Mulungu.

Khalidwe lotere ndilo chisonyezo cha kudzikuza.

William Kelly anaona chinthu ichi: “Mu chikhalidwe chakugwa cha munthu muli chikondi chosakhwima chimene chimakhala ndi mkwiyo”

Mu nyengo yotere thupi nthawi zonse limatenga ulamuliro ndipo limalimbana kuti litenge malo a pamwamba.

Misonkhano inachitikabe, koma tsopano aliyense anasankha kuchita mwatsopano.

Iwo anagawana mtimagulu magulu.

Ena anasankha Paulo – mlembi wabwino amene anali ndi utumiki wa zolembalemba, ndipo “makalata ake tili nawo komanso nkhani zake tili nazo”.


Ena anasankha Apolo – amene anali ndi mphatso ya kulankhula, wamphamvu pa Malemba, anali ndi utumiki wamphamvu wa kulankhula, ndipo tili nawo “ma tepi ndi makanema ake”.

Komabe ena anasankha Kefa – m’modzi wa ophunzira oyambilira, ndipo “tili nawo maumboni a zochitika zake ndi mabuku ake”.

Enabe anasankha Khristu – Munthu Woukitsidwa, ndipo “tili nacho Choonadi”.

Kunena kuti khalidwe lotereli likupitilirabe lero lino zikuonekera ‘mu mipingo’ yosiyanasiyana ya anthu, imene anthu ake amayang’ana kwambiri mphatso komanso kutchuka kwa munthu.

Kodi chimalakwika ndi chiyani ndi maudindo amenewa?

Tiyeni tiganizire chimene chingachitike ngati aliyense mwa ‘atatuwa’ atabwera ku mkumano wa ku Korinto.

Aliyense akasankha kumvera munthu wa kumtima kwake.

Pakuti abale akangokamba za Khristu, uthenga umenewu ena sakaulandira, mwinanso osaumvera kumene.


Magawano amachitika m’njira zosiyanasiyana: mayang’anidwe a nkhope, masankhidwe a kachitidwe ka zinthu, ndi zina zotere.

Iwo amene akuchokera ku magulu ena amangobwera kudzatsutsa ndi kulimbana.

Iwo amene ali m’gulu lachinayi sangathe ndi kubwera komwe ku misonkhano.

Iwo ali ndi ‘Khristu’ wawo molingana ndi mtsogoleri wawo, ndipo zotsatira zake sangafunenso kumva za Paulo, kapena Apolo kapenanso Kefa.

Chimenechi ndi chisokonezo komanso kusoweka ulemu!

Kodi tikuyenera kuchita kufunsa kuti cholakwika ndi chiyani ndi khalidwe limeneli?

Kunena zoona, pakukhazikitsa utsogoleri wa ku thupi, ndiye kuti iwo akukana utsogoleri wa Mzimu Woyera, komanso udindo wake ngati Mtsogoleri wa mu Mkumano- Iwo onse amamutsitsa Ambuye Yesu kufika pa mlingo wa atumiki Ake.

Ngakhale kuvomereza kwa Petro pa Phiri la Mawalitsidwe sikovomerezeka, pakuti Atate Mulungu anayang’ana kwambiri pa Khristu ndipo pa Khristu yekha (Mat. 17:4, 5).Lero Iye akutsitsidwa kufika pa mlingo wa Muhammad ndi Buddha.

Inde, chilichonse chikulakwika ndi chikhalidwe chimenechi, ndipo Paulo akudzudzula kotheratu khalidweli komanso iwo chifukwa cha kulimbikitsa khalidwe lotereli.

Kwa iwo amene akhoza kupeza mpumulo mkupezeka kwake amaona kuipa kwake kwa khalidweli, iwo amene analankhula kuti “Ine ndine wa Paulo kapena ine ndine wa Khristu” (1:13).

Tsimikizikani za chimenechi.

Zinthu zimenezo zimalimbana ndi thupi mosavuta, zinthu zimene timaziona zikuchitika:ndani amene anabatiza wakuti, ndani amene anatsogolera wakuti kwa Khristu, ndi zina zotere, zingathe kukhala maziko a magawano ngati okhulupilira sangasamale, pamene pali mkhalidwe osafuna kuyang’ana pa Khristu.Katemera othetsera matenda a uzimu amenewa ndiwo kuyang’ana kwa Khristu.

Iye akhale chida cha chikondi komanso kusamalirana kwathu.

Ntchito yake ya pamtanda ndi yomwe ife timalengeza, komanso zotsatira zake m’mitima mwathu ndi zimene Mulungu amafuna kuziona zikuonekera m’miyoyo yathu, osati ntchito zathu kapena zimene thupi lathu limakonda.

1:18-25 Nzeru za Ndani?

Kuchokera mu gawo la m’mbuyomu tikuona momwe thupi limakanira mosavuta kukhazikitsa umodzi ndi kuyambitsa magawano, mipatuko ndi timagulu.

Thupi limakondwera ndi kupembedzedwa.

Tikasiya zimenezi osazikonza, zimachotsa utsogoleri wa umulungu wa Mzimu Woyera ndi kukhazikitsa utsogoleri wa umunthu.

Thupi limasangalala ndi kutsogolera za uzimu.

Pendapenda wotsikira munsi akupitilirabe

Utsogoleri wa umunthu mukaukakamira umachotsa nzeru za umulungu ndi kukweza nzeru za umunthu.

Thupi limalemekeza chidziwitso cha maphunziro

Zotsatira za machitachita osakonzedwa a thupiwa ndiko kuthiridwa pansi kwa uthenga kupangitsa kukhala ‘waphindu’ kufikira nthawi ino.

Mulungu yekha angathe kuthetsa mchitidwe woopsa umenewu.

Ife tikhale osamalitsa kuti tisalimbikitse mchitidwewu, ngakhale ndi pang’ono pomwe, chiyambi cha chikhumbokhumbo cha thupi.

Mulungu waonetsa zimene Iye amaganiza za nzeru ya umunthu pa mtanda wa Ambuye Yesu.

Chilichonse chimene chili cha umunthu, ngakhale chimene chimatengedwa kukhala chabwino ndi chovomerezeka, chimaonetsedwa kukhala chotsutsana ndi Mulungu.

Kunena zoona, umunthu unaonetsera kusaganiza bwino kwake, kupusa kwake, manyazi ake, kufooka kwake, kusowa chiyembekezo kwake komanso udani wake kwa Mulungu pa mtanda wa Ambuye wathu Yesu.


Pamenepo munthu anapeza chigonjetso chathunthu.

Pamenepo Mulungu anayankha kudzionetsera konse kwa munthu.

Pakuti Mulungu anaonetsera Mphamvu Zake, Nzeru Zake, Ulemerero Wake, Chiyero Chake, Kufunikira Kwake komanso Chikondi Chake mwa Umunthu wa Ambuye Yesu.

Pamenepo anagonjetsa mwa ulemerero.

Ife amene tinapulumutsidwa tabweretsedwa maso ndi maso ndi mphamvu komanso chikondi cha Mulungu kudzera mu ulaliki wa mtanda.

Koma iwo amene akutaika amanyozera ulaliki wa mtanda kukhala wopanda phindu.

Mulungu anaonetsera bwino, komanso ife timadziwa za chimenechi: kuti chifooko cha Mulungu ndi cha mphamvu kuposera anthu ndipo zopusa za Mulungu ndi nzeru kwa anthu.

Yoswa anasonyezera zimenezi ku Yeriko (Yoswa, mutu 6);

Gideoni anaphunziranso zimenezi pamene anagonjetsa a Midiani (Oweruza, mutu 7).

Chomwecho mgonjetsi, wophunzira za chidziwitso, kapena munthu wodziwa kulankhula pagulu, aliyense wochita bwino ndipo amalemekezedwa ndi anthu, amatsitsidwa pansi ndi mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Pamene amafunafuna kuwala, kwa zisonyezo, Ayuda anakana Kuwala kwa dziko lapansi ndipo anagwa mu mdima waukulu; pamene amafunafuna chidziwitso, Agiriki anakana Nzeru ya Mulungu, natenga iyo kukhala yopusa.Iwo amene amagwadira ku ulaliki wa mtanda amalandira nzeru ya Mulungu komanso mphamvu ya Mulungu pomwe ophunzira za chidziwitso komanso za uzimu a lero lino amazitenga izi kukhala zopusa.

1:26-29 Chilolezo cha Ndani?

Mulungu amatipatsa ife chitsanzo cha iwo amene analandira chidziwitso Chake.

Pakati pa Akorinto panali iwo amene Mulungu anawaitana ndipo sanavomerezedwe ndi anthu molingana ndi nzeru, chuma komanso mphamvu zawo.

Umunthu umangofuna chitsimikizo cha zinthu zimene zili zosangalatsa pamaso.

Mneneri Samueli anatengeka ndi maonekedwe a umunthu otere kufikira Mulungu atakonza chisankho chake kukhala chodziwika, (1 Sam. 16:6, 7).

Kunena zoona Mulungu anasankha zinthu zimene umunthu unazikana kukhala zopanda pake, kukachititsa manyazi zinthu zosankhidwa ndi umunthu.

Kodi ophunzira sananenedwe kuti ndi “opulukira ndi osaphunzira” (Mach. 4:13)?

Komatu pamene ophunzira za chidziwitso ndi madokotala a za malamulo anawakana iwo kuti ndi mbuli, Mulungu akuwagwiritsa ntchito iwo pa “kutembenuza dziko” (Mach. 17:6).

Kuvomereza kwa Mulungu kuli ndi cholinga chimenechi m’malingaliro: kuti thupi lililonse, mu mphamvu yake, kukonzedwa bwino kwake komanso mchikhalidwe chake, silikuyenera kulemekezedwa pamaso pa Mulungu.

Pakuti “ndi khamu la nkhondo ayi, ndi mphamvu ayi, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu” (Zek. 4:6).

Pakati pa anthu a Mulungu palibe malo kuti thupi lionetsere kunyada.

Ntchito ya Khristu pa mtanda inaonetsetsa za zimenezi.

Tsopano Mkumano Wake uonetsere zomwe m’Misili ali.

1:30, 31 Chikonzero cha Ndani?

Mulungu anapereka kuthekera konse kuti Mkumano Wake uonetsere zomwe Ambuye Yesu ali.

Iye amayankha zokhumba zathu zakale pamodzi ndi Khristu amene ali “kulungama” kwathu, pakuti ife talungamitsidwa ku zinthu zonse ndipo tapulumutsidwa kuchoka ku chilango cha uchimo.

Iye amayankha zokhumba zathu za lero pamodzi ndi Khristu amene ali “kupatulidwa” kwathu, pakuti ife tinapatulidwa kwa Mulungu ndipo kwa Iye tapulumutsidwa kuchoka ku mphamvu ya uchimo.

Iye amayankha zokhumba zathu za mtsogolo pamodzi ndi Khristu amene ali “chiombolo” chathu, pakuti tidzatengedwa kuchoka pamaso pa uchimo.

Khristu, Nzeru ya Mulungu amakwaniritsa zokhumba zonse zimene tinali nazo, tili nazo komanso zimene tidzakhala nazo.

Zoonadi, “Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake, mu ulemelero wa Khristu Yesu” (Afil. 4:19). Dzina lake lidalitsike.

Mulungu anakhadzikitsa munthu Wake ndi nzeru Zake-Khristu

Pamene mitima ya anthu ake ipereka malo oyenera kwa Munthu wa Mulungu, Mulunguyo amalemekezedwa ndipo Khristu amalandira ulemu.

Mkumano wa Mulungu, anthu Ake padziko lapansi, sali pamenepo kuti akakwaniritse chikhumbokhumbo kapena chilakolako cha umunthu.

Mkumano uli pamenepo kuti ukasangalatse Mtima wa Mulungu basi. Uli pamenepo kukaonetsera zimene Mwana wa Mulungu ali.

Mtima Wake umakhutira pamene aliyense mu Mkumano Wake akuonetsera chithunzithunzi cha Mwana Wake.


Kodi kufanana kumeneku kukhoza kuonekera mwa ife?

2:1-5 Kodi Zinavumbulutsidwa Bwanji? Osati mu Njira ya Umunthu

Ataonetsera kuti mu Mkumano Wake mulibe malo a kudzilemekeza, monga mwa luso la umunthu kapena kulekeleredwa, - pakuti zimenezi ndi za kuthupi-, Mulungu akubwerezanso kutionetsera uthenga Wake komanso njira Yake ya kuperekera uthengawo.

Pakuti tadziwa kuti “ndi khamu la nkhondo ayi, ndi mphamvu ayi, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu” (Zek. 4:6), kenako timadziwa kudzera mwa Mzimu Woyera kuti Iye akulankhula uthenga.

Osati uthenga wokha, komatu mbali iliyonse yokhudza Mkumano wa Mulungu imabwera kwa anthu Ake kudzera mu ntchito ya Mzimu Woyera.

Kuonjezera apa, pakuti “thupi lilakalaka kutsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi” (Agal. 5:17), kenako zimene Mzimu amalankhula sizimakhala zokopa ku thupi.

Zimenezi ndi zolangiza kwambiri.

Chomwecho uthenga wake komanso njira yake ya kunenera uthengawo zimakhala zosemphana ndi zimene thupi limaona kuti ndi zosangalatsa.

Thupi limaona kuti nzeru komanso mphamvu ya Mulungu zooneka mu ulaliki wa Mtanda kukhala zopusa.

Kuonjera apo, umboni sumabwera ndi kusalala kwa malankhulidwe monga a Tertulo. (Mach. 24:1-9).

Kapenanso kubwera ndi kutsutsana monga mwa wophunzira za chidziwitso.

Kukhala pansi pa chitsogozo cha Mzimu Woyera, wamthenga akuyenera kufufuza kuti pasakhale kalikonse kotchinga maperekedwe a uthenga kapenanso zotsatira zake za uthengawo.

Uthenga wotani umenewu! Yesu Khristu ndi Iye wokhomedwa!!

Yesu Khristu –Mnazarene wodzichepetsa; amene anafotokozedwa mwa chipongwe ngati mwana wa mpalamatabwa;

amene Afalisi anamufotokozera ngati Msamaliya, wokhala nacho chiwanda komanso wozungulira mutu;

amene a ku Magadala, sanathe kuima ndi chozizwa chofunikira, ndipo anamufunsa kuti achoke pa gombe lawo;

amene a ku Nazarene anafuna kumukankha kuchoka pamwamba pa phiri.

Chiweruzo cha Yesaya chinatsutsana nalo fuko: “Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zawo” (Yes. 53:3).

Inde, dziko lonse lapansi linapezeka lolakwa pa kumukana Iye, pakuti “Anali m’dziko lapansi ndi dziko linalengedwa ndi Iye, koma dziko silinamzindikira Iye.Iye anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamlandira Iye” (Yoh. 1:10, 11).Komatu Iye ndi Munthu wodzodzedwa komanso “wochokera kwa Mulungu” (Mach. 2:22), ndipo chimenechi chimasiyanitsa zina zonse.

Ndi Iye wopachikidwa –anapezeka wosalakwa, komabe anaweruzidwa ku imfa;

mwa Iye mulibe uchimo, komabe moyo Wake unaperekedwa nsembe ya uchimo;

Wokondedwa wa Atate, komabe “wokwapulidwa, wotunduzidwa wa Mulungu ndi wozunzidwa”;

anakhalabe ndi Atate, komabe anasiyidwa ndi Mulungu;

kuwala kwa dziko lapansi, komabe anakutidwa ndi mdima.

Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m’malo mwa osalungama kuti akatifikitse kwa Mulungu” (1 Petro 3:18), amene “anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu naukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama” (Aroma 4:25).

Pakuvomereza, chinsinsi cha umulungu ndi chachikulu” –chachikulu kuposa malingaliro komanso mamvetsetsedwe a umunthu-

Mulungu anaonekera m’thupi, anayesedwa wolungama mu mzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m’dziko lapansi, wolandiridwa m’ulemerero” (1 Tim. 3:16).

Uthenga woterewu –ndipo Khristu ndiye uthengawu- wochokera ku ulemerero ndi kufikira mu ulemerero ukuyenera kukhala ndi zotsatira zabwino kwa mtumiki komanso womvera.

Ndipo umachitadi izi.

Umaika moyo wa mtumiki pa ntchito!

Iye amene amabweretsa uthenga wotere sayerekeza kudalira pa iye mwini –amatsitsidwa kufika pa mlingo wofooka ndi wosoweka, kunjenjemera kwakukulu.

Iye samakhala komanso sangakhale chitsanzo cha munthu wodzitsimikizira payekha komanso woganiza kuti dziko lino likufunika anthu odziwa kulankhula ndi wophunzira za chidziwitso.

Mose ndi Gideoni zinali zitsanzo zofanana za zotengera zosweka za dothi “ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife” (2 Akor. 4:7).

Zoonadi palibe thupi limene lidzalemekezedwa mu zimenezi.

Chimenechi ndicho chisonyezo cha Mzimu ndi mphamvu Yake kuti onse akhale a Mulungu ndipo popanda kalikonse ka munthu.

Monga zadziwitsidwa pachiyambi paja, zotsatira za uthenga wotere kwa omvera umakhalanso wa phindu.

Okhawo amene Mzimu wa Mulungu unagwira ntchito angathe kulandira uthenga woterewu.

Thupi lilibe gawo pamenepa.

Okhawo amene ndi odulidwa, (kotero kuti analandira mphatso ya chikhulupiriro kuchokera kwa Mulungu) –m’mawu a Ambuye Yesu Mwini “kutengedwa ndi Atate” kulandira nzeru kuchokera kwa Mulungu.

Ndi ntchito ya Mulungu monga mutu kubweretsa anthu ku mlingo umenewu.

Kuonjezera apa nzeru ya Mulungu ndi yamuyaya komanso yosasintha monga momwe Mulungu ali.

Nzeru ya m’badwo umenewu yamangika pa chidziwitso ndi zikhulupiriro, zambiri mwa izo sizingatsimikizidwe, ndipo zambirinso zingathe kupezeka kuti ndi zolakwika.


Pa kumukhomera Ambuye wa ulemerero zaonetsera poyera kuti atsogoleri a mnyengo imeneyo anali mbuli pa nzeru ya Mulungu.


Ndiponso kupitilira kukana Uthenga kukusonyeza kuti iwo pamodzi ndi mbeu yawo adakali mbuli.

2:9-14 Anavumbulutsidwa Bwanji? Cholinga Chachikulu cha Mulungu

Kuonjezera apa, choonadi cha Mulungu sichimapezeka wamba kwa munthu.

Diso lingathe kuzindikira, khutu lingathe kumva kapenanso mtima ungathe kulandira.

Pamene zimenezi zili zopambana mkati mwa chidziwitso cha munthu komanso kupambana kwake, komabe ndi zopanda pake mu zinthu za umulungu.

Mobwerezabwereza zanenedwa momveka bwino kuti zonse za Mulungu zili kunja kwa kumvetsetsa kwa munthu chifukwa cha nyengo yake ya kugwa.

Zikuyenera kubweretsedwa kwa munthu mu njira ina, mu njira imene ili ya Mulungu.

Kupatula Iye amene amadziwa, -Mzimu Woyera- amaphunzitsa, munthu samamvetsetsa.

Pokhapokha mukhale chilengedwe chatsopano mwa munthu cha kulandira chiphunzitso, munthu adzakhalabe mu mdima pa nkhani ya zinthu za Mulungu.

Zikuyenera kuvomerezedwa ngati umboni kuti mzimu wa munthu umadziwa zinthu, malingaliro komanso maganizo a munthuyo.

Chomwechonso Mzimu wa Mulungu umadziwa zinthu za Mulungu.

Tsopano, “Mzimu Woyera wa Mulungu anapatsidwa kwa ife” kwa iwo amene analungamitsidwa (Aroma 5:5), cholinga kuti tikadziwe zinthu za Mulungu zimene zaperekedwa kwa ife kwaulere.


Kuphunzitsidwa ndi Mzimu Wake komanso kupatsidwa ndi chidziwitso Chake, anthu Ake amatsogozedwa kulankhula zinthu za uzimu munjiranso ya uzimu, kutsegula dziko lathunthu losintha kwa munthu wa uzimu.

Anthu oterewa samadalira pa maonedwe a umunthu kapena kuthekera kwa umunthu, kapenanso kukaikira.

Mbali inayi, munthu wamba, amene amaganiza kuti nzeru ya Mulungu ndi yopusa, sangathe kulandira zinthu za Mzimu, pa chifukwa chakuti iye alibe Mzimu wa Mulungu (Aroma 8:9).

Zinthu za uzimu ndi zopusa kwa iye.

Kuti alandire zinthu za Mzimu akuyenera kubadwa mwa Mzimu.

Pali kusiyana kwakukulu pakati pa wokhulupirira ndi wosakhulupirira, pakati pa munthu wa uzimu ndi munthu wamba.

Munthu wa uzimu amatengedwa kukhala wopusa ndi anthu a nzeru a dziko lapansi ndipo munthu wamba amakhala wanzeru m’dziko lino ndipo amatenga choonadi cha Mulungu kukhala chopusa.

Kotero munthu wa uzimu angathe kukhala ndi chidziwitso pa zinthu zonse pakuti iye ali ndi Mzimu wa Mulungu.

Posatengera kuti akunyozedwa kapena akusekedwa, iye amakhalitsa chete umbuli wa anthu opusa, chimene chimachotsedwa ndi umunthu mu nzeru zake kuchokera m’malingaliro ndi njira komanso chidziwitso cha Mulungu (Yes. 55:8, 9).


Iwo okhawo padziko lapansi, amene ali ndi malingaliro a Khristu; monga; maganizo ndi mau a Khristu, ndi okhawo amene amapanga Mkumano Wake.

3:1-3 Thupi pa Ntchito –chiyambi cha Magawano

Titatha kukhadzikitsa kuti pali kusiyana komanso kugawikana kosakonzeka pakati pa chipembedzo ndi nzeru za anthu mbali inayi, ndipo mbali inayi choonadi chikupezeka mu Mkumano Wake, Mulungu akutembenukira ku mkumano wa ku Korinto ndipo akupima zofunika kuchita zopezeka kumeneko.

Mungathe kuona kuti kameneka ndi kachinayi mau akuti “abale” agwiritsidwe ntchito.

Monga taona kale (pa mutu 1:10, 26; 2:1) akuwabweretsa pamodzi oyera mtima kukaona zinthu zina pakati pawo, pamene akutsindika za ubale umene iwo akupezekamo.

Mau amenewa ndi a banja.

Pakuona mavuto a mkati amenewa, Mzimu Woyera akutsogolera mtumwi Paulo, amene pakati pa Akorinto anakhala “mofooka ndi m’mantha, ndi monthunthumira” (2:3), kulankhula mosanyengerera zokhudza zimene zikuwavuta iwo, -magawano ndi mikangano.


Pakuti, zimenezi ndi zotsatira zazikulu za nthenda ya uzimu, machitachita a thupi.

Pamenepa munthu ali pa ntchito yake ndiponso molingana ndi mfundo zimene iye akudziwa.

Komabe Mzimu akufotokozera ntchito zimenezi kukhala za thupi osati za uzimu.

M’mbuyomu kunalipo kusiyana kumene kunachitika ndipo cholinga chachikulu cha Mulungu chinaonetsedwa pakati pa uzimu (kubadwanso kwatsopano) ndi kuthupi (kusakonzedwa);

Iwo oitanidwa ndi Mulungu komanso iwo amene ali a dziko lapansi.

Mu kusiyana kumeneku mauwo akufotokozera za nyengo ya munthu pa kubadwa.

Tsopano pali kusiyananso kwina kumene kwachitika, nthawi imeneyi pakati pa oitanidwa.

Kusiyana kumeneku kukuchitika pakati pa iwo amene akupezeka mu Mkumano.

Kusiyana kumeneku kukuchitika pakati pa iwo amene ali oitanidwa “abale”, amene ali mu ubale wa banja.

Auzimu akusiyanitsidwa ndi a thupi

Pamenepa akutanthauza mu khalidwe lawo.

Iwo amene ali a thupi aikidwa monga makanda mwa Khristu, amene akufunika mkaka.

Mfundo yofunika kuidziwa ndi yakuti kaduka ndi mikangano zopezeka monga mwa chisonyezo cha umwana (1 Pet. 2:1 mpaka mtsogolo), pamenepa zikuoneka ngati zotsatira za kuthupi.

Choyambilira, ana amafunika mkaka.

Amafunika zinthu zoyambilira, manna, ndi zina zotere cholinga kuti Khristu wodzichepetsa akakonzedwe mwa iwo, kuti akaonetse malingaliro a Khristu.

Kusowekera zimenezi ndicho chisonyezo cha kukanika kukula, kuonetsedwa kwa umunthu.

Ukhanda umafanizidwa pa mfundo yakuti iwo akutenga nawo gawo mu chikhalidwe cha uchimo.

Limeneli ndi vuto la mkaka wa Mau limene likufotokozedwa.

Kupyola pamenepa komanso chimene chili chomvetsa chisoni kwambiri, mu kaduka wawo, magawano ndi mikangano akuonetsera kuti ndi za kuthupi –zodzala ndi chikhalidwe cha uchimo.

Machitidwe awo ali ngati munthu wamba amene ali ndi chikhalidwe cha uchimo.

Kotero amawerengera kwambiri pa zinthu za munthu.

Nyengo yomvetsa chisoni kukhalamo!

Zimenezi ndi zosalemekeza Ambuye!

Zimenezi ndi zolangiza kwa anthu a Mulungu lerolino!

Pamene pali kaduka, pamene pali kusagwirizana, pamakhala chisonyezo chotere cha kuthupi.

Pamene pali makangano, pamene pali magawano, pamene pali kukaikirana, pamene pali kusiyana pakati pa oyera mtima, pamenepo pali umunthu ndipo pali umboni wakuti chikhalidwe cha uchimo chatengapo gawo lalikulu.

Zonse zimakhala zobalalika, thupi limalamulira ndipo Mzimu wa Mulungu amadzimitsidwa komanso amamva chisoni.

Pakuti mbali ina umunthu umachepetsedwa kapenanso mbali inayi wotumikira amalemekezedwa.

Komatu umunthu umakana uthenga.

Zomvetsa chisoni pamene anthu a Mulungu akugwa mu chikhalidwe chimene Mulungu anawapulumutsamo modabwitsa.

Zimakhala zofunikira kuika zinthu mu ndondomeko yoyenera.

Paulo ndi Apolo ndi anyamata otumikira chabe, atumiki otumidwa ndi Mulungu kutenga uthenga wa Mulungu kwa anthu a Mulungu.

Iwo ndi ogwirizana mu cholinga ndi mkuthekera mu utumiki wawo pansi pa Mulungu.

Ntchito ndi yopatsidwa ndi Mulungu komanso yotsogozedwa ndi Mulungu, ndipo kuchulukitsa kumachokera kwa Mulungu.

Atumiki amenewa siofuna chuma ayi, kutsogoza zofuna zawo, kapenanso ambuye ofuna kukhazikitsa ma ufumu awo.

Wina amamangilirana ndi mzake; ntchito ya Paulo ya kudzala inali yoyamba ndipo ntchito ya Apollo ya kuthirira inatsatira.

Akugwira ntchito pamodzi m’munda mwa Mulungu, Mkumano Wake, umene wa ku Korinto unali gawo lake chabe.

Oyera mtima akuyenera kulemekeza atumiki a Mulungu, koma asawatenge ngati milungu (1 Ates. 5:12, 13).

Chimenechi ndi chikumbutso chathunthu nthawi iliyonse kwa oyera mtima!

GAWO 3 3:4-4:21 ATUMIKI A MULUNGU

3:4-19 Antchito ndi Zotsatira za Ntchito Yawo

Chisomo cha Mulungu chokha chimathandizira aliyense kugwira ntchito mu nyumba Yake.

Sichimatengera kuti tikuchita bwino.

Chomwecho aliyense awonetsetse kuti ntchito yake ikutengera pa chisomo cha Mulungu.

Maziko okhawo anakhazikitsidwa kale kudzera mu chisomo.

Palibe maziko ena koma Yesu Khristu, amene dziko lino linamunyadzitsa ndi kumukana.

Iye ndi maziko a Mulungu.

Agalatiya analandira chenjezo lokhwima pokhudza zimenezi, (Agal. 1:8, 9).

Chomwecho okhulupilira aliyense akuyenera kusamalitsa udindo umenewu.

Tsiku likubwera pamene Ambuye adzayesa ntchito ya munthu wina aliyense.

Zidzayetsedwa ndi “lawi la moto” (Chiv. 1:14), ntchito imene ili ya golide, siliva kapena mwala wa mtengo wapatali idzakhalabe chifukwa ikuonetsa khalidwe la maziko.

Imeneyi ndi ya phindu la uzimu ndipo idzalandira mphoto yake.

Ntchito yonse ya mitengo, udzu ndi mapesi ndi yosakhalitsa ndipo singalimbe pa muyeso wa moto.

Umunthu umaonetsera zimenezi; sumalemekeza Khristu.

Chifukwa umalemekeza munthu pokhala wa umunthu mu mtengo wache, limalephera kupeza mphoto.

Kunena kuti pali mphoto ndi zachidziwikire chifukwa munthuyo ndi wopulumutsidwa.


Iye ndi mwana wa Mulungu.

Koma amataya mphoto yake.

Chidziwitso ndi chamtengo wapatali, pakuti Mulungu sangakhale ndi munthu amene ali mbuli (mutu 6: 2, 3, 9, 15, 16 ndi 19).

Mzimu wa Mulungu wabwera kudzatiphunzitsa zinthu zonse komanso kudzakhala pa mkumano, kupangitsa malowo kusanduka pokhalapo Mulungu.

Chiyero chimasanduka Nyumba ya Mulungu (Mas. 93:5; 1 Pet. 4:17).

Kotero aliyense amene amayesa kudzitchula yekha mtumiki wa Mulungu amalandiridwa ngati mtumiki wa Mulungu.

Chitsimikizo cha kutumikira kwake ndi tsiku la kuyesedwa.

Munthu wamba, wosakhulupilira, amene amatenga udindo umenewu amakhalabe munthu wosowa pakuti samanamiza munthu wina aliyense koma amadzinamiza yekha.


Chifukwa amaononga Kachisi wa Mulungu ndi chipembedzo wamba, iye amakumana ndi chionongeko cha iye mwini.


Mitundu itatu ya a ntchito –auzimu, athupi ndi achilengedwe- kotero amalandira malipiro awo.

3:20-22 Mulungu –Chida cha Utumiki onse

Alipo mlonda m’modzi wotsutsana ndi kudzinyenga tokha.

Kugwada pa mapazi a Ambuye Yesu kuoneka ngati wopusa pamaso pa dzikoli, kukana nzeru ya dzikoli ndi kulandira nzeru ya Mulungu ndiye mlonda wotsutsana ndi kudzinyenga tokha.

China chilichonse kupatula nzeru ya Mulungu ndiko kudzinyenga komanso kusoweka, kulandiliratu chiweruzo cha Mulungu.

Kudzilemekeza tokha –ndiwo muzu wa nzeru ya dziko lapansi- zili chabe pamaso pa Mulungu ndipo sizingatitengere ife kwina kulikonse.

Zimene Mulungu wavomereza, zimene Mulungu wapereka ndi zogwiritsira ife ntchito komanso kupindulira uzimu wathu.

Komatu ulemerero ndi wa Khristu komanso Mulungu.

Kukhulupirika kwa Atumiki

4:1-7 Mtumiki wa Ndani?

Okhawo amene anakana nzeru ya dziko lapansi angathe kukhala otumikiradi Khristu.

Mtumiki wa Khristu amaonetsera maonekedwe a Khristu kotero kuti, mbali zonse za machitidwe ake chiweruzo chimakhala chimodzimodzi:

Kufanana ndi Khristu (Mat. 10:25).

Kumeneku ndiko kuchita mokhulupirika.

Monga kapitawo, iye amasamalira zinsinsi za Mulungu, zinsinsi zobisika mwa Mulungu asanakhazikitsidwe maziko a dziko lapansi kuvumbulutsidwa tsopano kwa atumwi ndi aneneri Ake oyera, kuti zigawidwe kwa oyera mtima Ake onse.


Chimene chili chofunikira ndi chakuti anthu onse aone kufanana ndi Khristu komanso kukhulupirika ngati chisonyezo cha Paulo, Apolo komanso atumiki ena a Khristu.

Kwa Paulo zinalibe ntchito ngati oyera mtima a ku Korinto amamuweruza, chifukwa monga umo zanenedwa kale, kuweruza kwa Mulungu ndi kumene kuli kofunikira osati kuweruza kwa munthu.

Ngakhale kudziweruza yekha kwa mtumiki sikumawerengedwa.

Kulira kodandaula kwa Eliya “popeza sindili wokoma woposa makolo anga” (1 Mafumu 19:4), kungathe kukhala koona koma Yehova sanayankhe kuliraku.

Ambuye ndi Woweruza Weniweni yekhayo, osati zimene znthu ena akuganiza, kapenanso zimene ndikuganiza, koma zimene Ambuye akunena.

Kuweruza mtumiki si udindo wathu.

Pamene Ambuye adzabwera, Iye adzaweruza zinthu zonse molungama: zolinga, machitidwe, zinsinsi komanso za poyera- Kenako Mulungu woyera wolungama adzalemekeza wina aliyense.

Mfundo zimenezi, Mulungu amaweruza osati munthu wina aliyense, zikukhudza Paulo (mtumwi) ndi Apolo, komanso mtumiki wina aliyense, cholinga kuti wokhulupilira aliyense akaphunzire kuti asakhazikitse milungu, (utsogoleri mu mpingo), kapenanso magawano ndi magulu a padera (mipatuko).

Zokoma komanso zofunikira motani kwa mtumiki komanso gulu kuti sizofunika kuchita mwa mphamvu zathu, kapena kuthekera kwathu, koma chisomo cha Mulungu chimene chimatitsogolera ife ku utumiki Wake.

Mulungu amene anaitana Bezaleli ndi Aholiabu, anawadzadza iwo ndi nzeru komanso luso kuchita ntchito Yake molingana ndi chikonzero Chake komanso mu ulemelero Wake, (Eks. 31:1-6).

Iye anapereka mwa chisomo zonse zimene iwo amazifuna: maitanidwe, nzeru ndi luso.

Funso limeneli limatisautsa: kodi munthu angathe bwanji kuganiza kuti iye ndi wopambana kuposa wina aliyense, atatha kulandira zonse kuchokera kwa Mulungu zofunika kugwilira ntchito?

4:8-13 Kunyozetsa Mtumiki wa Mulungu

Atatha kunyazitsa choonadi chofunikira chimenechi, Akorinto ananyoza atumiki a Mulungu, kusonyeza kubanika kwawo konse kumene anali nako.

Tsopano pamene Ambuye adzabwera, Iye adzapereka mphoto kwa atumiki Ake.

Moyo wa Chikhristu siumatengera pa za lero.

Komabe, Akorinto akuona ubwino umene anali nawo kukhala zinthu zowayenera iwo, ndipo amazitukumula ngati mafumu monga mwa maonekedwe a kuthupi.

Kuonjezera apa, maonedwe a Akorinto pa Paulo anali osakondweretsa.

Atumwi, pakukumana ndi imfa tsiku ndi tsiku, anali chionetsero ku dziko lapansi, kwa angelo komanso kwa anthu.

Iwo anali chilichonse chimene Akorinto anawatchula mosawaonetsera chisoni: opusa amene ali ofooka, osowa, onyozeka, okanidwa, ozunzidwa komanso ochititsidwa manyazi –koma mu kena kalikonse anali monga Mbuye wao (Mat. 10:25).

Okhulupilira anzawo a ku Korinto anawanyoza atumwi monga dziko lapansi limawanyozera iwo, ndipo Ambuye wao amanyozeka.

Machitidwe otere amene akuchulukira padziko lapansi sakudabwitsa konse, koma kodi tingayembekezere kuti akhoza kuchokera kwa oyera mtima?

Kodi okhulupilira amene amakhala ndi machitidwe otere sakuonetsera mzimu wa chikale?

Kuyesedwa woipitsitsa pa zinthu zonse, kukanidwa ndi anthu ochuluka amene ali osaganiza ndi chinthu chochititsadi manyazi, komatu pamene iwo omdziwa Khristu ndipo ali ndi maganizo ofanana a Khristu, achita khalidwe lotere zimakha “zoipitsitsa kwambiri kuposa zonse”.

Kodi ndi kangati monga dziko lapansi oitanidwa adzionetsera okha kukhaladi oitanidwa?

4:14-21 Mau a Mulungu Kutsogolera

Chikhalidwe chimenechi chinapangitsa mtumwi kupereka chenjezo lokhwima, chenjezo limene tate akhoza kusungira mwana wake wopulukira: mutsate chitsanzo changa.

Iye ndi amene anabweretsa Mau kwa iwo, ndipo kulankhula monenetsa, iye ndi amene anawabereka.

Mu kufatsa ngati kwa Khristu, anatuma Timoteo amene anasamalitsa ndi “mtima woona za oyera mtima” (Afil. 2:20), kuwakumbutsa za ndondomeko ndi machitidwe odziwikiratu kuti achitidwe mu mkumano wina ulionse.

Kaya maonedwe awo pa mtumwi ndi otani, iwo akuyenera kuzindikira chinthu chimodzi:

Mu ufumu wa Mulungu muli mphamvu ya kulimbana ndi chikhalidwe cha umwana cha mphulupulu.

Ngati chikhalidwe chimenechi sichitsogozedwa ndi lamulo, ndiye kuti chikuyenera kutsogozedwa ndi ntchito; ngati kulibe yankho ku pempholi, ndiye kuti chikwapu chikuyenera kulankhula.

Kodi ndi kangati kamene mtumwi akuonetsa kuti akumvera Ambuye wake, pakuti iye adzabwera pokhapokha Ambuye atamulola kubwera.

Kodi pakali pano akuyenera kuchoka ku chikhalidwe chodzikweza cha umunthu?

Chimodzimodzi lerolino kuli kukana mbali yaikulu ya chiphunzitso cha mtumwi.

Kodi tingathe kuchoka ku machitidwe oterewa?

MBALI YACHIWIRI: KUTSUTSANA NDI THUPI

GAWO 4 5:1-9:27 KUKHALA M’CHIYERO

5:1-5 Chilakolako: Chigololo Chidzudzulidwa

Mzimu Woyera akupitilira kupima chikhalidwe cha mkati, komanso chimene chili chosapereka ulemu kwa Ambuye cholekeleredwa pakati pa okhulupilira.

Ngakhale machitidwe a mzika anali onyozetsa ndi ochititsa manyazi, nkhani iyi ya tchimo la munthu payekha linabweretsa tanthauzo lokaikitsa pa kusiyana kwa Mkumano wa Mulungu.

Kuonjezera apa, kulekelera kwawo pa kupezeka kwa mdani komanso kusiyana kwawo mu ntchito zinali zizindikiro za momwe samakhuzikira ku chiyero cha Mulungu.

Iwo anali odzadza ndi kudziona okha kukhala ofunika!

Kusoweka kwa chikhalidwe ndi uzimu zinaonekera pamene iwo sanazililire okha pa nyengo imene iwo anali, iwo anakhutitsidwa ndi mphatso zawo komanso atsogoleri amene iwo anadzisankhira okha.

Kodi iwo sanadziwe zoyenera kuchita?

Sizingakhale zolondola kwenikweni kunena kuti analibe malangizo ovumbulutsidwa.

Pa mutu umenewu chifanizo chikuperekedwa mu kalata yoyamba ya mtumwi Paulo m’mene anawalangiza iwo “kusayanjana ndi achigololo” (ndime 9).

Kodi iwo anali ataiwala kalata imeneyo kapenanso kunyalanyaza zolembedwazo?

Chimene chili chodziwikiratu ndi chakuti Mzimu Woyera anali atachotsedwa pakati pawo ndi machitidwe komanso makhalidwe awo athupi.

Iwotu ananyozera kapena sanadziwe za njira imene inali yopezekeratu kwa iwo.

Zitsanzo ziwiri kuchokera mu Chipangano Chakale zingathe kukwanira kufotokozera zimenezi.

Pamene Mose amene analibe kupezeka kokhalitsa kwa Mzimu Woyera anapanga chisankho chokhudza munthu amene sanasunge Sabata, anamtsekera iye m’ndende ndipo anafunsa Yehova zoyenera kuchita, (Numeri 15:34).

Pa zochitika zina zosiyana, Yehova anamlonjeza Solomoni kulowererapo kwa umulungu pamene anthu a Mulungu amadzichepetsa okha nafunafuna nkhope Yake, (2 Mbiri 7:14).

Zitsanzo zonse zikuonetsa kufunika kwa kudzichepetsa ndi kudalira, makhalidwe amene sakuonekera mwa akhristu othodwa a ku Korinto.

Mzimu Woyera pamene wapatsidwa malo ake woyenerera amaonetsera zimene zalakwika komanso momwe mungakonzere zolakwikazo.

Mau a uneneri amachokerabe kwa Iye.

Ngakhale iye kunalibeko mtumwi analamula zoyenera kuchitika.

Zimenezi ndi zolangiza kwambiri.

Zoyenera kuchita zinayenera kuchitika pamene okhulupilira asonkhana pamodzi.

Nkhaniyi inali yodziwika kwa anthu onse.

Chomwecho, okhulupilira mu mkumano anayenera kuthana nayo.

Sinali nkhani yakuti abale ochepa akumane pamodzi ndi kupempherera.

Motsutsana, “asachinene ku Gati” (2 Samuel 1:20), kapenanso m’misika ya dziko lapansi, limeneli ndilo chenjezo lofunikira.

Kodi chiweruzo cha chikhalidwe chimenechi chinagwiritsidwa ntchito ndi ulamuliro wanji?

Kodi chikuyenera kugwiritsidwa ntchito chifukwa chiyani?

Kodi chiweruzo chinali chotani?


Choyambilira, chinali mudzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, oyera mtima kukhala mu mkumano, ndi mzimu wa mtumwi komanso mphamvu ya Ambuye Yesu Khristu.

Mtumwi anabweretsa poyera chikhalidwechi ku chikumbumtima cha oyera mtima; anabwera pamodzi nazindikira dzina loyera ndi lodalitsika la Ambuye wathu Yesu –limene sililola chidetso- ndipo anagwada ku mphamvu Yake-imene simalola maudani.

Cholinga cha chiweruzo ndi chakuti mzimu akasungidwe mu tsiku la Ambuye wathu Yesu.

Chigamulo choterechi chinali kubwenzeretsedwa kwa munthu wopatsidwa mwambo.

Zonsezi zikuyenda mozungulira ulemu wa Ambuye wathu Yesu.

Kubuma kumene anayenera kuchita mosakaika konse kunaonjezera ulemu kwa Ambuye wathu.

Tsopano anali ndi langizo la kutaya ‘munthu wochimwa’ ameneyu monga mwa mwambo wa mu mkumano.

Kodi ndi ndani amene amapereka munthu kwa Satana?

Mtumwi akunena kuti iye anaweruza kale munthu wotere kwa Satana kuti akaonongedwe ku thupi. 1

Zimenezi zili mu mphamvu ya mtumwi komanso mophatikizira ndi machitachita amene akuyembekezedwa mu mkumano.

Thupi ladzifotokozera lokha kumene likuyenera kukakhala malo a imfa.

Machitachita ake anali obweretsa munthu ku kulapa ndi kubwerera kwa Mulungu komanso ku chiyanjano.

Chimenechi ndiye cholinga cha mwambo wa mu Mkumano.

5:6-13 Machitidwe a MkumanoZomvetsa chisoni kuona iwo akuganizira za iwo okha! Zimenezi sizabwino, si za Mulungu.

Zimaonetsera umbuli onse wa chikhalidwe cha uchimo, umene ukaloledwa, umakhala ngati chotupitsa mkate.

Chotupitsa chochepa chimafufumitsa mtanda onse.

Dontho la chodetsa limaononga ndowa yonse ya madzi abwino.

Okhulupilira sigulu chabe la anthu obwera pamodzi kukakhala motayilira mu bungwe lotchedwa Mkumano.

Okhulupilira ndi thupi lamoyo, ndi thupi limene chiwalo chimodzi chikavutika, chimasokoneza magwiridwe ntchito komanso thanzi la thupi lonse.

Machitidwe a mkumano akuchotsa chotupitsa chakale, kutumphuka kwa chikhalidwe chakale cha moyo wakale, monga moto umaletsa machitachita a chotupitsa, cholinga kuti akaonetsere chimenedi ali –opanda chotupitsa.

Iwo amene amadya Pasaka amalamulidwa kusunga phwando la mkate wopanda chotupitsa pambuyo pake.

Chimodzimodzinso, tazindikira kuti Khristu amene ali Pasaka wathu anaperekedwa nsembe kwa ife.

Chomwecho, ponena kuti tadya nawo Pasaka ameneyu, timasunga phwando la mkate wopanda chotupitsa -moyo wachiyero, pamaso pa Ambuye amene ali woyera, (1 Pet. 1:15, 16).

Miyoyo yathu ikhale ndi chisonyezo chenicheni ndi choona mtima, choonekera kwa onse, kukhala mwa chikhulupiliro cha Mwana wa Mulungu.

Kaduka ndi kuipa mtima ndi zitsanzo za chotupitsa m’malingaliro mwathu ndi m’machitidwe athu zimene zilibe malo pakati pa anthu a Mulungu.

Kalata yoyamba inafotokoza zowachenjeza iwo kusakhala pamodzi ndi anthu oipa.

Zikuonetsa kuti iwo sanamvetsetse izi, nchifukwa chake sanachitepo kanthu kufikira nyengo imeneyi.Tsopano zafotokozedwa bwino lomwe kotero kuti akuuzidwa kuti asayanjane ndi iwo amene ali ochimwa.

Mu chimenechi sangasokonezedwe.

Kunena zoona, kuti iwo asayanjane ndi onse amene ali achigololo a dziko lapansi, iwo anayenera kuchotsedwa padziko lapansili.

Pakuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo” (1 Yoh. 5:19), ndipo ana ake akusangalala.

Kumenekutu sikulimbikitsa kudzisankha.

Maitanidwe a kupatulidwa amenewa akukhudza iwo okhawo amene akunyema mkate.

Ngati “aliyense amene atchulidwa m’bale……….” ndi amene tinyema naye mkate pamodzi.

Iye amene sakuyenera kuyanjana naye ngati iye adziwika kuti ndi wachigololo, ndi zina zotere.Kapena tikuyenera kutero.

Komatu Mulungu akutiyitana kukadzudzula “ntchito za mumdima zosabala kanthu” (Aef. 5:11).

Palibe chimene Mkumano ukuyenera kuchita pokhudza iwo amene sasonkhana nawo pamodzi.

Mulungu ndiye Oweruza wa onse.

Iye asamalira zosoweka za oterewa.

Koma iwo amene ali mkatimkati, amabwera pansi pa chitetezo cha Mkumano ndipo Mkumano ukufunsidwa kukagwira ntchito yosungitsa mwambo mu mkumano mokhudzana ndi amenewa.

Zimenezi sikuti ndi zosafunika masiku ano omaliza.

Mchitidwe woterewu umaonetseranso poyera kusiyana kwa pakati pa Mkumano wa Mulungu ndi chipembedzo cha dziko lapansi.

6:1-8 Milandu Iletsedwa

Mzimu Woyera akuonetseranso poyera umboni wina wa umunthu pakati pa okhulupilira ku Korinto.

Iye akuwadzudzula iwo pa kulimba mtima kwawo posumilana milandu wina ndi mzake.

Mchitidwe umenewu wosumila m’bale wawo umapeputsa kusiyana kumene Mulungu anaika pakati pa osalungama ndi oyera mtima.

Umaononga kusiyana kwakukulu pakati pa nzeru ya munthu ndi nzeru ya Mulungu, pakati pa munthu wa kuthupi ndi munthu wa uzimu ndipo zimaonetsera poyera kuti okhulupilira ali pansi pa chikhalidwe cha uchimo.

Iwo amalephera kuvomereza kuti Mkumano si bungwe lapadera la dziko lapansi.

Kuonjezera apa ndi kofunika kuona kuti funsoli limene lafunsidwa pa mutu wa m’mbuyomu: “kodi amene ali mkatimo simuwaweruza ndinu?” (5:12).

Funso limeneli likukhudzana ndi nkhani zimene zinalipo pakati pa okhulupilira zimene sizimayenera kubwera pamaso pa osakhulupilira.


Usachinene ku Gati” (2 Sam. 1:20) kunalinso kukumbutsa kwa malingaliro a Mulungu.

Monga kunali kofunika kudzudzula chikhalidwe chawo cha kuthupi, palinso mfundo zina zotere zimene zili zofunika.

Pano tsopano pali chidzudzulo pa umbuli wawo:(1) oyera mtima adzaweruza dziko lapansi.

Kodi ndinu amene Mulungu anamusankha, wopanda pake, (wosakwanitsa, koma mwa chikhalidwe wosayenera) kuweruza zinthu zochepa?


Tikafanizira ndi chiweruzo cha dziko lapansi, zimene okhulupilira akutengera ku mabwalo a milandu zoonadi ndi zinthu zochepa.

(2) Ifeyo, oyera mtima tidzaweruza angelo.

Kodi ndife osayenera kuweruza zinthu za m‘moyo uno?

Kodi ndi chiyani chimene chimatilepheretsa kuweruza zinthu za moyo uno?

Anthu amene Mzimu Woyera amawasankha amadziwa kuti zinthu zimenezi ndi zinthu zochepa, zosafunika mphatso ya uzimu, koma nzeru zapadera, kapena kukhulupirika pamaso pa Mulungu.

Koma chifukwa cha kukonda kudzionetsera, oyera mtima a ku Korinto anayenera kukhala pansi pa Mzimu Woyera.

Kotero kuti akanakwanitsa kuthana ndi vuto limeneli.

Nyengo imeneyi ikulankhula zambiri za manyazi awo, komanso kusalemekeza Ambuye kumene kumachitika.

Zikusonyeza kuti PANALIBE M’MODZI wa nzeru pakati pawo abale onse amene anali ndi mphatso kumeneko.
Kusoweka kwakukulu kunali pakati pawo.

Limeneli ndi phunziro lofunika kwa okhulupilira onse!


Ife tikupatsidwa mafotokozedwe ena owonjezera okhudza kusoweka kumeneku: iwo sakuonetsa machitachita a Khristu amene ndi “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima” (Mat. 11:29).

Pakati pawo, panalibe kusoweka chidziwitso ndi mphatso, komanso pakati pawo, panalibe kuonekera kwa chikondi ndi chisomo.

Lerolino mzimu wa Laodeseya ukuonekera, komanso ntchito za thupi zikudzula mphamvu ya Mzimu Woyera.

Chigamulo chake ndi chodziwikiratu: chinyengo m’mitima mwathu chikuonekera mu zochita zoipa, ngakhalenso kuchita chinyengo pa m’bale wathu.Mu zonsezi anthu olakwa komanso olakwiridwa onse akudzudzulidwa.

6:9-11 Choyambitsa Milandu

Chimene chimayambitsa kuchita zinthu mopupuluma chonchi ndi machitachita a thupi.

Kodi tsopano phindu la chidziwitso chawo ndi chiyani?


Zikungoonetsa momwe malingaliro awo alili kutali ndi Mulungu.

Pa zimenezi iwo ndi mbuli.

Kodi sitikudabwa ndi kukula kwa kusoweka kwao pa za uzimu?

Tikuchita bwino kukumbukira kuti tili ndi Mau a Mulungu okwanira komanso chitsanzo chomvetsa chisoni chimenechi

Zotsatira zake tili ndi udindo waukulu kulemekeza Ambuye ndi miyoyo yathu.

Pamene tikudzipima tokha mwa kuunikidwa ndi malemba, timavomereza kuti sindife opambana kuposa iwo.


Mzimu Woyera akukamba za kutumphuka kwa umunthu, kumene kunawanda mzaka zoyambilira ku Korinto, komanso zawirikiza mzaka zino pa dziko lapansi.

Iye akunena momveka bwino kuti zotumphuka zimenezi ndi za iwo amene ali osalungama amene sadzalowa ufumu wa Mulungu.


Zofunikira kuti oyera mtima ku Korinto akukumbutsidwa kuti iwonso anali ochimwa ndi machitachita osalungama otere koma chifukwa cha ntchito ya Mulungu anasambitsidwa (Yoh. 13:10).

Kotero iwo anayeretsedwa mwa kusambitsidwa ndi Mzimu Woyera, (Yoh. 3:5; Tito 3:5).

Mulungu mwa chisomo Chake anawabweretsa iwo mu dziko lina, iwo anapatulidwa, anaikidwa padera mwa Iye; ndipo analungamitsidwa, napatsidwa chilungamo, (Mach. 13:38).

Kotero Mulungu anakonza kusiyana kowonekeratu pakati pa nyengo yawo yakale ndi nyengo yawo yatsopano.

Iye anagwira ntchito.

Tsopano tikhoza kuimba ndi mtima wonse: “Wabwino kotani Mulungu amene timulemekeza”

Iye wapanga zonse mu Dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu –potengera nsembe Yake.

Iye wapanga zonse ndi Mzimu wa Mulungu –Mzimu Woyera walungamitsa choonadi chake cha ichi mwa ife.


Zimakhala zosapereka ulemu kwa Mulungu wathu kutiona ife, amene Iye anatigula, kuonetsera makhalidwe amene anachotsedwa amene mwa kudabwitsa kwake anawakwatula mwa ife.

6:12-20 Osati Mwa Nokha; Ufulu si Chiphaso

Mulungu anatibweretsa ife kwathunthu mu chikhalidwe china, chikhalidwe cha ufulu.

Mu chikhalidwe chimenechi zonse ndi zololedwa.

Komabe, sizonse zimene zili zopindula.

Kwa wina kunenedwa:

ukhoza kusuta ndudu ngati utafuna, koma”…… zinthu zotere sizoyenera, nzosapindulitsa.

Zimalankhulidwa popanda kunena kuti ufulu umenewu sukuphatikizirapo zinthu zimene zili zoletsedwa pano kapena mbali zina za Mau a Mulungu.

Kuchita zonse mu ulemelero wa Mulungu ndiye mlingo wake.

Mlingo umenewu umafunika manyazi pa ziwalo zathu “zimene zili padziko” (Akol. 3:5) cholinga kuti pasapezeke woyera mtima aliyense odzadzidwa kapena kutsogozedwa ndi kathu kamene kali ka thupi.

Kusangalatsa matupi athu sichifukwa chimene timapezekera padziko lapansi.

Matupi athu ndi olemekezera nawo Mulungu amene anatisambitsa ife.

Mulungu yemweyu adzasanduliza thupi (Afil. 3:20, 21).

Mulungu wakonza matupi athu kukhala ziwalo za Khristu.

Ife talumikizidwa kwa Iye.

Matupi athu asaphatikidwe ndi akazi achiwerewere, pakuti awiri amene aphatikana pamodzi asanduka thupi limodzi, monga iwo amene ali m’banja.

Pakusunga matupi athu kukhala oyera kuchoka ku chidetso tikuyenera kuthawa choipa ndi zilakolako za unyamata.


Matupi athunso ndi kachisi wa Mzimu Woyera.

Iye amene ali woyera amakhalira mwa ife payekha.

Chotero matupi athu asungidwe angwiro kwa Mzika ya Kumwamba.

Matupiwa si athu ayi.

Ife tinagulidwa; mtengo wake ndi mwazi wopambana wa Ambuye Yesu.

Chotero ife tikuitanidwa kugwiritsa ntchito matupi athu kukabweretsa ulemelero ndi ulemu kwa Mulungu.

7:1-24 Okwatira Okhulupilira: Banja ndi Lolemekezeka

7:1-6 Chiyanjano pakati pa Mwamuna ndi Mkazi

Mzimu Woyera akuona za nkhani yofanana ndi nkhani ziwiri zimene zakambidwa kale.

Atakhudza za chiyero cha gulu (mutu 5) komanso chiyero cha munthu aliyense payekha (mutu 6) Iye akulankhula ndi mtumwi za chiyero mu chiyanjano chathu cha chibadwidwe.

Oyera mtima ku Korinto analembera mtumwi zokhudza chiyanjano pakati pa munthu ndi munthu mzake.

Iwo amadziwa ndi kuvomereza za kusoweka thandizo mu dela limeneli la moyo wawo.

Sitikudziwa zinakhala bwanji kuti mpingo wa oyera mtima a mphatso za chidziwitso kukafunsa thandizo kwa Paulo, komanso zinaonetsera poyera kuti iwo analibe chidziwitso pa zonse.

Tonse timadalirana wina ndi mzake.

Paulo analankhula mwa chilolezo cha Mzimu Woyera, monga m’modzi amene ali ndi lingaliro la Khristu.

Ngakhale ndi kwabwino (osati monga mwa lamulo) kuti munthu asakhudze mkazi, Mulungu anadalitsa banja kuchokera pachiyambi kuti mwamuna aliyense akhale naye mkazi wa iye yekha, komanso mkazi mwamuna wa iye yekha (5:1)

Monga analembera Hamilton Smith, “kuzidzimbaitsa poziyika pa mlingo wa uzimu kwambiri pakuumilira kusala zinthu zina chifukwa cha chipembedzo zikutsutsidwa kwathunthu2.”

Zoterezi komanso zina zawononga chikhalidwe maka pakati pa iwo amene amadzitchula abusa ndi ena onse ndipo zikupitilira kutero.

Onse a pa banja akuyenera kulolerana wina ndi mzake, pozindikira kuti aliyense ali ndi ufulu wopatsidwa.

Mapeto ake iwo amapereka mpata kwa woipayo kubweretsa kusapereka ulemu ku dzina la Ambuye.

7:7-9 Monga Ambuye Amaperekera

Mtumwi ali ndi malingaliro ake: kunena kuti, aliyense akakhale monga iye ali.

Komabe iye akuzindikira, kuti Mulungu amapereka kwa munthu aliyense payekha monga mwa utumiki ake.

Izi pokhala chomwechi, kaya munthu ndi wosakwatira kapena anaferedwa, ngati afuna, ndi kwabwino munthu woterewu kukwatira.

7:10-11 Palibe Kulekana Ukwati

Mulungu amadana ndi kulekana ukwati (Mal. 2:16), koma “pachiyambi sikunakhala chomwecho” (Mat. 19:3-8).

Kunena kuti pasakhale kulekana ukwati zinalembedwa bwino lomwe kuchokera ku Mat. 19:6.

Ngati pangakhale kulekana ukwati, awiriwo akhale osakwatira kapena ayanjanitsidwe wina ndi mzake.

Limeneli ndi lamulo la Ambuye.

Zikusephana bwanji ndi lamulo lowonetsedwa la Ambuye pamene pali kulekana ma ukwati pakati pa okhulupilira.

Ndi zonyansa kupeza kuti kulekana mabanja kwakula kwambiri pakati pa okhulupilira monganso zilili pakati pa osakhulupilira.

Mochulukira tikuona kuti kusiyana kooneka bwino kumene Mulungu anakonza pakati pa Mkumano Wake ndi dziko lapansi kukuphimbidwa ndi machitidwe a chikunja pakati pa anthu Ake.

7:12-17 Tsopano kuti Munthu M’modzi Wapulumutsidwa

Mu nkhani yotsatirayi mtumwi mosamalitsa akulankhula kuti iye akupereka chigamulo chake.

Koma tikayang’ana mosamalitsa zikuonetsa kuti zikuchokera pa malamulo a Ambuye.

Pamenepa anthuwa anakwatirana kale m’modzi wa iwo asanatembenuke mtima.

Choncho limene poyamba linali banja la anthu awiri osakhulupilira tsopano lakhala banja la kasakaniza pa uzimu: wokhulupilira ndi wosakhulupilira.

Ngati wosakhulupilira wafunitsitsa kukhalabe ndi wokhulupilira, wokhulupilirayo sangapange chisankho cha kuchoka, ngakhale kuziteteza pa mau a “kumangidwa m’goli ndi osakhulupilira” (2 Akor. 6:14).

Pakuti golilo lakonzedwa pamene iwo onse anali munyengo yofanana.


Kuonjezera pamenepa, pali mdalitso wa chisomo umene waikidwa mu nyengo imeneyi ya anthu awiriwa.

Pakuti wokhulupilira akuyenda m’kuwala, mzake wosakhulupilirayo akupangidwa kuzindikira za mphamvu ya chisomo cha Mulungu mwa kupezeka kwa wokhulupilirayo ndipo akhoza kubweretsedwa kwa Mulungu mwa chikhalidwe cha umulungu (1 Pet. 3:1, 2).


Kuonjezera pamenepa, ana awonso ali ndi kukonderedwa kwapadera kuchokera kwa Mulungu chifukwa cha kupezeka kwa oyera mtima mnyumbamo.

Kuwala kwa Mulungu kuli pamenepo.

Mulungu wathu wachisomo amadziwa nyengo zathu ndipo mwa chikondi Iye amakhala nafe mu nyengozo (Yes. 43:2).

Ngati wosakhulupilirayo achita chisankho cha kuthetsa ukwatiwo, wokhulupilira sakuyenera kulimbana naye, pakuti Mulungu anatiyitanira ife ku mtendere.

Malangizo oterewa ndi a mpingo onse, osati mpingo wa ku Korinto okha.

7:18-24 Atumiki a Ambuye

Kaya ndi chikhalidwe kapena nyengo zimene timakumana nazo sizingasinthe mfundo imeneyi.

Mulungu anatiyitana ife akudziwa kale za nyengo zathu ndipo Iye akungofuna kumvera kwathu.

Chotero mfulu ndi kapolo wa Ambuye ndipo kapolo ndi mfulu wa Ambuye.

Iye anatigula ife.

Ife ndi atumiki Ake posatengera nyengo zimene tikukumana nazo.

7:25-40 Osakwatira ndi Amasiye

7:25-35 Kodi Ife Tikuyenera Kuchita Chiyani Tsopano?

Mzimu Woyera akubweretsa mtumwi kulankhula za okhulupilira amene ndi osakwatira kapena amasiye.

Iye alibe lamulo kuchokera kwa Ambuye monga kwatirani kapena musakwatire.

Koma monga munthu amene analandira chifundo kuchokera kwa Ambuye kukhala wokhulupirika mu nyengo yosakwatira, iye akulankhula ngati munthu wa uzimu amene ali ndi ukadaulo wapadera.

Chifukwa cha zinthu zoipa mu nthawiyi, kuli bwino munthu kukhala mu nyengo imene iye ali.

Komabe munthu amene akwatira sanachimwe, pakuti Mulungu anadalitsa banja.

Komabe iwo amene ali pa banja adzakhala ndi zovuta m’moyo uno.

Mau a Mulungu sakudziwa kalikonse kokhudza mapeto a nkhaniyi: kukwatira ndi kukhala moyo wosangalalabe pambuyo pake.

Mu nthawi yochepa imene yatsala, pakufunika kuchita zinthu mofanana, kotero kuti kaya ndi kukwatira kapena kukhala tokha, tichite mofanana pamene tikusangalala, pa chisoni chathu, pa kupambana kwathu kapena pa kukhumudwa kwathu.

Kuti tikatumikire Ambuye popanda chotisokoneza.

7:36-40 Kukwatira Mochedwa M’moyo

Mtumwi akulankhula za munthu amene amakwatira mochedwa m’moyo.

Kungoganizira kuti munthu wotereyu waganiza kukhala wosakwatira chifukwa cha ntchito ya Ambuye.

Oyera mtima akutsimikiziridwa kuti kukhumba kukwatira ndi kololedwa pamaso pa Mulungu.

Munthu ameneyo sanachimwe ayi.

Mbali inayi kuletsana kukwatira zingathe kupangitsa munthu kuchimwa.

Iye amene akhoza kuyenda moyo wakudziletsa achita bwino, pakuti onse ali ndi mphatso ya payekha kuchokera kwa Mulungu.

Kuvomerezana kukwatira ndi kwabwino.


Kusakwaniritsa udindo umenewu ndi kwabwino.

Kusiyana banja si malingaliro a Mulungu: “Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse” (Mat. 19:6) zimenezi zizakhala zoona nthawi zonse.

Ngati wina amwalira, wotsalayo angathe kukwatiranso amene iye wasankha.

Komatu chisankhochi chichitike pansi pa chitsogozo cha Ambuye.

Potengera zimene zanenedwa, munthu wosiyidwayo amene wakhalabe wosakwatira, ndi wokondwa molingana ndi maganizo a mtumwi.

Mfundo imeneyi ikuchokera ku malingaliro a Mzimu wa Mulungu.

8:1-6 Ufulu Wolimbitsidwa ndi Chikondi – Ufulu wa Ndani?

Zikuonetsa kuti kudya chakudya choperekedwa ku mafano chinali chinthu china chimene chinawakhudza oyera mtima a ku Korinto.

Mu mzinda umene kupembedza mafano kunali kochuluka, ndi chachidziwikire kudya nyama yoperekedwa kwa mafano inali nkhani yaikulu kwa iwo amene Mulungu anawatulutsa ku zochitika za anthu a mu mzindawo.

Zimene oyera mtima amadziwa zokhudza mafano zinawapangitsa iwo kukhala ovutika mu mtima.

Chomwecho Mzimu Woyera anatsogolera mtumwi kuyambira pa mlingo umenewu wa chidziwitso.Okhulupilira onse ali ndi chidziwitso, pakuti “kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa” (Miy. 1:7).

Koma pali chenjezo: chidziwitso chongofuna kudziwa chabe chimamusiya munthu kudzala ndi kunyada.

Pamene chidziwitso chikhala chodziganizira chokha kufuna kutamandiridwa, chikondi chimachoka, chimakayang’ana ena.

Chidziwitso ndi cha nthawi yochepa (13:9).

Ngakhale tonse tili ndi chidziwitso, ifetu tilibe chidziwitso chonse.

Tonse tikuphunzirabe.

Mbali inayi, chikondi cha Mulungu chikuzinga m’mitima mwathu, chikumanga, ndipo chimaumba chidziwitso.

Munthu amene amakonda Mulungu amadziwika mwa Mulungu kwathunthu.

Mulungu yekha ali ndi chidziwitso chonse.

Pamenepo Mulungu adzavumbulutsira kwa iwo amene amamukonda Iye posatengera kuti iwo amakonda oyera mtima amzawo kapena ayi.

Iye wapereka lamulo ili: “Iye amene akonda Mulungu akondenso m’bale wake” (1 Yoh. 4:21).

Chomwecho pofuna kukwaniritsa lamulo limene “silili lolemetsa” (1 Yoh. 5:3) oyera mtima ku Korinto anayenera kuonanso ufulu umene anali nawo mwa Khristu komanso momwe akukakamilira ufulu wawo aliyense payekha.


Sitikuyenera kuchita mochepa.

Tisanapitilire ndi mzere umenewu, Mzimu Woyera amapima chimene chimadziwika ndi mafano.

Fano si kanthu konse ayi.

Fano si Mulungu, ndipo silichokera kwa Mulungu.

Pali Mulungu m’modzi yekha.

Umunthu unalingalira ndi kumanga zinthu zimenezi.

Chomwecho mu umunthu muli milungu yochuluka zedi komanso ambuye ochuluka monga umo alili amisili omanga nyumba.

Komatu monga umo analankhulira Abraham Lincoln mu mfundo iyi:

Kutchula mchila wa nkhosa kukhala mwendo sikupangitsa mchilawo kukhala mwendo,” chimodzimodzinso kutchula mafano milungu ndi ambuye sizipangitsa zinthuzo kukhala choncho.


Wokhulupilira wina aliyense, mwana wa Mulungu wina aliyense amadziwa zimenezi.

Kwa ife okhulupilira pali Mulungu m’modzi, Atate Chiyambi cha zinthu zonse (Mach. 17:28) ndipo ife tili pano mwa kufuna Kwake (Chiv. 4:11).

Kwa ife okhulupilira pali Ambuye m’modzi Yesu Khristu.

Iye ndi Mlengi yekhayo (Yoh. 1:3; Akol. 1:16) ndipo ife tilipo chifukwa cha Iye (Chiv. 5:9, 10).

Ife oyera mtima timadziwa ndi kuvomereza kuti zinthu zonse chiyambi cha kupezeka kwake komanso cholinga cha kupezeka kwathu chili kwa Mulungu yekha.

Pali Ambuye Yesu Khristu m’modzi amene analenga zonse.

Chotero milungu yambiri ndi ambuye zimene zikhoza kukambidwa m’dziko lapansi ndi chikonzero chabe cha malingaliro a munthu.

Pali Mulungu m’modzi yekha ndipo fano lili chabe.

8:7-13 Ufulu Woyendetsedwa ndi Chikondi

Mwatsoka okhulupilira onse si omangilirika mu chidziwitso chimenechi.

Pali okhulupilira kufika lero lino amene amatenga fano ngati chofunikira pa zifukwa zawo.

Ngati akudya nyama yoperekedwa ku mafano, amaononga chikumbumtima chawo, ndipo amaika umboni wawo pa chiopsezo.

Tsopano, ngakhale kuti Mulungu Mwini anapereka nyama kwa munthu ngati chakudya, kudya nyama sikutipangitsa ife kuvomerezedwa kwa Mulungu.

Nyama ndiyo ya mimba (6:13).

Ufumu wa Mulungu suli mu “nyama kapena chakumwa” (Aroma 14:17).

Chomwecho, iye amene akana kudya nyama siolandiridwa mochepa pamaso pa Mulungu kusiyana ndi iye amene akudya nyama ndi chikumbumtima chosautsika.

Komabe kutsutsana kudzakhalako pa nkhani imeneyi.

Chotero mtumwi akupereka chenjezo limeneli kwa woyera mtima amene ali wolimba ndipo ali pa ufulu wakudya: yang’anirani kuti chilimbiko chanu, ufulu wanu zisakhale chokhumudwitsa kwa m’bale wanu amene simukufana naye mlingo wa chilimbiko.

M’bale amene amatenga fano kukhala lofunika pamene awona ufulu wanu wafika pa mlingo woterewu: -kudya nyama yoperekedwa nsembe kwa mafano kapenanso kukhala nawo pa phwando mu kachisi la fano zingathe kumukopa iye kuchita chimodzimodzi.

Kwa iye amene ali ndi chikumbumtima pa zimenezi, ndi tchimo, pakuti sakuchita mwa chikhulupiliro.

Zomvetsa chisoni kwa m’bale kukhala patsogolo kuchita zinthu zimene ena akhoza kukopeka nazo zimene zikhoza kuwaononga iwo.

Ameneyu ndi amene Khristu amukonda kwambiri kumufera.

Kunyalanyaza zimenezi zimabweretsa kusalemekeza kwa Ambuye.

Limeneli ndi tchimo kwa m’bale wake komanso tchimo pamaso pa Ambuye.

Tsopano si nkhani yokhudza ufulu, kapena chidziwitso, koma chikondi.

Wina akhoza kutsutsana ndi chidziwitso komanso ufulu wa mzake.

Wina akhoza kufuna m’bale wake, inde, aliyense kuti abwere mu chidziwitso chimenechi.

Koma kodi chikondi cha Mulungu chimakhala bwanji mwa wotere?

Iye amene akonda Mulungu mwa Mulungu amalamulidwa kukonda m’bale wakenso (1 Yoh. 4:21).

Kumeneku ndi kuomba mkota kumene Mzimu Woyera akubweretsa kwa mtumwi ndiwo machitachita osavuta a chidziwitso cha chikondi kwa wina ndi m’bale wake:

Pamene pali ine, sindidzadya nyama kuti ndisakhumudwitse m’bale wanga.

Chimenechi ndi chikondi cha umulungu, chikondi chimene chikuchokera ku mtima wa Ambuye Yesu, chikondi chimene chimadutsa ufulu wake cholinga kuti m’bale wina asakhumudwe.

Chimenechi ndi chikondi chimene chimamangilira.

Mulungu angathe kupangitsa chikondi chimenechi kuonekerabe pakati pa oyera mtima Ake.

Ena akhoza kutsutsa kuti nkhani imeneyi ndi yakale, ndipo ikukhudza kwambiri chikhalidwe cha Akorinto komanso maiko a chikunja.

Palibe chiopsezo china chilichonse chotere ku ‘maiko a Chikhristu’.

Yankho lake ndi la pompopompo: Pali zinthu zimene zili zololedwa, zimene zili chabe molingana ndi chidziwitso chathu.

Palinso zinthu zina zimene zikhoza kutengedwa chifukwa cha mankhwala, molingana ndi chidziwitso chathu.

Pali abale amene ali ndi chikumbumtima chofewa pokhudzana ndi zinthu zimenezi.

Kwa ena kukhala ndi nyumba yogulitsira mowa amaona kuti palibe vuto lililonse.

Cholinga chikhoza kukhala chomveka m’malingaliro a mwini wake.

Ku phwando, wina akhoza kutenga chikho cha madzi koma kwa ena, maka iwo amene amapsinjika ndi mowa, imeneyi ndi nkhani yoipa.

Pamenepa ndi pomwe chikondi chomangilira chimaonekera.

Iye amene amakonda Mulungu akuyeneranso kukonda m’bale wake.

Ufulu wa Kapolo wa Mulungu

Phindu lake limaoneka pakulankhula ngati malangizo amapeza mphamvu pakuonetsera ntchito.

Pa maubale a anthu “werengani milomo yanga” kawirikawiri zimathera milomoyo kuwerenga.

Sizili chonchi ndi Mau a Mulungu.

Chiphunzitso Chake ndi cha muntchito pakuti malamulo Ake sioipa.

Pamene Mzimu Woyera anatsogolera Paulo kuyankha nkhawa za oyera mtima pokhudzana ndi zinthu zoperekedwa kwa mafano, Iye anafotokozera mfundo zofunika kwa okhulupilira.

Chikondi kwa Khristu komanso chikondi kwa m’bale wofooka zimatsogolera wokhulupilira kukhala wopanda ufulu mu zinthu zina.

Iye tsopano amapita chitsogolo kuwonetsa kuti kudzikana wekha kotere kumayembekezedwa pa mtumiki wa Mulungu, kumutsogolera kuti mtumiki akuyenera kukhala pansi pa ufulu wake chifukwa cha Ambuye komanso kuthandiza anthu Ake.

9:1-14 Paulo, ndi Ndani?

Otsutsana ndi mtumwi akukhala ndi mtsutso waukulu pa iye

Zochita za aphunzitsi onyenga zakhala zikusokoneza anthu kotero kuti oyera mtima ku Korinto akukaika zokhudza Paulo.

Kodi iyeyu ndi mtumwidi?

Kodi umboni wake uli kuti?

Mobwereza, Mzimu Woyera amene amachita zonse mwa ulemelero wa Khristu akugwiritsa ntchito chipongwe chimene mtumwi akulandira kukakwezeka Ambuye Yesu komanso kukamulungamitsa mtumiki Wake Paulo.

Chimene chimamuyenereza munthu kukhala mu utumiki wa utumwi ndi chakuti akhale munthu amene anamuonapo Khristu, kukhala mboni ya kuuka Kwake (Mach. 1:21 mpaka mtsogolo).

Paulo akulandira mwayi umenewu munjira yapamwamba (Mach. 9:3 mpaka mtsogolo).

Iye akuvomereza, “ndipo potsiriza pake pa onse, anaonekera kwa inenso monga mtayo” (15:3). 3

Chomuyenereza chimenecho chakwaniritsidwa.

Iye akuthana nalo vutoli ndi umboni wosakaikitsa.

Oyera mtima a ku Korinto ndi zotsatira za utumiki wa mtumwi.

Ngati utumwi wake si weniweni, zimenezi zikupereka mafunso ambiri zokhudza chipulumutso chao.

Kwa ena onse amene Paulo sanawachitireko umboni wa Khristu akhoza kukaika za utumwi wake koma Akorinto, SAMAKAIKA, pakuti kutembenuka kwao ndi zotsatira za ntchito yake pakati pawo.

Komabe dandaulo lina likubwera ndipo mwachidule likuyankhidwa ndi Mau a Mulungu komanso chidziwitso.

Zinthu zonse ziloledwa kwa ine” (6:12) ndipo Paulo ali nawo ufulu pa kupindula mu zinthu wamba za m’moyo: kudya ndi kumwa, kukwatira kapenanso kulembedwa ntchito ina iliyonse.

Atumwi ena anachita ichi mwa ulamuliro wa Ambuye Yesu, ndipo abale ena akuchitanso ichi.

Mau odziwikiratu amaphunzitsa kuti msilikali amasamalidwa ndi gulu limene linamulemba iye ntchito.

Mlimi amadzala ndi cholinga chofuna kukolola; m’busa amapindula kuchokera ku ziweto zimene akusamalira.

Kuonjezera pamenepa, malemba akuperekera umboni pa mfundo imeneyi: Lamulo la Mose likuonetsa kuti chimenechi ndi chifundo posakaniza ng’ombe kudya pamene ikugwira ntchito (Deut. 25:4).

Zimenezi zinalembedwa osati kuti tisamalire kokha ng’ombeyo komanso kuti tikasogozedwe ndi mfundo imeneyi.

Chiyembekezo chikaonekere mu ntchito zathu monga umo zikuonekera ndi mlimi komanso m’busa.

Mfundo yodziwikiratu ndi iyi: iwo amene amafesa zinthu za uzimu ali ndi ufulu opatsidwa ndi Mulungu kulandira zinthu zosakhalitsa za iwo akupindula kuchokera mu ntchito ya uzimu.

Chomwecho monga m’modzi amene ntchito yake yeniyeni inabweretsa phindu lochuluka la uzimu, mtumwi Paulo ali ndi ufulu wochuluka ku zopindula za kuthupi kuchokera kwa oyera mtima amenewa kuposera ena onse amene amapindula pa zimenezi.

Iye akuonjezera pa fanizo lodziwikiratu la Alevi ndi ansembe amene amatumikira pakati pa Ayuda.

Iwo amagwira ntchito ndi kutenga nawo gawo pa zinthu zoyeretsedwa za mkachisi komanso pa guwa.

Zimenezi Ambuye anazidzodza mu ntchito ya uthenga wabwino: iwo amene amafalitsa uthenga wabwino akuyenera kukhala monga mwa uthenga wabwinowo.

Kenako mfundo ikukhazikitsidwa mwamphamvu.

Onse amene amakonda Ambuye asamalitse kuti asadelere mtumiki weniweni woitanidwa ndi Iye ku utumiki Wake.

Ngati tichita zimenezi ife tidzakhala tikuuluka mu nkhope ya mau Ake, ndipo zotsatira zake tidzakhala ifeyo olephera.” (F.B. Hole) 4

Komabe mtumwi sadakakamile zomuyenereza zimenezi.

Chikhumbokhumbo chake chofuna kugwira ntchito ya ulere ya uthenga wabwino wa Khristu pakati pawo chinamulimbikitsa iye kugwirabe ntchitoyo.

Mtumwi ndi osamalitsa kupereka ulemu kwa Khristu Yesu Ambuye wake.

Ifenso tikuyenera kukhala osamalitsa chimodzimodzi monga akutsanza mtumwi.

9:15-23 Chitsanzo cha Mtumwi pa Kulengeza Uthenga Wabwino

Posaitanitsa zomuyenereza zodalitsika ndi Mulungu Mwini, mtumwi akuonetsera poyera kuipa kwa moyo wa uzimu wa oyera mtima a ku Korinto.

Iye sakutchula za izo kwa iwo kuti apatsidwe.

Iye anasankha imfa kusiyana ndi kukhala wolekelera pozitamandira.

Mulungu wakhazikitsa ulaliki wake.

Iye akudzitenga kukhala mtumiki waphumphu (Mach. 9) kuti akakwaniritse utumiki umenewo.

Ngati ntchito ichitika modzipereka, iye alandira mphoto.

Ngati ichitika mosadzipereka, iye ali m’mavuto akulu chifukwa sangathenso kusiya utumikiwo.

Kodi mphoto ilipo?

Inde ilipo, ndipo kwa Paulo imeneyi ndi mphoto imene mtumiki weniweni wa Mulungu akuyenera kuifunafuna: kuti uthenga wabwino ukakhale wopanda mtengo wake kwa anthu ena (ngakhale wa mtengo waukulu kwa iye mwini).

Iye sakugwiritsa ntchito ufulu wopatsidwa ndi Mulungu pakulalikira Uthenga.

Iye ndi womasuka, koma sakulekelera.

Monga chomwecho iye ali mtumiki wa machawi wa Ambuye, mwakuti iye mwa ufulu akukhala mtumiki wa onse cholinga kuti akawakope ambiri kwa Ambuye.

Iye akupereka magulu anayi amene nkhani zawo akugwiritsa ntchito kufotokozera kukula kwa machawi ake pa uthenga wabwino: Ayuda, amene ali omvera lamulo (ma Zealot), iwo opanda lamulo (Amitundu) komanso ofoka.

Zoonadi, aliyense wa ife amapezeka mu limodzi kapena kuposerapo mwa magulu amenewa.

Iye akulankhula kwa Ayuda, atadziwa kwathunthu za mbiri yawo, chipembedzo chawo ndi malamulo awo, osati kutengera kapena kudzipereka kuchoka mu Chiyuda, koma kugwiritsa ntchito zimene iwo anazigwiritsitsa kwambiri kuwabweretsa iwo ku uthenga wabwino wa ulemelero wa Khristu.

Iwo amene ali pansi pa chilamulo ndi Ayudanso koma zikuonetsa kuti iwo anali anthu achipembedzo kwambiri, osamalitsa chilamulo mwa machawi.

Kwa iwo iye anakhala ngati omvera lamulo.

Iye akulemekeza kudzipereka kwao ku lamulo ndipo akugwiritsa ntchito chimenechi ngati poyambira kuwabweretsa iwo kukwaniritsidwa kwake mwa Khristu.

Kwa iwo opanda lamulo, pa mlingo ulionse umene akupezeka, iye akugwiritsa ntchito kulephera kwa nzeru zawo ndi chipembedzo kuwabweretsa iwo ku choonadi monga zilili mwa Yesu.

Kwa ofoka, anakhala ngati wofoka.

Iye anaphunzira kukhala ngati mwana cholinga kuti akaganize molingana ndi malingaliro a mwana, monga mphunzitsi wa ana akuyenera kuchitira. 5

Iye akutsatira mfundo imeneyi ndi malingaliro othera amodzi: chipulumutso kwa onse.

9:24-27 Chenjezo la Mtumwi

Tsopano mtumwi akutenga chimene chili chidziwitso chodziwika kwa onse cholinga kuti akafotokozere njira ya mtumiki wa Ambuye kuti ndi njira ya kudzikana wekha.

Kufotokozera kwake kwa munthu wochita masewero, kaya ndi wothamanga kapenanso ankhonya, zikuonetsera mfundo yodziwika kwa tonse.


Moyo wao ndi odzikana okha umene uli ovomerezeka ndi cholinga chopeza chipambano pa ulemelero: nthawi imeneyo anali ndi korona wa masamba tsopano ali ndi korona wa mkuwa.

Mphoto zawo komanso ulemelero wawo zinazima chifukwa sizokhalitsa.

Mtumiki akuyenera kukhala mu mfundo yomweyi ya kudzikana wekha imene mtumwi ndiye chitsanzo chabwino, cholinga kuti akapeze mphoto.

Mosiyana ndi momwe zimachitikira mu masewero, mu utumiki wa Mulungu atumiki a Mulungu enieni onse amalandira mphoto.

Mau akuti “kukanidwa” anabweretsa kudabwitsika kwakukulu pakati pa okhulupilira.

Kukhulupilira kuti Paulo akhoza kuganizira kuti ndi zotheka kutaya chipulumutso ndi zosiyana ndi chitsimikizo chimene iye akupereka mu makalata ake.

Kuganiza kuti zimenezi zikungokhudza okhulupilira enieni zingapangitse chitsimikizo chimenechi kukhala chokaikitsa.

Pa kulankhula pamwamba pa utumiki kwa oyera mtima a Mulungu, Paulo anatsutsana nawo antchito a chinyengo, ulusi umene wausoka mu kalata imeneyi kuyambira pa mutu 3:17.

Mutu otsatira ukukonza malingaliro amenewa mwinanso kupitilira pamenepa, pakugwiritsa ntchito zimene zinachitika kwa iwo amene anatuluka ku Aigupto kuchokera pa mfundo ya Pasaka wa mwanawankhosa.

Zotsatira zake, Paulo akusamutsa mtundu wa kagwiridwe ka ntchito kameneka kwa iye yekha kuonetsera kuti ndi zotheka munthu kutenga ntchito ya Ambuye, kulalikira uthenga wabwino wa chisomo ndi chiphunzitso cha Mulungu popanda choonadi chenicheni cha chipulumutso.

Pakati pawo pali ena amene malankhulidwe awo amati: “Chitani zimene ndikulankhula osati zimene ndikuchita”.

Chikhristu chadzadza ndi anthu amene amalalikira mau koma samakhulupilira malemba, anthu amene amakomedwa ndi zikhumbokhumbo za thupi.

Anthu otere ndi amene adzakanidwa chifukwa cha chinyengo chawo.

Mfundo imeneyi ikukonza mbali ina ya zokambirana za mutu umene ukubwerawu.

GAWO 5 10:1-11:34 UNSEMBE WOYERA

10:1-13 Zitsanzo zochokera Kumbuyo

Polankhula kwa Akorinto kumbali yokhudza kudziyang’anira, Mzimu Woyera akutsogolera mtumwi kukaonetsera mu mfundo yomangilirika zotsatira zake za anthu amene ali osapulumutsidwa koma amachita mwambo wa Chikhristu.

Iye akudzudzula za nyengo ya uzimu wa Akorinto pakuonetsa zimene zinawachitikira iwo amene anapulumutsidwa kuchoka ku Aigupto.

Kudzudzula kwake kukufunika kudzipima okha (2 Akor. 13:5).

Chimenechi ndi chidziwitso chofunika “pakuti zonse zimene zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza” (Aroma 15:4a).

Kunena kuti iye sakuphatikizirapo zolembedwa za chikunja zili ndi umboni woonekeratu, pakuti akupitilira kulankhula “kuti mwa chipiliro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo” (Aroma 15:4b).

Onse amene anatuluka ku Aigupto kuphatikizirapo “ambiri osokonezeka” (Eks. 12:38 mpaka mtsogolo) anali pansi pa chitetezo cha mtambo.

Onse anaona chozizwa pa Nyanja Yofiira.

Pamene iwo anasiyanitsidwa ndi kupulumutsidwa (kutetezedwa) kuchoka ku Aigupto ndi anthu a ku Aigupto (Eks. 14:19 mpaka mtsogolo), iwo anabatizidwa mwa Mose, pakuti iye anali mtsogoleri wawo.

Zopindula zawo zinali zofanana kwa onse.

Iwo onse anadya chakudya chofanana; manna kuchokera kumwamba (Eks. 16) ndipo onse anamwa kuchokera ku Mwala (Eks. 17), amene ali Khristu.

Komabe ngakhale anakumana ndi kukonderedwa kwapadera koperekedwa ndi Yehova, iwo analephera kupilira ndi kulimbikitsidwa m’chikhulupiliro chifukwa cha mitima yawo yosatembenuka. 6

Chomwecho mtumwi akubweretsa mitundu yotereyi kwa Akhristu a kudera.

Kaya anali ku Korinto kapena Filipi, ku Galatiya kapena ku Efeso, iwo amene amatchula pa dzina la Ambuye awonetsetse kuti chikhalidwe chimene chimaotsedwa pakati pa iwo amene anatuluka ku Aigupto, chikupezeka mu mtima wa munthu wina aliyense, “ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika” monga zilili (Yer. 17:9; Mat. 15:18 mpaka mtsogolo).

Mayendedwe ake nthawi zonse amakhala chimodzimodzi: mitima yawo imakhumba zimene ikufuna kuchita mwa chilengedwe, zinthu zoipa.

Zimenezi posakhalitsa zimatenga malo amene Mulungu akuyenera kukhalapo; zimasanduka mafano.

Pambuyo pa mafano zoipa zimatsatira.

Pakudzadzidwa ndi kunyada, mtima umadelera Yehova, kumunyozetsa Iye ndi atumiki Ake.

Chizolowezi cha uchimo chimenechi chimayamba ngati kambeu kakang’ono mkati mwa mtima ndipo chimakula kufika pa chipatso chachikulu chonyozetsa Mulungu, osawerengera zokoma zimene Mulungu anazipereka.


Ngakhale a Israeli anaona chiweruzo cha Mulungu pa Aigupto, ngakhale analandira chitetezo Chake komanso machitachita onse a Chisomo Chake, mitima yawo inali yosakhudzika ndipo chikumbumtima chawo chosakhudzika.

Zimene anadutsamo zinali za mitundu mitundu, osati monga mwa mbiri yolembedwa, pakuti Mulungu anatilembera izi monga chenjezo kwa ife.

Tsopano Mzimu Woyera akuonetsera bwino lomwe amene Iye akufotokoza.

Iye samangolankhula kwa iwo amene Paulo anali nawo pamodzi mu nyengo imeneyo ndi oyera mtima a ku Korinto. Ifenso tikuphatikizidwamo, amene “mapeto a dziko atifikira”.

Iye akutanthauza aliyense amene amaitanira padzina la Ambuye ndipo kwa iwo akuwapatsa chenjezo lotsutsana ndi kudziyenereza, azipime okha ndi kufufuza mitima yawo.

Yeremiya anaganizira za chinthu chomwechi kwa iwo amene amamutsatira.

Tisanthule nitiyese njira” (Maliro 3:40).


Kodi chilipo chimene chingayambitse nkhawa yochepa?

Mtumwi akutitsimikizira ife kuti yesero lililonse limene limabwera kwa ife ndi mtundu wa yesero limene limabwera kwa anthu.

Mayesero athu siapadera kapena owonjeza.

Koma Mulungu…” mau awiri a mtengo wapatali komanso opereka chiyembekezo!

Amatikumbutsa ife kuti Mulungu wathu amasamalira!

Iye amadziwa kalikonse ka thupi lathu.

Iye amadziwa aliyense wa ife payekha payekha.

Iye adzatipatsa thandizo lofunikira kutipambanitsa ku mayesero.

Kodi Ambuye Yesu si Wamkulu Wansembe wathu?

Adamva zowawa poyesedwa yekha” ndipo akhoza kutithandiza ife (Aheb. 2:18).

Zodabwitsa kudziwa zimenezi komanso kudalira pa Iye.

Mzimu woyera akuonetsera mwa mphamvu za kuperekedwa kumeneku komanso kuthekera kwa Wamkulu Wansembe wathu.

Zimenezi ndi zolowa za tonse.

Udindo wathu wogwirizana ndi zimenezi ndiko kuthawa mafano.

Pa mutu 8 mtumwi akutsindika kuti mafano ali chabe.

Mfumu Hezekiya anaonetsera zimenezi pamene anapeza kuti Israeli akufukiza nsembe ku njoka ya mkuwa, imene Mose anakonza molamulidwa ndi Mulungu (Num. 21:8).

Iye anaiphwanya mtidzidutswa, naitchula monga mwa kupangidwa kwake, “chimkuwa” (2 Maf. 18:4).

Zoonadi fano lili chabe.

Komabe, ngakhale mtumwi akukana fano (chinthu chopangidwacho) kuti kulibe, iye sakukana kuti kupembedza mafano kuliko (lingaliro).

Zotsatira zake ndi zazikulu.

Chinthucho pachokha ndi chopanda pake (mu nthawi imeneyo mwina chinali chinthu chabe cha ma kilogalamu ochepa); kupembedza mafano (lingaliro) ndi chisonyezo cha chikhalidwe cha uzimu.

Mulungu akuchotsedwa pa malo ndi kuikapo ziwanda.Kotero ife tikupatsidwa chenjezo kuti tisiye kupembedza mafano, ndipo tikane zimenezi munjira ina iliyonse.

Ife tikuyenera kuchoka ku zinthu zonse zimene zingayambitse zikhumbokhumbo zoipa ndi kubwera pakati pa miyoyo yathu ndi Mulungu.

Nthawi zonse pamene ife tichimwa, zimakhala zotsatira za zilakolako zathu (kupembedza mafano m’mitima mwathu) kupezerapo mpata mwa ife (Yak. 1:14, 15).


Pokhapokha ngati tithawa kupembedza mafano, timadzipanga tokha kukhala osalemekeza Mulungu.

Ndi zofunikira kwa aliyense wa ife kudzipima yekha, kudzifunsa moona mtima:

Kodi Ambuye, ine ndili ndi chinthu pansi pano

chimene chingagawe mtima wanga kuchoka kwa Inu;


Chimene chingapatutse mayendedwe ake abwino

Pakuyankha kukhulupirika Kwanu?

Inde, ndiphunzitseni ine mwachangu kubwerera,


Ndipo pangitsani mtima wanga kuyaka mwatsopano. 7

10:15-22 Ufulu Woyenera ndi Wosayenera pa Gome la Ambuye

Langizo limeneli kwa anthu a nzeru kupima mau a Mtumwi ndi kofunikira.

Chimene chinatsogola ndi chikumbutso choopsa cha momwe kusokonekera kwa mtima wa munthu kulili.

Kufanizira ndi zimene zikubwera, langizo limeneli likubweretsera anthu a nzeru kuzindikira malo oopsa kumene mtima wopsinjika ungapite.

Pakungotchula za Gome la Ambuye mu Chipangano Chatsopano, ife timafika pa chiyanjano cha mtengo wapatali chimene okhulupilira enieni onse akubweretsedwa posatengera zipembedzo za masiku ano (1:9; 1 Yoh. 1:3).

Gome limalankhula makamaka za kubwera pamodzi kapena chiyanjano

Danieli 11:27 akutionetsera momwe munthu mwa chikhalidwe chake cha uchimo komanso zotsatira za luntha lawo mu ndale zikuwapangitsa kutenga choonadi chimenechi kukhala chopusa.

Gome la Ambuye limatibweretsa pa kuganizira za chikho ndi mkate.


Chikho ndi chiyambi cha kupezeka kwathu pa Gome la Ambuye; chimenechi ndi chithunzithunzi cha mwazi wokhetsedwa ndi Ambuye Yesu, umene umatiyeretsa ife ku machimo onse, umene aliyense amene akhulupilira abweretsedwa chifupi ndi Mulungu.

Amenewa ndiwo okhulupilira enieni.

Chikho chimalankhula za mwazi wa Khristu.

Gulu limeneli, lopangidwa ndi anthu angapo, limakhala gulu limodzi lokhalo.

Zimenezi zimaonekera mu umboni wa mkate umodzi.

Mzimu Woyera mu ntchito Yake pa ife komanso mwa ife zinabweretsa zimenezi.

Iwo amene amapezeka mu gulu limeneli ali pa Gome la Ambuye.

Mosiyana mtumwi Paulo akutchulapo zinthu ziwiri: guwa la a Israeli la mthupi komanso nsembe za Amitundu.

Kumbali ya Israeli onse amene amadya pa nsembezi anali otenga nawo gawo pa guwa.

Zimenezi zikutchulidwanso ku Ahebri 13:10.

Pamenepa akufotokozera momveka bwino kuti palibe kulumikizana pakati pa iwo amene ali pa Gome la Ambuye ndi iwo amene akhala nawo pa guwa la Israeli.

Ikukhazikitsanso mfundo yokhayo yomveka bwino.

Komabe kutengera ndi zomwe zimawakhudza Amitundu, iye akutenga mfundo ya pa mutu 8, ndi kulumikizitsa ndi mfundo imene wangoikhadzikitsa kumene.

Kuonjezera pamenepa, zinthu zimene zimaperekedwa nsembe ku mafano zimaperekedwanso nsembe ku ziwanda.

Iye akudziwa popanda kukhala ndi ubale wa chidziwitso kuti okhulupilira akuyenera kukhala pa chiyanjano ndi ziwanda.

Kunena zoona, ndi kosatheka kwa wokhulupilira, amene ali pa Gome la Ambuye kukakhala pa Gome la Ambuye komanso pa gome la ziwanda.

Choonde onani chikhalidwe cha mau osakhala bwino: Simungathe (ndime 21).

Chimenechi chakhazikitsidwa ndithu ndipo tsopano chikumbumtima chikuyenera kutenga gawo.8

Ngati chikumbumtima sichingakhudzike, wokhulupilira ameneyu amakhala pa chiopsezo chomupangitsa Ambuye kukhala wa nsanje,9 pomubera Ambuye chinthu chimene chikuyenera kukhala Chake.Lero, mfundoyi ndi yofunikira kuganizira pamene tiona kubwera pamodzi kwa zipembedzo.


Pali kuchuluka kwa chikunja mbali inayi komanso Chiyuda mbali inayi chimene chasakanikirana ndi Chikhristu; pali kuchuluka kwa chikhalidwe chimene chikupezeka kumadera a Chikhristu komanso mu zipembedzo chimene kupezeka kwake ndi chizolowezi chenicheni chokhazikitsa zinthu kumene kwa iwo ndi zofunikira zedi kuposa Khristu.

Imeneyi ndi njira yatsopano yopembedzera mafano, chinthu chimene tikuyenera kusamala nacho.

10:23-11:1 Kukopa Ena

Mzimu woyera akuyankha mtsutso umene ukhoza kubwera: pakuti fano ndi chabe, ndipo nyama yoperekedwa kwa mafano sinapangidwe munjira ina iliyonse yosiyana, kuposa munthu kungodya ndi malamulo.

Ngakhale tikudziwa kuti zinthu zonse ndi zololedwa, timadziwanso kuti zinthu zonse sizopindulitsa kapena sizonse zili zomangilira.

Ife timauzidwanso kuti zinthu zonse zipangidwe kuti zikamangilire (14:26), pakuti moyo wa wokhulupilira simoyo woganizira za iwe wekha.

Chomwecho ife timafunitsitsa kuthandiza ena.


Zotsatira zake zikukhadzikitsidwa moonekeratu: wina akhoza mwa ufulu kugula nyama pa msika asafunse kathu chifukwa cha chikumbumtima.

Pakuti dziko lapansi lili la Ambuye ndi kudzala kwake.”

Pa chifukwa chimenechi, wina akhoza kukhala nawo pa phwando la chinkhoswe ndi kudya nyama momasuka popanda kufunsa kathu.

Ngati wina apereka chidziwitso kuti chakudyacho chinaperekedwa ku mafano, chifukwa cha chikumbumtima cha munthu ameneyo, musadye chakudyacho, “Pakuti dziko lapansi lili la Ambuye ndi kudzala kwake.”

Kupereka chidziwitso chimenechi ndiye kuti munthu ameneyu ali ndi chikumbumtima cha zimenezi ndipo akuvutika nacho.

Chomwecho ufulu wa wokhulupilira siwopangitsa ena kuti akhumudwe –pamenepa kukhumudwitsa iye amene wamupatsa chidziwitso kapena iwo amene akuona- zimene iye akhoza kuvomereza.

Kulemekeza Mulungu kwake kusapangitse ena kufunsa Chikhristu chake kapena kunyozetsa Mulungu.


Mapeto akenso siwosokonekera: Zonse zimene tichita, timachita kukabweretsa ulemelero kwa Mulungu kumwamba.

Ifenso sitimapangitsa abale athu pansi pano kukhumudwa.

Makamaka miyoyo yathu yonse ikhale yodzala ndi machitachita a Mzimu kuti tisakhumudwitse aliyense wa magulu atatu amene Mau a Mulungu anawagawa mokhudzana ndi dziko lapansi: Ayuda, Amitundu kapena Mkumano wa Mulungu.

Mfundo imeneyi ya moyo ikhala ndi zotsatira zokhazikika pa chikhalidwe chathu.


Ife tikuona kuti Mtumwi mwini ndiye chitsanzo cha khalidwe lotereli pachikhumbokhumbo chosazikonda ndi kuyetsetsa kusagwedezeka kukopa ena kwa Khristu.

Iye akutsatira Khristu mu chikhumbokhumbo chimenechi ndipo akadakonda tonse titamutsatira monga iye akutsatira Khristu.

MUTU, UMBUYE komanso Mgonero wa Ambuye

11:2-16 Mutu Kudziwika mu Zinthu Zonse

Mzimu Woyera akukhadzikitsa mfundo yofunikira kumayambiliro a gawo limeneli.

Mtumwi akuwayamikira iwo pa zinthu zabwino: pomukumbukira iye mu zinthu zonse komanso kusunga miyambo imene iye anawapatsa.

Ndi zofunika kudziwa mfundo imeneyi: iwo sanangosunga miyamboyo koma anasunga monga iye anawapatsira.

Palibe kusintha kulikonse kumene kumachitika pa chikhalidwe, chigawo, kapena chilankhulo kapenanso kusiyana kwina kulikonse kumene kukhoza kukhalapo, zenizenizo kapena zongolingalira, zimene tikuyenera kusamalira kuti zimenezi zitheke.

Komabe, kwa iwo a ku Korinto, kapena ife a lero, sitinganene kuti tafikapo pa chidziwitso chonse pamene tidakali padziko lino lapansi.

Chomwecho tsiku ndi tsiku Mzimu Woyera amatiphunzitsa zambiri ndi kutipangitsa ife kuchitapo kanthu pa chidziwitso chimenecho (Yoh. 12:17).


Iye akutibweretsa tsopano ku choonadi cha Mutu.

Matupi athu ndi chithunzithunzi chabwino cha choonadi chimenechi.

Matupi amapeza chitsogozo kuchokera ku mutu.

Zimadziwika kulikonse kuti bungwe silingapite patsogolo popanda bwana wamkulu (mutu).

Komabe choonadi cha mutu ndi chimodzi mwa choonadi chimene chakhala chikuponderezedwa kawirikawiri pakati pa okhulupilira lerolinoNgakhale pali chisokonezo motsutsana ndi choonadi chimenechi, Mulungu akadakonda ife titadziwa kuti mutu wa munthu wina aliyense ndi Khristu; mutu wa mkazi aliyense ndi mwamuna ndipo mutu wa Khristu ndi Mulungu.

Zimenezi zili chomwechi, ndipo sizikufunika kuti tidzisutsana, tidzikambirana kapena tidzikonzenso.

Ena amanena kuti Agal. 3:28 imatsutsana ndi choonadi chimenechi ndipo ena amapezerapo chifukwa chabodza kuti asagwiritse ntchito choonadichi.


Koma tikawerenga mosamalitsa ndime zonse ziwiri monga momwe zilili malingaliro oterewa amachoka.10

Mutu wa munthu wina aliyense ndi Khristu.

Mlengi anatenga malo mwa umunthu.

Masiku Ake padziko lapansi lino Iye anaonetsera chimene munthu anayenera kukhala pa Mulungu.
Iye anatenga chitsogozo tsiku ndi tsiku, inde nyengo iliyonse kuchokera kwa Mulungu (Yoh. 4:34; 5:30; 6:38).

Umboni Wake, “ndichita ine zimene zimkondweretsa Iye nthawi zonse” (Yoh. 8:29) ndipo iye sanachite zosemphana.

Tsopano pokhala analawa “imfa m’malo mwa munthu aliyense” (Aheb. 2:9), nakonzeka kotheratu, Iye anakhala “chipulumutso chosatha” (Aheb. 5:9).

Iye ndi Mkhalapakati (1 Tim. 2:5) ndipo ndi Mutu wa munthu aliyense.

Kaya munthu avomereze kapena akane palibe chimene chikhoza kusintha.

Iye ali wokonzeka, wofunitsitsa komanso wakutha kupereka chitsogozo choyenelera kwa munthu wina aliyense.

Mutu wa mkazi aliyense ndi mwamuna.

Limeneli ndi dongosolo la dziko lapansi, lokhadzikitsidwa mwa chilengedwe ndi Mlengi.

Palibe mlingo wa mafunso, mtsutso kapena chiweruzo umene ukhoza kusintha mfundo imeneyi.

Kunena kuti anthu anagwiritsa ntchito choonadi chimenechi kukabweretsa chisokonezo pakati pa mitundu sitingakane, koma tonse timadziwabe kuti kugwiritsa moipa kapena kuononga kwa chinthu sikumapangitsa chithucho kukhala choopsa.11

Mutu wa Khristu ndi Mulungu.

Munthu wodalira amene anaikidwa pamwamba kuposa m’mwamba ndi Munthu wodalira yemweyo amene akudikira chitsogozo cha Mulungu mu zonse (Marko 13:32 mpaka mtsogolo).

Palibe kusagwirizana, kapena mtsutso kumwamba okhudza zimenezi, kapenanso malo a mtsutso pa zimenezi padziko lapansi lino.

Mutu wa Khristu ndi Mulungu.

Kutengera pa zimene Mulungu anakhazikitsa, mwamuna akaphimba mutu wake pamene akupemphera (kulankhula ndi Mulungu), kapenanso kunenera (kulankhula ndi Mulungu), iye amanyozetsa Khristu Mutu wake.

Iye amachititsa manyazi pagulu Khristu, Mutu wake.

Kaya pakhala chiphaliwali kuchokera kumwamba kapena ayi kutsimikizira za zimenezi zikhala zosafunikira.

Mau a Mulungu anatsimikizira za zimenezi ndipo akuthetsa zonse.

Mosemphana, mkazi amene ali ndi mutu wosaphimba mu zochitika za uzimu zotere amanyozetsa mwamuna (mutu wake).12


Mkumano uli ndi zabwino zoonekeratu ziwiri.

Umapangitsa kudziwika kwa angelo m’mwambamo “nzeru ya mitundu mitundu ya Mulungu” (Aef. 3:10).

Umaonetseranso ulemelero wa Khristu kwa anthu padziko lapansi pamene udzipereka ku Mau a Mulungu.

Ulemu waukulu umene Mulungu Anaika pa ife amene timakonza mkumano!

Mwayi waukulu umenewu kwa zolengedwa zofooka za mu fumbi.

Chipambano chachikulu cha Mulungu kuti Iye akatipange chionetsero cha Ulemelero ife amene kale tinali adani a Mulungu posalekerera chilengedwe Chake, chilungamo Chake kapena ulemu Wake.

Umboni wotani wa ntchito komanso kukwezedwa kwa Khristu, kuti Iye akuikidwa mu ulemu pa malo pomwepo pamene iye ananyozedwa kosaneneka.

Lilemekezeke Dzina Lake la ulemu kwamuyaya.

Pamene mlongo aganiza kuti kuphimba kumutu kukutanthauza pamene “asonkhana pamodzi”, akuyenera kudziwa kuti palibe gawo limene limafotokoza kuti Mzimu Woyera akulankhula za nthawi ya misonkhano ya mkumano yokha.

Ifetu tiona mbali ya misonkhano ya mkumano mu gawo lotsatira.

Ayi ndithu, akutanthauza nthawi zonse.

Ulemelero umene unasokonezedwa ukuyenera nthawi zonse kuphimbidwa ndipo ulemelero wa Khristu ukuyenera kuonetsedwa.

Ngati mlongo aumilira, Mau akulankhula momveka bwino: “asengedwe” –kusiyana kumene kunaperekedwa kwa mkazi wolakwira.

Kupambana pamenepa, Mzimu akufotokoza za chigamulo cha chilengedwe kuti tsitsi lalitali ndi lokopa kwa mkazi ndipo ndi zochititsa manyazi kwa mkazi kusengedwa.

Chifukwa cha chimenechi, iye akuyenera kutsatira Mau a Mulungu.

Angelo akuona ndipo akuphunzira kuchoka kwa ife.

Mwai wukulu wotani umenewu komanso udindo wodabwitsa.

Ndi kofunika kumvetsetsa kuti malingaliro a munthu alibe phindu mu chikonzero cha Mulungu.

Zimene tikuona pano ndi chithunzithunzi cha Khristu ndi Mkumano mwa mwamuna ndi mkazi.

Monga Mpingo uli pansi pa Khristu, chomwechonso mkazi ali pansi pa mwamuna ndipo amaonetsera zimenezi pamene aphimba kumutu kwake.

Chikhalidwe kapena chitukuko sizingasinthe kanthu pa zimene Mulungu ananena, pakuti “Mau Ake aikika kumwamba” (Mas. 119:89).

Chomwecho timaphunzira choonadi cha mutu ndi kuphimba kumutu mogwirizana ndi ndondomeko ya Mulungu, komanso mogwirizana ndi angelo.

Kuphatikizira pa zimene Mzimu watiphunzitsa kukhudzana ndi munthu, Iye akupangitsa maziko a chiphunzitsochi kukhala chodziwika.

Mulungu analenga mkazi kuchokera ku mthiti ya mwamuna komanso iye analengedwera mwamuna.

Kodi zimenezi zikumupangitsa kutsitsidwa kukhala malo a pansi?

Ayi ndithu sichoncho, pakuti iye ali ndi udindo wapadera kupitiliza mtundu kuti ukhalepobe.

Kodi nanga kufunikira kwa tsitsi lalitali ndi kotani?

Linaperekedwa kwa mkazi m’malo mwa chophimba ku nkhope (velo).

Chimenechi ndi chisonyezo cha kumvera kwake ku Mau a Mulungu komanso ku mutu wake.

Pamene akuvomereza, iwo amatsutsana ndi choonadi chimenechi mu Chikhristu tsiku ndi tsiku.

Mfundo yakuti iwo akutsutsidwa, imapereka mphamvu yaikulu ku mfundo ya Mzimu, “Koma akaoneka wina ngati wotetana, tilibe makhalidwe otere, kapena ife, kapena Eklesia wa Mulungu” (ndime 16).

Mzimu Woyera pakuyembekezera za kusagwirizana kumene kukhoza kubwera akutipatsa chenjezo limeneli.

Pakuti chikhalidwe cha umunthu (thupi komanso malingaliro a umunthu) zimene zinalipo nthawi imeneyo sizikusiyana ndi zomwe zilipo tsopano.

Ndi zofunika kudziwa zimenezi, pakuti zolembedwa m’kalata imeneyi kwa Akorinto ndi zofunikira kwambiri kwa okhulupilira a mnyengo zonse.

11:17-34 Umbuye Kuonekera pa Madyerero Oyenera a Mgonero wa Ambuye

Atawayamikira iwo pachiyambi zokhudza chikumbutso chawo pa Paulo, Mzimu Woyera tsopano akuwakonza iwo pa chikhalidwe chawo mu mkumano.

Komanso Iye akuwaonetsera umunthu wawo umene umaonekera pamene iwo a kusonkhana pamodzi.13

Mwatsoka misonkhano yawo ya mkumano inali yosalongosoka kotero kuti imatsimikizira za kupezeka kwa timagulu pakati pawo.

Zimene Mzimu Woyera anafotokoza ngati chifuniro cholunjika cha Mulungu kwa iwo (1:10), chinaponderezedwa ndi kukanidwa ndi gulu kotero kuti Iye anavomereza magawano pakati pawo.

Iwo analephera kugwadira ku chifuniro Chake cholunjika ndipo tsopano akuvutika ndi zotsatira za chifuniro Chake cha ufulu (onani Mas. 106:15).

Chifukwa chiyani Mulungu amavomereza nyengo ngati imeneyi?

Zili chomwechi cholinga kuti iwo amene avomerezedwa tsopano awonekere poyera.

Kodi amenewa ndi omwe Mulungu anawavomereza?

Mfundo ya mu Mach. 13:1-4 ikuti ayi.

Komatu ali iwo amene ndi atsogoleri a timagulu tosiyanasiyana mwina owonetsedwa poyera mu chikhumbokhumbo chawo chofuna kukhala pamalo apamwamba.

Zotsatira zomvetsa chisoni za moyo wakuthupi wotere ndi chisokonezo.

Pamene abwera pamodzi, iwo sangathe kudya Mgonero wa Ambuye.

Iwo akhoza kudya mgonero waowao komanso maphwando a chikondi, pakuti amenewa ndiwo maphwando ofunikira kwambiri m’malingaliro mwawo.

Chisonyezo china cha umunthu wao chikuonetsedwa.

Kudzikonda kumalamulira kufika pa mlingo wakuti ena amadya ndi kumwa kufikira kuledzera, ndipo ena ali nazo zochepa kapena alibe kena kalikonse ndipo ali ndi njala.

Chisonyezo chodzikonda cha dala chimenechi komanso kupeputsa tanthauzo lenileni la mgonero, kumadzetsa kutsutsidwa kwakukulu.

Iwo akuyenera kudya ku makomo awo.

Pakutero asanyazitse Mkumano wa Mulungu kapena kuchititsa manyazi osawuka.

Pakuti chimene Mgonero umaimira monga mwa Mutu 10 chanyozeredwa.

Khalidwe limeneli likuyenera kudzudzulidwa kotheratu.

Nanga machitidwe athu pamene tibwera pamodzi kunyema mkate?

Chidwi tsopano chalunjika pa kukhazikitsidwa kwa Mgonero wa Ambuye.14

Paulo analandira vumbulutso la payekha lokhudza Mgonero kuchokera kwa Ambuye wokwezedwa, zimene zikugwirizana ndi zochitika ku Mauthenga.

Mkate wonyemedwa ndicho chizindikiro cha thupi la Ambuye loperekedwa chifukwa cha Iye mwini; chikho, mwazi wake wokhetsedwa kuombola machimo athu.

Pakuti pa chizindikiro chilichonse Iye akuyamika komanso kufunitsitsa kuti chichitike pakukumbukira Iye.

Mlingo wina owonjezera ukuoneka, okhudza umboni, “kulengeza imfa ya Ambuye”.

Pakunyema mkate Mkumano umapereka umboni kudziko lapansi za kulumikizana kwake ndi Ambuye amene anafa.

Angelo kumwambako nawonso amaphunzira za tanthauzo la imfa ya Khristu ndipo Atate amakhutitsidwa pamene tigawana malingaliro ofanana ndi Iye pokhudzana ndi kukondwera kwake mwa Mwana Wake.

Pakuti imfa ndi kuuka kwa Ambuye wathu Yesu kumatibweretsera ife ubale wina watsopano ndi Mulungu, osangoti monga Mulungu komanso monga Atate (Yoh. 20:17).


Mafunso ochepa angathe tsopano kukhudza malingaliro athu.

Kodi tikuyenera kunyema mkate kangati?

Yankho likhoza kutengera pa zinthu ziwiri: Choyamba, momwe chikhumbokhumbo chathu chikuonekera pofuna kuchitira umboni komanso kudziwika ndi Ambuye amene saoneka.

Palibe lamulo lokhazikika kufotokoza kuti zizichitika tsiku lililonse, sabata iliyonse, mwezi ulionse kapena chaka chilichonse.

Zimenezi zinakhazikitsidwira kwa a Israeli ku Numeri 28.

Mitima ya chikondi, kuzindira za Iye komanso chikondi Chake pa ife zimatipangitsa kukhala ndi nthawi ya kuganizira za Iye, ndi Iye kupezeka pakati pathu.

Kuonjezera apa, pali ndondomeko imene inaikidwa ku Machitidwe 20:7.

Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate.”

Masiku asanu ndi limodzi amakonza uthunthu wa nthawi, kuganizira kuti tsiku la Ambuye ndi pothera komanso malo onyamukira.

Ndi mpata wabwino wobweretsera “mitanga yathu yodzadza”, komanso mpata wabwino woyamba sabata ndi malingaliro atsopano a Ambuye wathu wodalitsika.

Funso lotsatira likugwirizana ndi momwe tikuyenera kupitirizira kunyema mkate.

Kodi tikuyenera kuleka pamene tikumva kutero?

Umboni ndi wakuti “Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye” (ndime 26).

Mapeto athu a kunyema mkate ndiko kubweranso kwa Ambuye, mwina lero.

Zimenezi zimabweretsa funso lachitatu komanso kulingalira mozama, kumene kuli kofunikira kwa onse amene amanyema mkate pafupipafupi ndi iwo amene sanyema mkate.

Kudya monga umo amadyera Akorinto ndiko kosasamala komanso kwa chipongwe.

Kulephera kulumikiza kumeneku pa kudya komanso kumwa kwathu ndi thupi komanso mwazi wa Ambuye zidzabweretsa dzanja Lake kuti atilange ife.

Chomwecho wokhulupilira aliyense akufunika kudziyesa yekha.

Kodi tikuyenera kukhala amantha kudya Mgonero?

Iwo amene sanyema mkate akuyenera kukumbutsidwa kuti pempho likuchokera kwa Iye amene ali Ambuye.

Chotero ife tonse sitikuyenera kuopa kudya, koma tikuyenera kudzipima bwino ndi kudya.

Imeneyi ndi ntchito ya munthu payekha, koma ndi yofunikira kwambiri.

Zochitika ku Korinto zikuonetsera kusoweka kwa kudzipima okha ndipo zotsatira zake ndi zoopsa.

Pali zotsatira za uchimo, matenda komanso imfa.

Pa chikondi Chake kwa oyera mtima Ake, Mulungu sangawalole iwo kunyozetsa dzina Lake osawalanga.

Dzanja Lake la chilango limachita mwa chikondi kuti pasapezeke m’modzi Wake kutsutsidwa ndi dziko lapansi.

Aliyense wa ife akuyenera kusamalitsa!

Mzimu wa Mulungu ukumaliza gawo limeneli ndi zinthu ziwiri zofunika kuganizira.

Choyamba, Iye akuomba mkota pa kufunikira kwa kudekha ndi chikondi pakati pa oyera mtima: “posonkhanira kudya lindanani” (ndime 33).

Iwo amene anali ndi njala amalimbikitsidwa kudya kunyumba kuopa kunyazitsa dzina la Ambuye ndi kubweretsa dzanja Lake ku chilango pa iwo.

Chachiwiri, Iye akulankhula za kukhazikitsa ena onse m’malo mwawo pamene mtumwi adzafika.

Zimenezi zikupereka lingaliro lakuti panali zinthu zina zimene zinali zofunika ku Korinto nthawi imeneyo ndipo sizinayenera kulembedwera kwa oyera mtima a nthawi zonse.

Zimenezi zikupereka kukhazikika kwa mzimu komanso mphamvu ya kalata imeneyi (1:2).

Kaya ndi nkhani yokhudza munthu payekha kapena kuvuta kwa chilengedwe sakufotokozera.

Chodziwika ndi chakuti Mzimu anafuna kuti Mtumwi ayitenge nkhaniyi mwachinsinsi.

Zimenezi zikuphunzitsa kuti kukhala pansi pa Umbuye wa Khristu ndi kudalira pa chitsogozo cha Mzimu Woyera ndi zoonadi zake kotero kuti m’Mau a Mulungu mulibe lemba lakufa.

Chimenechi ndi chisonyezo chenicheni cha Kuuziridwa kwa Malembo Woyera.

GAWO 6 12:1- 14: 40 UNSEMBE WA CHIFUMUKUONETSEDWA KWA MPHAMVU YA MZIMU

12:1-3 Mzimu Woyera Amalimbikitsa

Si oyera mtima onse a ku Korinto amatenga kuonetsedwa kwa mphamvu ya Mzimu pakati pawo kukhala zachibwana.

Ena amaoneka kuti amapempha thandizo pokhudzana ndi zinthu zimenezi (Onani 7:1; 8:1).

Chotero Mzimu Woyera amafunitsitsa kuwaphunzitsa iwo mfundo zochepa za kuonekera kwa mphamvu ya Mzimu Woyera pakati pa okhulupilira.

Amitundu enieni a oyera mtima ku Korinto anawaonetsera iwo ku kupembedza mafano.

Zimenezi zinawatengera iwo pansi pa mphamvu ya ziwanda.


Posautsika ndi zimenezi, ambiri ndi okaikira ndi kuonekera kwa mphamvu yoonekera mu mkumano.

Kodi ndi mphamvu ya ndani imene ikuonekera pamenepa?

Pakuthandiza iwo ndi ife tomwe, Mzimu Woyera akupereka milingo iwiri yosavuta yokhazikika imene tikuyenera kuweruza chiyambi cha umboni wooneka mu mkumano.

Munthu wolankhula mwa mphamvu ya Mzimu Woyera sangathe kulankhula, “thembelero pa Yesu”.

Malankhulidwe otere alibe chiyambi mwa Mzimu Woyera.

Mosemphana, palibe amene angathe kudziwa Yesu Khristu ngati Ambuye pokhapokha mwa Mzimu Woyera.

Mzimu Woyera ndi chiyambi cha umboni ulionse woyenera kwa Ambuye Yesu Khristu ndipo okhulupilira aliyense akhoza kupeza chiyambi komanso chikhalidwe cha mboni ina iliyonse.

12:4-11 Chiyambi ndi Ntchito ya Utumiki.

Titazindikira za mphamvu ndi chiyambi cha utumiki weniweni, Mzimu Woyera akutenga mitundu yosiyanasiyana ya ma utumiki mu Mkumano.

Choyamba, Mulungu anasankha kudzionetsera kudzera mu mphatso zimenezi kuti mphamvu ndi za Mzimu yemweyo.15

Chachiwiri, ma utumiki operekedwa osiyana koma ndi Ambuye yemweyo amene amatsogolera.

Potsiriza, zotsatira zake ndi kagwiridwe kake ndi zosiyana, koma ndi Mulungu yemweyo amene amabweretsa zotsatira m’miyoyo.

Chomwecho, mphatso zosiyanasiyana zimagwiritsidwa bwino ntchito mu mphamvu ya Mzimu Woyera; mautumiki osiyanasiyana amangoperekedwa ndi chitsogozo cha Ambuye komanso ntchito yeniyeni yochitika m’miyoyo ndi machitachita a Mulungu payekha.

Kodi malingaliro amenewa ndi machitachita a Mulungu amenewa achotsedwa motani pakati pa Akhristu lerolino.

Pamenepa, nzeru za munthu ndi maphunziro zikutenga malo.

Kutumikira, munthu akuyenera kudzodzedwa ndi kukhazikitsidwa ndi ulamuliro wa munthu.

Machitachita onse amaonekera ndi ulamuliro wa malingaliro a munthu, mu nyimbo, nyumba zopemphelera zabwino, mabungwe okhazikitsidwa, amene amatsogozedwa ndi zokhumba za mphamvu za umunthu.

Pamenepa pakuonetsedwa kusiyana kwa malingaliro a Mulungu: chokhumba choyamba chokhacho ndicho mphamvu komanso kupezeka kwa Mzimu Woyera.

Mulungu akutsogolera choonadi chonse cha utumiki, komanso Mulungu amachita ntchito yeniyeni m’miyoyo.

Munthu wa umulungu amasamalira utumiki m’malo mwa Mulungu.

Kuonjezera pamenepa, Mzimu Woyera samatanganidwitsa aliyense ndi mphatso Zake zosiyanasiyana zopezeka mwa munthu.

Wina akhoza kupatsidwa zingapo, koma munthu aliyense amalandira.

Cholinga ndicho kupindulira onse.

Nzeru (kupeza malingaliro a Mulungu) ndi chidziwitso (kukhala ndi Mau ovumbulutsidwa m’malingaliro ndi mu mtima) zonsezi zimatipangitsa chidwi chathu kukhala pa Khristu (Akol. 2:3), cholinga kuti kuonetsedwa kwa Mzimu Woyera kuli ndi Khristu ngati poikapo chidwi chathu (Yohane 16:13, 14).

Chikhulupiliro pamenepa sakukamba za chikhulupiliro chopulumutsa pakuti okhulupilira onse akuyenera kukhala ndi chikhulupiliro (Aef. 2:8, 9).

Koma makamaka ndi kulimbika pa Mulungu, kumene kumagwiritsidwa ntchito pa kusamalira ena.

Yoswa anaonetsera zimenezi pamene amalimbana ndi adani a Mulungu (Yos. 10:12 mpaka mtsogolo).

Kuchokera mu zochitika zooneka mu mkumano mwao, chisonyezo cha mphatso, mphatso ya machiritso komanso magwiritsidwe ntchito a zozizwa zimalandira ulemu waukulu pakati pa oyera mtima a ku Korinto.

Kuti zimenezi zigwire ntchito, komanso zosintha zopezeka pamenepa zingathe kukhala zoseketsa komanso zosavuta kukumbukira.

Uneneri sivumbulutso lokha la zochitika mtsogolo komanso vumbulutso la malingaliro a Mulungu nthawi imeneyo kutsutsa mitima ndi chikumbumtima cha oyera mtima.

Pamenepa vumbulutso limeneli ndi lofunika kwambiri, pakuti Chipangano Chatsopano chonse chinali chisanaonetsedwe.

Kuyesa mizimu ndiwo mlingo wa uzimu kudziwa zimene zili mu utumiki ulionse kuti zikuchokeradi kwa Mulungu.

Mitundu ya malilime –chisonyezo cha mphatso chimene chimaonetsera zilankhulo zosiyanasiyana, za nzeru kwa ena, koma zosadziwika kwa wolankhulayo.16

Kutanthauzira kwa malilime kumatanthauza kupangitsa zimene zanenedwa kuti zimveke bwino.

Zimenezi komanso mphatso ya malilime zakambidwa pa Mutu 14.

Chodziwika bwino ndi chakuti Mzimu Woyera ndi amene amapereka mphatso zimenezi kwa anthu, ndipo amagwiritsa ntchito iwo amene Iye wawapatsa mphamvu monga mwa kufuna Kwake.

Iwo amagwira ntchito pamodzi monga ziwalo zofunikira pa thupi kuti wina apindule.17

Ndi kofunika kuona kuti pali mphatso zimenezi zokwanira zisanu ndi zinayi zimene zafotokozedwa, zimene zikutipatsa malingaliro pa magawo asanu ndi anayi a chipatso cha Mzimu (Agal. 5:22, 23).

Pamenepanso, ndi mphamvu ya Mzimu Woyera imene imakonza chipatso chimenechi.

12:12-21 Sukulu ya Ukachenjede ya Mulungu

Pa kufufuza kwawo mu umodzi pa kusiyana kwa zinthu ndi kusiyana kwa zinthu mu umodzi, akachenjede anabwera ndi malingaliro a sukulu ya ukachenjede.

Komabe iwo analephera mu kufufuza kwawo, pakuti sukulu zawo za ukachenjede mwa chinsinsi zinayamba kusula akatswiri.

Iwo samavomereza za zinthu zambiri zosiyanasiyana.

Pamwamba pa zimenezi iwo sanakwanitse kuonetsera umodzi mu kusiyana kwa zinthu, pakuti pamene chidziwitso chinachuluka, munthu anaganiza zotulutsa anthu ena ofanana ndi iye, kapenanso kuchotsa onse amene akutsutsana nawo.

Mulungu ali ndi sukulu yake ya ukachenjede.

Mzimu Woyera akutionetsa ife chitsanzo ndipo mu chitsanzo chimenechi muli ubwino wa ntchito ya Mzimu.

Machitidwe 2:2-46 akutionetsa umodzi mu zinthu zambiri zosiyanasiyana pamene Mzimu akugwira ntchito.

Machitidwe 13:1-4 akutionetsa zinthu zambiri zosiyana mu umodzi pamene Mzimu akugwira ntchito.

Thupi la munthu likusonyezedwa ngati thupi la Khristu ndipo lili ngati chitsanzo pamene likugwira ntchito.

Limeneli ndi thupi limodzi (umodzi) lokhala nazo ziwalo zambiri (zinthu zambiri zosiyanasiyana).

Ngakhale lili ndi ziwalo zambiri (zinthu zambiri zosiyanasiyana), ziwalo zambiri zimenezi ndi thupi limodzi (umodzi).


Chomwecho, monga thupi la munthu ndi umodzi mu zinthu zambiri ndipo zinthu zambiri mu umodzi, chomwechonso Khristu, thupi la okhulupilira.

Mulungu anabweretsa zimenezi mu njira ya pamwamba.

Gulu labatizidwa mu thupi LIMODZI (Mach. 2) posatengera fuko kapena udindo wa kudera.

Kuonjezera pamenepa, munthu aliyense anapangidwa kukhala wotenga nawo gawo wa Mzimu m’modzi.

Mobwereza malingaliro a umodzi mu zinthu zambiri zosiyanasiyana komanso zinthu zambiri zosiyanasiyana mu umodzi zaikidwa pa ife.

Tsopano Mzimu Woyera akufotokozera za malingaliro alionse ndi chithunzithunzi chochokera mu thupi la munthu.

Thupi (umodzi) lili ndi ziwalo zambiri (zinthu zambiri zosiyanasiyana).

Ngati phazi (kuyenda) lidandaula chifukwa sidzanja (ntchito), kodi ndiye kuti ilo silofunika mu thupi?


Ntchito yopanda kuyendamo mu ntchitoyo ndi chinyengo cha “chitani monga ndikunenera osati monga ndikuchitira”

Zoonadi, ngati khutu (kumva Mau a Mulungu) lidandaula kuti si diso (kuona mwa chikhulupiliro), kodi silofunika mu thupi?

Kumva koma osaona mwa chikhulupiliro ndiko kulandira gawo chabe la uthenga (Yes. 30:20, 21; 53:1).

Chikhulupiliro chopanda Mau a Mulungu kutitsogolera ndiko kungodzionetsera chabe.

Chiwalo chilichonse cha thupi ndi chofunika; diso (chikhulupiliro), khutu (kumva Mau) komanso kununkhiza (chidziwitso) zonsezi ndi zofunika mu thupi limene likugwira bwino ntchito.

Chomwecho, kudzichepsa wekha pa kagwiridwe ntchito mu thupi la Khristu ndi kuyamba kusilira wina kumeneku ndi kudzidelera, ndipo zimabweretsa nsanje ndipo ndi chipongwe kwa Mulungu.

Mulungu, amene ndi mlengi wa thupi la munthu (Gen. 2:22) alinso mlengi wa thupi la Khristu.

Mwa kukula kwa nzeru zake Iye anaika ziwalo zosiyanasiyana mthupi monga mwa kusangalatsidwa kwake kuti atero.

Ziwalo zonse za thupi zikanakhala chiwalo chimodzi komanso chofanana, thupi silikanakhalapo.

Tsopano akufotokoza za lingaliro lachiwiri, la zinthu zambiri mu umodzi, pakuti ngakhale pali ziwalo zosiyana komabe pali thupi limodzi.

Chomwecho diso (kuona mwa chikhulupiliro) silingakanize dzanja (ntchito), pakuti “chikhulupiliro chopanda ntchito chili chakufa” (Yak. 2:26).

Kuonjezera pamenepa, mutu (chitsogozo) sungakanize phazi (kuyenda).

Chitsogozo chimene chaperekedwa koma osachitika chimabweretsa kukhumudwa.

Chomwecho, kunyozetsa ntchito ya ena kumatsogolera ku kuchititsidwa manyazi chimene ndi chipongwe kwa Mulungu.

Thupi la munthu limachita bwino chifukwa cha chisamaliro choonetsedwa ndi ziwalo.

Chimodzimodzinso thupi la Khristu.


Chotero iwo amene ali olimba akuyenera “kunyamula zofooka za opanda mphamvu” (Aroma 15:1), “yense ayese amzake omposa iye mwini” (Afil. 2:3).

Ntchito ya manja a Mulungu inaika thupi pamodzi kuti likhale labwino kwathunthu.

Pamene chiwalo china, kaya ndi cholemekezeka, cholimba kapena chokongola, chimagwira ntchito pamodzi ndi china chimene ndi chosemphana nacho, thupi lonse limakhala la thanzi, losakhala nako kusagwirizana, koma chiwalo chilichonse kuthandizira ndi kusamalira china.

Pamene pali kuvutika kuthandizana komanso kusamalirana kumakhalapo.

Pamene pali chimwemwe, onse amakondwera.

Chithunzithunzi chodabwitsa cha Mkumano ndi thupi la munthu.

Tsopano kwa oyera mtima a ku Korinto Iye akunena, “koma inu ndinu thupi la Khristu” (ndime 27)

Iwo ndi chisonyezo cha Mkumano ku dela limenelo.18

Oyera mtima ku mkumano wa kudela amapanga kagawo kochepa ka Mkumano wa Mulungu.

Pano Mzimu Woyera akulankhula zokhudza iwo amene Iye anawaika mu Mkumano pa nkhani za dongosolo komanso kagwiridwe kawo ka ntchito.

Atumwi akupatsidwa koyamba kwa zonse.

Iwo ali ndi ulamuliro wa Mulungu kuyala maziko.

Aneneri ali ndi malingaliro a Mulungu ndipo amalankhula ku mtima komanso chikumbumtima cha oyera mtima.

Kenako aphunzitsi ali ndi Mau a Mulungu ndipo amalankhula mwa kuwamvetsetsa.

Monga mwa kuperekedwa kwa ndondomeko imeneyi, iwo amapanga Mkumano wa Mulungu mwa mphamvu ya Mzimu wa Mulungu.

Zozizwa ndi machiritso zimatsatira monga chizindikiro choyamba kwa iwo amene ali osapulumutsidwa.

Thandizo lingathe kuoneka losafunika koma ndi kofunika kudziwa kuti dzina la ‘Ezara’ limatanthauza kuti thandizo ndipo timadziwa kuti ntchito imene iye anachita pakati pa iwo obwenzeretsedwa a Chiyuda inali yofunikira.

Kudzichepetsa ndi kofunikira pamaso pa Mulungu.

Kaya thandizo libwere motani kwa ogwira ntchito, thandizolo limakhala lopanda phindu.

Maboma amatchula iwo amene amagwira ntchito pakati pa oyera mtima m’njira ya umulungu.

Kuchuluka kwa malilime kwathetsedwa.

Zimenezi zikuonetsa kuti mphatso yomweyo, imene Akorinto akuthupi anaiyika pamwamba, Mulungu waiyika pamalo otsika.

Mafunso osiyanasiyana ochuluka amene amatsatira, akuyenera onse kuyankhidwa mowatsutsa.

Mzimu Woyera akutsindika kuti umodzi mu zinthu zosiyanasiya zochuluka komanso zinthu zosiyanasiyana zochuluka mu umodzi zimapezeka pamene Mzimu Woyera ndi Mtsogoleri, mu sukulu ya ukachenjede ya Mulungu.

Mkumano sigulu la mitsutso, kapena kuonetsera kukula kwa mphatso, kapenanso kuti ndi gulu loyambika chifukwa cha kugwirizana pa mfundo imodzi.

Iye akutilimbikitsa ife kufunitsitsa mphatso yabwino yogwiritsira ntchito kwa oyera mtima a Mulungu kulikonse kumene alili.

Kuti tikhale aphindu tikuyenera kulimbikitsidwa ndi chikondi cha Mulungu, chimene nthawi zonse chimaloza kumwamba kwa Mulungu komanso kunja kwa anthu ake (Aroma 5:5).

Mu Mkumano, Malamulo a Chikondi cha Kumwamba

13:1-3 Popanda Chikondi, Pali Chabe

Powonetsera “njira ya kuchita bwino kwambiri”, Mzimu Woyera akuonetsera bwino lomwe kuti chikondi cha Mulungu chikuyerena kufalikira pa zonse.

Iye amaonetsera zimene ndikunena, zimene ndili nazo ndipo zimene ndimachita zili chabe popanda chikondi cha umulungu.

Malo opempherera, kaya pansi pano kapena nyengo ya kumwamba, afanana ndi nguli yolilitsa ngati chikondi chikusoweka.

Iye amene ali ndi mphatso ya uneneri, namvetsetsa zinsinsi zonse ndipo ali nacho chikhulupiliro chachikulu amatsitsidwa kukhala wopanda pake komanso wodzikonda, ngati zimenezi sizikuchitika mwa chikondi cha Mulungu.


Kuonjezera apa, popanda chikondi cha umulungu, machitachita athu a chikondi amangokhalabe chionetsero chabe, -kaya ndi munthu amene amapereka chuma chake kwa osowa, kapenanso munthu amene amapereka moyo wake pa chifukwa china chake.

Zimenezi zimakhala zokhumudwitsa ku thupi la munthu.

Mwazotsatira zake zimene akulankhula kwa oyera mtima ku Korinto amene anaperewera mu mphatso (1:7), koma amene machitidwe awo pa kunyema mkate akuonetsa mochepa chikondi cha Mulungu (11:20-22).

Akulankhula mokakamiza kwa ife monga okhulupilira a lero.

Kodi ife timatsogozedwa ndi Ambuye kuti mau athu, chuma chathu ndi machitidwe athu zimaonetsera kuti chikondi cha Mulungu chatsanulidwa m’mitima mwathu?

Kodi kuvomera kwathu ndi zotsatira zenizeni za kutsogozedwa kwa chikondi cha Mulungu?

13:4-7 Chikondi ndi Machitachita

Momwe chikondi chimadzionetsera chokha chimatipangitsa ife kudziwa momwe chikondicho chinachotsedwera ku thupi ndi machitachita a thupilo.

Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima.

Chikondi sichitsatira zimene zili za anthu ena.

Chikondi sichichita chipongwe (kusalemekeza), kapena nkhanza (mavuvu).

Chikondi sichifooka (kudzala ndi zokomera tokha).


Chikondi sichimachita zinthu munjira yosayenera; sichimanyoza ndi kuchita chipongwe.

Sichitsata za mwini yekha, koma chitsata zimene zili zabwino kwa ena.

Chikondi sichipsa mtima pakuti chilibe khungu lochepa monga thupi lili.19

Chikondi sichimaimira zoipa; sichimakhala ndi malingaliro oipa, chinthu chimene thupi limachita mwachangu.

Kupeza choipa sichinthu chimene chikondi chimakondwera kuchita.

Motsutsana, chikondi chimakondwera mu choonadi.

Chikondi chimakwilira zinthu zonse, sichimakwiya.

Sichidzikonda kapena kukayikira, Chikondi chimakhulupilira zinthu zonse.

Chikondi chimadziwa “kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake” (Aroma 8:28), chimayembekezera zinthu zonse.

Pomaliza Chikondi chimapilira zinthu zonse chifukwa ndi cha Mulungu, chimadziwa Iye amene ali “Mtsogoleri ndi Wotsiridzitsa” (Aheb. 12:2), “Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza” (Chiv. 1:8, 17).

Chikondi cha umulungu chimasiyana kwambiri ndi machitachita a thupi.

Timaonetsera pang’ono chikondi cha umulunguchi chimene “chinatsanulidwa m’mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife” (Aroma 5:5).

13:8-13 Kukula kwa Chikondi cha Umulungu

Atationetsa momwe chikondi cha umulungu chimadzionetsera chokha, iye akutitsimikizira kuti chikondi choterechi sichimalephera.

Zinthu zambiri zimene timaziona ndi zosakhalitsa, zingakongole bwanji.

Zimenezi zikuphatikizirapo uneneri, malilime ndi chidziwitso.

Uneneri umalangiza (kumangilira), umalimbikitsa (kutakasa) komanso kutonthoza (kulimbikitsa).

Nthawi ikubwera pamene zimenezi sizizafunika.

Chomwechonso malilime, nawo adzaleka pakuti ali pamenepo kukakopa osakhulupilira.20

Chidziwitso chidzatha.

Chifukwa cha kusakhalitsa kumeneku ndi chakuti zinthuzi ndi zosamaliza.

Ife timapeza chidziwitso m’magawo, tsiku lililonse kuonjezera pa zimene tikuzidziwa.

Ife timanenera mu kagawo pakuti Mulungu amavumbulutsira “kuno pang’ono uko pang’ono” (Yes. 28:10).
Komabe nthawi yodalitsika ikuwandikira mwachangu pamene ife tidzakhala pamaso pa Ambuye.


Kenako ife tidzamalizika.

Chikhumbokhumbo cha uneneri, chidziwitso kapena malilime zidzakwanitsidwa.

Kufotokozerabe mfundo imeneyi, ife timakumbutsidwa za chithunzithunzi cha umwana.

Maganizidwe ndi machitidwe a umwana amaonetsa kusakhwima.

Zimene mwana amalankhula zimalinga ku zozungulira dziko lake, zikhoza kukhala pakuona kwake kapena zimene wapeza.

Komabe pamene iye akukula, amasiya zonse zimene zili zachibwana.

Imeneyi ndi ntchito ya kukhwima.

Zonse zimene tili nazo tsopano ndi gawo chabe.

Ife timaona zinthu mu zenera mwa chizimezime.

Kutengera pa kuwala kumene kulipo ndi zosokoneza zoonetsedwa kapena khungu limene limaononga maonedwe athu, ife timaphunzitsidwa ndi zisonyezo kapena zitsanzo.

Koma tsiku lina la ulemerero, chikhumbokhumbo chonse cha Mzimu woyera, zikhumbokhumbo zathu zonse zizadziwika.

Mu tsiku lodabwitsa limeneli kudzakhala “maso ndi maso” (1 Yoh. 3:2, 3).


Chidziwitso cha kagawo chidzachotsedwa ndipo padzakhala chidziwitso chathunthu.

Tsiku la ulemelero

Kwa nthawi ino, zinthu zitatu izi zidzakhalabe: chikhulupiliro –machitidwe amene amafikira m’mwamba, chiyembekezo –machitidwe amene amafikira chitsogolo, komanso chikondi chimene chimafikira m’mbali.

Zonse zinazikika mwa Ambuye ndipo timalandira mphamvu kuchokera kwa Iye kugwiritsidwa ntchito mwa Iye.

Zimenezi zimakhalabe zofunikira pa utumiki.


Koma chopambana pa zonsezi ndi chikondi, chofunika mu utumiki wa Mulungu kumwamba komanso kwa oyera mtima pansi.

Utumiki woyendetsedwa ndi Chikondi cha Umulungu

14:1 Chikondi ndi Chinthu Chofunika Choyambilira

Mafotokozedwe a chikondi cha umulungu mundime yapitayi ikutipatsa chinthu chofunikira kwambiri pamene tikugwiritsa ntchito mphatso.

Titakhazikitsa chinthu chofunika choyambachi, Mzimu Woyera akulimbikitsa oyera mtima kutsatira Chikondi, kupangitsa chikondicho kukhala cholinga cha miyoyo yawo.

Nyengo pakati pa oyera mtima ku Korinto ikuchitira umboni kulira kwa kukhumba chilimbikitso choterechi.

Sikuti ndi zosafunikira pakati pa okhulupilira masiku ano komanso munyengo zino.

Pamene chofunikira choyamba chimenechi chakwaniritsidwa pamakhala chikhumbokhumbo cha kuonekera kwa uzimu pakuti zinaperekedwa kuti zikapindulire tonse (12:7).


Chikondi chimafunitsitsa phindu lotere, ndipo mphatso ya uneneri ndi yaikulu koposa phinduli.

14:2-12 Kumangilira, Cholinga cha Mphatso

Oyera mtima a ku Korinto anatsindika kwambiri mu mphatso za malilime.

Mzimu Woyera anapeza kuti ndi kofunikira kufotokozera mwa tsatanetsatane kwa oyera mtimawa komanso kwa ife, kuti cholinga chachikulu cha mphatso mu Mkumano ndi kumangilira oyera mtima, osati munthu kudzionetsera.

Mphatso ya malilime ndi kuthekera kopatsidwa ndi Mulungu kulankhula mu chilankhulo, osati wolankhulayo kuphunzira kapena kulankhula chilankhulo cha kumene iye anabadwira.21

Imeneyi inali ntchito ya tsiku la Pentekoste (Mach. 2:4-11).

Nyengo ya mu Mkumano ku Korinto inali yophweka, pamene onse moonetsera analankhula chilankhulo chimodzi.

Chotero munthu ngati alankhula chilankhulo china chosadziwika kwa anthu ena onse, iye akulankhula kwa iye yekha komanso kwa Mulungu.

Amamvetsetsa chimene iye akufuna kulankhula, ndipo Mulungu amamvetsetsa zimene iye walankhula.

Mzimu Wake amalankhula zinthu zobisika.

Komabe iye amene amanenera amalankhula kwa anthu mu chilankhulo chimene iwo akuchimvetsa bwino ndi mfundo zitatu izi: kumangilira –kumanga pamodzi monga mwa nthawi ino; kulimbikitsa –kutakasa monga mwa mtsogolo komanso kutonthoza –chitonthozo monga mwa kale.

Mwachidule, iye amene amalankhula mu chilankhulo china amadzimangilira yekha, koma iye amene amanenera amamangilira Mkumano/Mpingo.

Chikhumbokhumbo chabwino ndi chakuti aliyense agwiritsidwe ntchito mwa Mzimu.

Koma mwa chikhumbokhumbo kuonetsetsa kuti oyera mtima amangililike, mtumwi akadakonda kuti aliyense anenere.

Pachifukwa chimenechi iye amene anenera ali ndi phindu lalikulu ku Mkumano.

Pofananitsa phindu pali mphatso ya malilime imene ili ndi wotanthauzira.

Mkumano umapindula pa kutanthauzirako.

Komane ndi kofunika kukumbukira kuti malilime chinali chizindikiro kwa osakhulupilira.

Pa kutsindika mfundo ya kumangilira, nyengo iyi ikuperekedwa: Kodi phindu lake ndi chiyani kwa oyera mtima ngati Paulo akanalankhula kwa iwo mu chilankhulo chimene iwo sangachimvetsetse?

Palibepo phindu lililonse!

Koma iye akutipatsa mfundo zinayi za utumiki wa phindu umene ukapindulira anthu onse: vumbulutso, chidziwitso, uneneri ndi chiphunzitso.

Vumbulutso limene Mulungu yekha amapereka ndi lofunikira munthu asanayambe kunenera.

Chidziwitso chimabwera munthu asanaphunzitse.

Munthu wina anapeza izi: ‘Sungaphunzitse ngati sukudziwa’.

Kuonjezera apa, zinthu zopanda moyo zimatulutsa mau.

Ngati mau osiyanasiyana sangasiyanitsidwe, ndani amene akhoza kumasulira uthengawo?

Msilikali aliyense amadziwa kuti kulira kwa lipenga kusasokonezedwe cholinga kuti iye akadziwe kutanthauzira uthenga wa lipengalo ndi kuchita moyenera.

Chotero ngati iwo akulankhula sagwiritsa ntchito chilankhulo chomveka bwino, palibe amene apindule ndi uthengawo pakati pawo posatengera kuti akulankhula mosangalatsa.

Pamenepo palibe kulumikizana kwina kulikonse.

Iwo “alankhula kumlengalenga” (1 Akor. 14:9).

Kotero pa chikhumbokhumbo, kuti kupezeka ndi mphamvu ya Mzimu zionekere, zonse zimene zikuchitika zichitike pa kubweretsa phindu la uzimu limene Mulungu akufuna kupereka kwa anthu Ake.

Ifetu tikuchita bwino kuganizira funso limeneli: ndani amene amadziwa lingaliro la Mulungu koma ndi Mzimu wa Mulungu yekha (2:11)?

Chomwecho Iye yekha adzapereka chakudya choyenera cha uzimu kuchokera kwa Mulungu pamene oyera mtima adziperekha okha ku chitsogozo Chake.

14:13-20 Kumanga Osati Kuphwasula

Zotsatira zake, iye amene alankhula mu chilankhulo china apemphere kuti pakhale kutanthauzira.

Kudalirana koonekera kumeneku ndi kofunikira pakuti palibe munthu amene amakhala ndi mphatso zonse.

Pamene Mulungu waloledwa kugwira ntchito ndi Mzimu Wake, Mzimu amene amapereka mphamvu monga mwa kufuna kwake (12:7-11), amagwiritsa ntchito Iye amene afuna.

Palibe utumiki wa munthu m’modzi mu zinthu za Mulungu.

Iye amene apemphera mu chilankhulo china, apemphera mu mzimu.

Ngati achita zimenezi mu mkumano, sizibereka chipatso chilichonse.

Oyera mtima samamangilirika pakuti samamvetsetsa zimene zikunenedwa.

Zoonadi kaya ndi kupemphera kapena kuimba mu mkumano, ife timachita bwino kuzindikira kuti cholinga ndi kumangilira oyera mtima.

Chimenechi sichionetsero; cholinga sikukulitsa zikhumbokhumbo za munthu (thupi).

Mathero amene mtumwi akufikapo ndi umboni wa zimenezi.

Iye amene amalankhula zilankhulo zambiri kuposa onse, akhoza kulankhulako mau asanu amene oyera mtima akhoza kuwamvetsetsa, kuposa kuwavutitsa iwo ndi mau zikwi zikwi amene sangawamvetsetse.

Amenewa ndi mathero a nzeru za uzimu komanso chidziwitso choyeretsedwa.

Komanso zimatsutsa lingaliro lakuti machitidwe mu mkumano ndi danga kwa okhulupilira kuonetsera mphatso zawo ndi luso lawo.22

Machitidwe oterewa ndi chitsanzo cha chikhalidwe cha umwana chimene sichimafuna kudziwika ndi anthu a Mulungu.

Pamene mu chikhumbokhumbo tikuyenera kukhala ngati ana, mu kamvetsedwe tikuyenera kukhala okhwima.

Zomvetsa chisoni pamene abale agwiritsa ntchito mphatso ndi chikhumbokhumbo chopsinja ena.

Machitidwe omvetsa chisoni a thupi amenewa ndi onyozetsa kwa Mulungu ndipo amapsinja Thupi la Khristu.

14:21-25 Mphatso za Malilime

Kutengera zitsanzo zochokera ku Chipangano Chakale (Deut. 28:49; Yes. 28:11, 12), Mzimu Woyera amatsimikizira kuti Mulungu amagwiritsa ntchito zilankhulo zina kukalankhula ku mitima ya osakhulupilira.

Mosiyana, iye amagwiritsa ntchito mau a uneneri kulankhula mitima ndi chikumbumtima cha okhulupilira.

Iye akusonyezera choonadi chimenechi ndi zitsanzo zochitika.

Pamene mu mkumano, okhulupilira aliyense alankhula mu chilankhulo china, osakhulupilira amene abwera pakati pawo awayesa iwo onse kuti ndi amisala.

Zimenezi zimatchinga ntchito yotsimikizika ya Mzimu.

Munjira ina, ngati onse anenera, osakhulupilira amene abwera amatsutsika pa onse.


Iye amabweretsedwa pamaso pa Mulungu, pakukhala ndi malingaliro obisika amenewa obweretsedwa poyera ndi Mzimu Woyera.

Mathero ake ndi odziwika bwino.

Zimene Mulungu amapereka ndi zopindulira mkumano.

Iye amafunitsitsa kuti Mkumano Wake padziko lapansi lino ukadziwike ndi mphamvu Yake.

Mphamvu imeneyi simaonetsedwa kuti ikakwaniritse zokhumba za thupi za wokhulupilira koma kukamanga gulu lonse.

Mwatsoka, ife tikhoza kutchinga kumanga kumeneku pamene sitikutsatira chitsogozo cha Mzimu Woiyera.

Chomwecho tikuyenera kubwera pamodzi mu ufulu wa Mzimu kuti mphamvu Yake ikaonekere mwa kumangilira oyera mtima.

14:26-40 Ndondomeko ya Mulungu lilibe Utumiki wa Munthu M’modzi


Zimakhala bwino pamene wina aliyense ali ndi kenakake.

Umenewu ndi umboni wa zinthu zambiri umene Mzimu Woyera anakonza.

Koma zimenezi zisasanduke kukhala ufulu kwa tonse, pamene aliyense payekha ayesetsa kuti akhale ndi gawo lake.

Ufulu wa Mzimu kenako umasandulika kukhala chiphatso cha thupi.

Pofuna kukonzanso chiphaso cha thupi, ambiri ayesetsa kukonza kalikonse kamene ali nako mwa dongosolo ndi kuiwala chitsogozo cha Mzimu Woyera.

Mzimu Woyera akupereka chitsogozo kwa mkumano pamene ife timatha kulewa nyengo yomvetsa chisoni imeneyi.

Ifetu tikuyenera kutsatira Mau Ake.

Kulankhula pagulu, kaya ndi kulankhula m’chilankhulo chachilendo kapena kunenera, zichitike mopatsana mpata akamaliza wina kwa anthu osapitilira atatu.Imeneyi sinambala yosankhidwa mwa ngozi.

Ikutengedwa mu mfundo ya m’Malemba (Deut. 19:15).

Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu maneno onse adzakhazikika” (2 Akor. 13:1).

Pano pali ndondomeko yokhazikitsidwa ndi Mzimu pa mfundo yodziwika mu Chipangano Chakale.

Ndondomeko imeneyi sinakhazikitsidwe ndi madongosolo a anthu.

Pa nkhani yokhudza zilankhulo za chilendo, pakuyenera kukhala omasulira.

Pakasoweka otanthauzira, munthuyo alankhule pa iye yekha ndi Mulungu.


Kulankhula mwa umunthu, munthu angathe kudziwa kuti pakufunika kutanthauzidwa pamene uthenga waperekedwa.

Nzosangalatsa kudziwa kuti mu mkumano palibe chimene chimadalira maonedwe a munthu kapena kuthekera kwa munthu!


Pamene iye analimbikitsidwa kukhala wodalira (ndime 13), pemphero limene limabweretsa yankho kuchokera kwa Mulungu wathu wakumwamba wodalitsika likuvumbulutsira kupezeka kwa kutanthauzira.

Kunena kuti iye amapatsidwa ufulu wakulankhula ku gulu, kapena kukhala chete.

Ndi mau a uneneri, palinso udindo kwa iwo amene akumvetsera.

Lingaliro lililonse loperekedwa likuyenera kugwirizana ndi mfundo ya m’Malemba.

Iwo a ku Bereya anaonetsera njira (Mach. 17:11).23

Ndi malemba a m’Chipangano Chakale okha amene analipo nthawiyo, Mulungu anagwiritsa ntchito mavumbulutso kulumikiza lingaliro Lake kwa “atumiki Ake aneneri” (Amos 3:7).

Kulankhula mwa umunthu, kodi wolankhula angazindikire bwanji kuti china chake chikuvumhulutsidwa kwa wina amene wakhala pambali pake?

Zimenezi ndi zosavuta kuzindikira.

Pamene wolankhula akupereka zokhazo zimene Mzimu wapereka kwa iye, akuyenera kukhala chete mu nthawi yoyenera.

Kumeneku ndiko kutsogolera kwa Mzimu Woyera kwa iwo amene ali pansi pa Iye.

Kumeneku ndiko kumvera, iye akupereka malo kwa Mzimu Woyera kuti agwiritse ntchito ena.

Mwatsoka thupi limakonda kuti lionekere ndi kumveredwa komanso kudziwika.

Chomwecho tikulimbikitsidwa kulola zinthu zimenezi kuti zichitike, pakuti pamene tikukaniza zimenezi ndipo mwakutero timapsinja ntchito ya Mzimu.

Kuonjezera pamenepa, kuti onse akaphunzire, kuti onse akatonthozedwe, onse akanenere wina akatha mzake kufikira pa mlingo wopatsidwa.

Zimenezi zimapherezera choonadi kuti palibe munthu amene ali ndi mphatso zonse.

Pambali pa izi, tilankhula mau a munthu wina: “atumiki a Mau akuyenera kuti mau atumikiridwenso kwa iwo.”

Kuti wina angakhutitsidwe ndi mphatso zake kapena kujijilika kwake, Mzimu Woyera akuchenjeza kuti mizimu ya aneneri imamvera aneneri.

Zimenezi zikusiyana kwambiri ndi kudzala ndi ziwanda pamene palibe kudzigwira (mau ofanizira Agal. 5:22, 23).


Mwakuyamika timakondwera kuti Mulungu sichiyambi cha chisokonezo.

Akorinto anafunika kukumbutsidwa zambiri za zimenezi chimodzimodzinso ifeyo.

Mtendere mu mikumano yonse umachokera kwa Mulungu.

Mzimu kenako akutenga nkhani ya kagwiridwe ntchito ka akazi mu mikumano.

Mwa chiyembekezo, Mzimu amalumikizitsa mtendere mu mikumano yonse ndi kagwiridwe ntchito ka akazi.


Mu mbiri yonse ya Mkumano padziko lapansi komanso mopitilira palibe kutsutsana kochepa kamene kamabwera pa kagwiridwe ntchito ka akazi.

Lamulo la Israyeli limalamulira mkazi kukhala omvera chimodzimodzinso lamulo la chilengedwe.

M’malo molankhula iwo amayenera kufunsa amuna awo kunyumba, ngati akufuna kuphunzira.

Ngati mkazi alankhula mu mkumano, amenewa ndi manyazi ake.

Nkhani iliyonse imaonedwa motere kufikira tsiku lalero mtumwi Paulo wakhala akulankhulira motsindika komanso kudzudzula mokhudzana ndi izi potengera malemba.

Nzokwanira kunena kuti Mzimu Woyera akuyembekezera kutumphuka kwatsopano kotere pa nkhaniyi.

Chomwecho kaya kutsutsa kulikonse kapena kudandaula kulikonse kumene munthu akhoza kubweretsa, kutsutsana kumeneku kuli ndi Mulungu Mzimu Woyera.

Pakutero, pali mafunso ena ofunikira amene tikuyenera kuwaganizira.

Kodi Mau a Mulungu anayamba pamodzi ndi ndani?

Kodi anayamba pamodzi ndi oyera mtima a ku korinto?

Kodi anafikira oyera mtima a ku Korinto okha?

Kodi nanga Akhristu obwera ku mibadwo yotsatira?

Mauwa sanachokere kwa iwo.
Palibe kukambirana kwina kulikonse pa mauwa kuyambira nthawi imeneyo, lero ngakhale mtsogolomo.

Mzimu amapereka chitsogozo chabwino komanso chophweka.

Aliyense amene amazitenga yekha kukhala wauzimu kapena kukhala mneneri, azindikire kuti chitsogozo chimenechi ndi malamulo a Ambuye.

Amenewa si zipatso za ubongo wa Paulo.

Kukhala wa uzimu, munthu akuyenera kukhala ndi malingaliro a Mzimu.

Kuti akhale mneneri, iye akuyenera kukhala ndi lingaliro la Mulungu.Mwanjira ina iliyonse, iye akuyenera, ndi zina zotere.

Choonadi chokhumudwitsa ndi chakuti iye akhoza kukankhidwa ndi zochitika zatsopano.

Koma kulira kukhale kuti: musapondereze zimene Mzimu wavumbulutsira; musavundikire zimene zikudziwika kuti ndi malingaliro a Mulungu.24

Chomwecho palibe kutsutsana nawo iwo amene amanyalanyaza kapena kukana malamulo a Mulungu.

Alekeni apitilire kukhala mu umbuli umene iwo anasankha.

Pa kuomba mkota, ife tikuyenera kufunitsitsa kunenera –kumangilira oyera mtima.

Ife tisaletse kulankhula m’malilime, kulengeza uthenga wabwino kwa iwo amene sakhulupilira.

Umenewu ndi Mkumano wa Mulungu.

Chomwecho khumbani chimene Iye amakhumba.

Pakutero ife tidzapereka ufulu wochepa ku thupi kuti likagwire ntchito, cholinga kuti zinthu zonse zikachitike mwabwino ndi mwadongosolo.

GAWO 7 15:1-58 KUUKA KWA THUPI

Chiphunzitso ndi Choonadi cha Kuuka

Tsopano tafika pa nkhani ya chiphunzitso chimene oyera mtima akhala nacho vuto –kuuka kwa thupi.

Ena mwa Akorinto anagonjera ku chiphunzitso cha mphekesera chakale ndipo akukanitsitsa za kuuka kwakufa.

Pofuna kukonza kulakwika kumeneku, poti ndi kulakwitsa ndithu, mtumwi akutionetsera za uthenga wabwino.

15:1-11 Kuuka kwa Thupi: Kuuka kwa Khristu

Iye akuwafikiranso oyera mtima monga m’bale ndipo akuwaonetsera za zotsatira za kulakwitsa kumeneku kumene kunabuka pakati pawo.

Uthenga wabwino umene iye anawalalikira iwo ndi njira ya chipulumutso chawo.

Amenewa ndi maziko a kuima kwawo pamaso pa Mulungu.

Udindo wawo ndi kugwiritsitsa mosamala uthenga wabwino, pakuti kuusiya zifanana ndi chikhulupiliro (chopanda) phindu.

Mwachidule, iwo amene alandira mau a chipulumutso, tsopano akuyenera kuwagwiritsitsa.

Kodi nanga akuyembekezeka kugwiritsitsa chiyani?

Khristu anafera machimo athu molingana ndi Malemba (fanizirani Yes. 53), Iye anaikidwa m’manda naukanso tsiku lachitatu molingana ndi Malemba.”

Iwo akuyenera kugwiritsitsa mosamala imfa, kuikidwa m’manda ndi kuuka kwa Khristu, pakuti Malemba amalimbikitsa za imfa, kuikidwa m’manda ndi kuuka kwa Khristu.

Malemba ndi umboni woyambilira –kuyembekezera mwa ulemelero- za kuuka kwa Khristu.

Palinso mboni zina zisanu ndi imodzi amene ndi: Kefa, ophunzira khumi ndi awiri, abale oposa mazana asanu pamodzi, Yakobo, atumwi onse komanso Paulo.

Asanu ndi m’modzi amenewa anamuona Ambuye mu nthawi ya kuuka, kaya ndi ku Galileya, panjira ya ku Emau, ku Yerusalemu, mnyumba yosanjikana, kunyanja ya ku Tiberiya kapena panjira ya ku Damasiko.

Iwo anamuona Iye ndi kumzindikira chimene Iye ali.

Paulo akudzifotokozera yekha ngati mtayo –amene anaona Ambuye osati padziko lapansi koma mu ulemelero.

Iye akudzitenga kukhala mtayo chifukwa mwayi umenewu umapezeka kwa iwo amene ali mkupezeka mwa Ambuye.

Kodi ndi malingaliro otani amene Paulo akubweretsa, pamene akufotokozera za zimenezi?

Kodi anamuchepetsa motani kufika podziona yekha ngati wochepa pakati pa atumwi?

Zoonadi, chifukwa iye anazunza Mpingo, anaziona yekha ngati wosayenera kukhala mtumwi.

Kodi nanga woyenera ndi ndani kugwiritsidwa ntchito ndi Mulungu?


Ndani mu mbeu ya Adamu?

Chisomo cha Mulungu chimatipanga ife kukhala chimene tili, mboni Zake.

Chimodzimodzinso kwa Paulo, chisomo chimenechi chinaperekedwa ndi zotsatira zazikulu.

Pakuti antchito ake ndi ochuluka, ochuluka kuposa iwo a atumwi ena.

Chimenechi ndi choonadi; sizotsatira za mtima wodzikuza, pakuti chinali chisomo cha Mulungu.

Chomwecho chisomo cha mphamvu cha Mulungu chinamuitana iye ndi kumugwiritsa ntchito mochuluka mu utumiki Wake.

Mobwereza, chofunikira si yemwe anabweretsa Mau.

Chofunika ndi chakuti oyera mtima anakhulupilira Mau olalikidwa kwa iwo

15:12-19 Zotsatira za Kulakwitsa –Kuuka kwa Khristu Kukukaikidwa

Mboni zitapezeka pa kuuka ku thupi kwa Khristu (Luka 24:39 mpaka mtsogolo), mtumwi akuonetsa zotsatira za chiphunzitso chimenechi.

Kodi nanga zikanakhala zoona?

Zotsatira zake zikanakhala zotani?

Choyamba, kulakwitsa kumeneku kumabweretsa chitonzo pa Khristu, chitonzo pa Umunthu Wake wodalitsika komanso pa ntchito Yake yomalizika.

Kulira kofuula kuti “kwatha!” kukuikidwa mu funso, (Yoh. 19:30).

Iye analengeza kuti adzaukanso (Mat. 16:21; 17:22, 23; Yoh. 2:9; 10:18).

Ngati kuti palibe kuuka kwa akufa monga ena amanenera, ndiye kuti Khristu sanauke kwa akufa.

Zotsatira za chiphunzitso chotere ndi zoipa.

Kukwera Kwake kumakanidwa.

Kupezeka kwa Mzimu Woyera padziko lapansi lino kumakanidwa.

Ntchito zake za Khristu wokwezedwa Wansembe Wamkulu komanso Wotiyimira zimakanidwa.

Kulalikira kwa mphamvu kogwira mtima kwa atumwi pansi pa chitsogozo cha Mzimu Woyera kuli chabe; chikhulupiliro cha okhulupilira mwa Khristu woukitsidwa chilibe phindu.

Kuonjezera apa, atumwi akutengedwa ngati mboni zabodza za Mulungu pamene anachitira umboni kuti Iye anaukitsa Khristu ngati ndi zoona kuti kulibe kuuka kwa akufa.

Kuonjezeranso, sichikhulupiliro chokha cha okhulupilira chimene chili chopanda phindu, koma choonadi chenicheni ndi chakuti iwo adakali mu machimo awo.

Okhulupilira amene anafa kale, ndipo imfa yawo inali ya mtengo wapatali pamaso pa Ambuye (Mas. 72:14; 116:15), anaonongeka; ndipo Akhristu omwe ali ndi moyo, ndi anthu omvetsa chisoni kwambiri padziko lino lapansi, ngatidi Khristu sanauke.25

Pa zokopa ndi zikhumbokhumbo zimene munthu wadziko lapansi lino amafuna kudzikwaniritsa chifukwa chiyembekezo chake chili mu dziko lapansi ili, okhulupilira samadzikwaniritsa nawo.

Choncho ngati kulibe kuuka, okhulupilira amafa pawiri: pano padziko lapansi chifukwa iwo amadzikaniza okha ku zosangalatsa za chilakolako cha nyama, komanso mtsogolo.

Kupezeka kwathu kukhoza kukhala kochititsa mantha komanso kopanda phindu! Kumeneku ndi kulakwitsa kwakukulu.

15:20-28 Zotsatira Zodalitsika za Kuuka kwa Khristu.

Koma choonadi cha ulemelero, inde, maziko a uthenga wabwino ndiko kuuka kwa kuthupi kwa Khristu.

Tsopano Khristu waukitsidwa kwa akufa” (ndime 20)!

Imeneyi ndi mfundo yokwaniritsidwa!

Mulungu adalitsike!

Amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, naukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama” (Aroma 4:25).

Komatu pali zambiri.

Iye ndi chipatso choyambilira kwa iwo akugona tulo”

Choonadi chodabwitsa ndi ichi: kuukitsidwa kwa Khristu ndi lonjezano lodalilika limene limatitsimikizira ife za kuuka kwa oyera mtima ogonawo.


Chitsanzo cha mphamvu cha izi chaperekedwa ngati umboni ku Mat. 27:51-53.

Zotsatira zake ndi zoipanso.

Mwa munthu munabwera imfa, ndipo mwa munthu munabwera kuuka kwa akufa.

Koma tiyamika, zimenezi sizinachitike ndi munthu m’modzi yemweyo.Kudzera mu tchimo la munthu m’modzi (Adamu), mbeu yake (mtundu onse wa anthu) unakhala pansi pa imfa.

Ndipo anafa” (Gen. 5) ndi ndemanga yobwerezedwa kawirikawiri pa mbeu ya Adamu.

Kufikira lerolino kulibe mtendere.

Komatu Khristu –amene si mbeu ya Adamu (Luka 1:31, 35) –amene ali Munthu wosiyana, anabweretsa ndondomeko yatsopano ya zinthu.

Choncho iwo onse amene amabadwa kuchokera kumwamba (Yoh. 3:3, 5), iwo amene ali mwa Khristu, adzakhala a moyo, pakuti iwo ali olengedwa atsopano (2 Akor. 5:17).

Khristu ndi Mutu.

Iye amabwera koyambilira.

Iye ndi chitsanzo chodalitsika cha thupi loukitsidwa.

Iye ali ndi mphamvu.

Iye ali ndi ulamuliro pa zinthu zonse.

Palibe chimene chinatchinga kuuka Kwake, chomwechonso palibe chimene chidzatchinga kuukitsidwa kwa Ake omwe.

Iye akubwera kudzawaitana iwo kuchoka kumanda (1 Ates. 4:13 mpaka mtsogolo) ndipo adzawapatsa matupi atsopano, matupi oukitsidwa nawo, monga “thupi lake la ulemelero” (Afil. 3:21).

Zotsatira zosafikirika za kuuka kwa Khristu ndi mphamvu Yake yoonetsedwa pa zinthu zonse zikupitilira kuyendabe m’malingaliro a mtumwi.

Khristu Munthu wa ulemelero, atatenga ulamuliro wa dziko lapansi, ndi Mfumu wa iwo akulamulira komanso Mbuye wa iwo akulamula.

Ulamuliro Wake (ngati Mfumu) komanso mphamvu Zake (ngati Mbuye) ndi zadziko lonse.

Iye amagwirabe ntchito zimenezi kufikira Mulungu atakonza zonse kukhala pansi pa ulamuliro Wake.

Mphamvu yoipa yomaliza kulimbana nayo komanso kuthetsedwa ndi imfa, mphamvu yoopsa kwambiri pa munthu (Aheb. 2:15).

Mulungu ndi wotsimikizika kuika zonse pansi pa mapazi a Mwana wa Munthu (Mas. 8:4-9), chifukwa Mwana wa Munthu amapanga dzina la Yehova kukhala labwino padziko lonse lapansi.

Kenako, pamene zinthu zonse zaikidwa pansi pa ulamuliro wa Munthu Yesu Khristu, Iye Mwiniwake adzakhala pansi pa ulamuliro wa Mulungu, kupereka Ufumu wa Mulungu ndi cholinga chimenechi komanso zotsatira zimenezi, kuti Mulungu –Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera- akhale zonse mu zonse.


Zimenezi ndi zotsatira zodabwitsa za kuuka kwa Khristu.

Iwo amapyola pa tsiku la kuuka Kwake, kupyola m’badwo uno kufikira tsiku lamuyaya. Amen.

15:29-34 Nkhani ya Chikhalidwe kuchokera ku Kuuka kwa Khristu

Gawo lapitali timaona zotsatira zimene kuuka kwa Khristu kunakwaniritsa pa Mulungu ndi chilengedwe Chake, komanso pa tsiku lamuyaya.

Tsopano mtumwi akupitilira kuona nkhani imene ndi yolakwika, kuonetsera zinthu zimene zimatsatira pa kuuka kwa Khristu.

Ngati akufa sangauke, chifukwa chiyani okhulupilira akutenga malo a imfa ndi kuuka pamodzi ndi Khristu?

Chifukwa chiyani amabatizidwa?

Ubatizo umasanduka lamulo lopanda phindu, ngati akufa sadzauka.


Ndi chithunzithunzi chomwechi, atumwi anaziika okha pa chiopsezo mosasamala pa zinthu zimene palibepo.

Mopitiliza Paulo akuchita zimenezi, kulimbana ndi “zimbalangondo” za ku Efeso.

Ngatidi akufa sadzauka, kuyesetsa kumeneku, ngakhale ndi kwabwino, koma kulibe phindu.

Njira yokhayo yopezera thandizo labwino mu nyengo ngati imeneyi ndiyo kukhala ngati nyama –pakuti nyama zilibe chiyembekezo kuseri kwa imfa.

Kuti kulakwitsa kumeneku ndi chipatso cha ukathyali wa mdani, ndi zodziwikiratu.

Kumeneku ndi kuyesetsa kwina kufuna kusokoneza Mpingo pansi pano.

Ndipo chilimbikitso chikuvumbulutsa zimenezi: “Musanyengedwe”

Chiphunzitso chonyenga ndiwo muzu komanso chifukwa cha chikhalidwe chopanda umulungu.

Zimaika nkhungu pa oyera mtima osasamala.

Zimaonetsanso kuti iwo amadziwa zochepa mwinanso sadziwa kumene zokhudza Mulungu, nyengo yochititsa manyazi yosayenera kukhalamo.

Oyera mtima akuyenera kutsatsa tulo timeneti cholinga kuti akhale tcheru mu chilungamo, pakutsitsimutsa chikhalidwe choyendayenda chimene chimapezeka mwa iwo.

Mwachisoni, atataya masomphenya akubweranso kwa Ambuye Yesu, Akhristu akulimbana ndi kudzikundikira chuma, kufuna kutchuka ndi maulemu kapenanso kufuna kukhala munthu wodziwika padziko lino.26

15:35-49 Thupi Latsopano ndi Thupi la Uzimu

Zotchinga ku kuuka kwa thupi zikuonetsedwa kukhala zolakwika komanso ntchito ya mdani wa Mulungu.

Madalitso amene amalumikizana ndi kuuka kwa thupi ndi a dziko lonse maonekedwe ake, chipambano cha Mulungu pa tchimo.


Zinthu zimenezi zinaikidwa kukhala zomveka bwino, komabe otchingawo amabwera ndi mdidi.

Tsopano iwo amafunsa mafunso awiri: “Kodi akufa amaukitsidwa bwanji?

Kodi akadzauka adzakhala ndi matupi otani?”

Zotsatira zoopsa ndicho chikumbutso kuti umbuli owuputa dala ukuonekeratu ku umboni ogwira mtima.

Palibe munthu amene ali wakhungu monga uyo amene saona.

Mtumwi akugwiritsa ntchito chimene chili umboni odziwika bwino kwa aliyense.

Mbeu singamere, pokhapokha itafa (Yoh. 12:24).

Chimene mlimi amaika mu nthaka sichimene chimatuluka.


Simukuyenera kudzala papaya kuti mukolole papaya.

Kambewu kakang’ono mu nthaka kamatulutsa mtengo waukulu wa papaya.

Chimene chimatuluka ndi zotsatira za kambewu kenakake kamene kanadzalidwa.

Mbeu ina iliyonse ili ndi thupi lake limene Mulungu analipatsa.

Chimene chimatuluka sichimasiyana ndi maganizidwe a anthu ena kuti munthu akafa mzimu wake umalowa mwa munthu wina.

Chinthu chilichonse cha moyo chili ndi mnofu wake.


Chimene chili mwa munthu ndi chosiyana kwambiri ndi chimene chili mwa nyama, kapena cha m’madzi kapenanso mbalame.

Palibe kuzisokoneza zimenezi.

Sizinachitike mwa ngozi monga nzeru ya iwo amene amakhulupilira kuti munthu akafa mzimu wake umalowa mwa wina.


Kuonjezera apa, matupi akumwamba komanso matupi adziko lapansi ali ndi malo awo okhala komanso kukongola kwawo.

Pakati pa matupi akumwamba, thupi lililonse lili ndi malo ake osiyana komanso kukongola kwake.

Pakati pa nyenyezi zosawerengeka, nyenyezi iliyonse ili ndi maonekedwe ake komanso kukongola kwake; palibe nyenyezi ziwiri zimene zili zofanana.

Mulungu mlengi anazisankha izo.

Kuukitsidwa kwa thupi kumaimira ngati vuto lophweka kwa Mulungu monga umo amaikira m’malo mwake maonekedwe ndi kukongola kwa zinthu zonse padziko lapansi.

Ndipo Iye akuonetsera zimenezi.

Thupi limene limaikidwa m’manda limaikidwa m’menemo kuti likavunde (kukawola), kusalemekeza (chadziko), mu chifooko27 (zakutha) ndipo limeneli ndi thupidi la chilengedwe.

Koma chimene Mulungu amabweretsa mwa kuukitsa kuchoka kumanda ndi thupi la uzimu, kuukitsidwa mu chisavundi (chosayenera kuwola) mu ulemerero (ulemelero wakumwamba) komanso mu mphamvu.

Kusintha kumene thupi limadutsa, kuti likhoza kukayenda mwa ufulu mu nyengo ya kumwamba komanso pansi pano.Tibwereranso ku chitsanzo choyambilira chimene chimasiyanitsa Adamu ndi Khristu.

Mtumwi tsopano akulowa kwakuya.

Munthu woyamba, Adamu, anapangidwa kukhala mzimu wa moyo.

Iye anali ndi thupi lachilengedwe.

Thupi lake la chilengedwe linalandira moyo kuchokera kunja kwa iye yekha (kuchokera kwa Mulungu).

Kusamvera kwake kunabweretsa tchimo ndi imfa ku mtundu (mbeu yake), kuphatikizira matenda ndi kunyozeka.

Iye ndi Adamu woyamba komanso mutu wa mtundu wa anthu.

Aliyense wopezeka mu mtundu umenewu amatenga chikhalidwe kuchokera kwa iye (Aheb. 9:28).

Khristu, Mutu wa Chilengedwe Chatsopano, amapereka chikhalidwe kwa onse obadwa kuchokera kumwamba.

Iye akutsitsimutsa Mzimu, kupereka moyo kuchokera kwa akufa kwa onse otere.

Iye ndi Adamu Womaliza, Mutu wa mtundu wina wa anthu.

Palibe mtundu wina wa anthu umabwera pambuyo pa umenewu.

Chifukwa?

Pali ndondomeko ziwiri zokha: choyamba chimene chili chathupi (Adamu), kenako, chimene chili cha uzimu (Khristu).

Monga mwa chiyambi, munthu woyamba anakonzedwa ndi dothi (Gen. 2:7).


Munthu Wachiwiri, sikukonzedwanso kwa munthu woyamba, pakuti Iye ndi Ambuye (Wolamulira) kuchokera Kumwamba.

Monga mwa chikhalidwe, onse amene ali mbeu ya Adamu ali ndi chikhalidwe chake (cha uchimo) (Aroma 5:19).

Onse mwa Khristu amatenga chikhalidwe kuchokera kwa Iye.

Monga mwa chimaliziro, ife amene tili a Khristu tidzakhala ndi chithunzi chimenechi cha Munthu wodalitsika wakumwamba (Afil. 3:21; 1 Yoh. 3:3), monga zilili mosalakwitsa kuti ife tinabadwa mwa chithunzi cha dziko lapansi.

Monga Mulungu kutipatsa ife zonse ndi zochuluka zimene zinalandidwa mwa Adamu.

15:50-57 Kusinthika mwa Kanthawi.

Atathana ndi funso la chilengedwe cha thupi loukitsidwa, mtumwi akutembenukira ku chikhalidwe cha kuukitsidwa.

Choyamba akuvundukula kanthu kalikonse kamene kali kosafunikira.


Thupi ndi mwazi (munthu ali ndi moyo) sangathe kupeza ufumu wa Mulungu monga cholowa chake,

Tsopano sichinsinsinso: njira ikuvumbulutsidwa.

Sionse amene adzafa (kugona), koma aliyense adzasandulika.

Mulungu adzachotsa nyengo ya dziko lapansi imene ilipoyi, imene imazinga matupi athu m’moyo kapena imfa padziko lapansili.

Iye adzasanduliza matupi athu cholinga kuti ife tisazingidwenso ndi nthawi, malo kapena zotchinga zosakhalitsa.

Mu nyengo yochepa Mulungu adzakonza kusintha konse kwa oyera mtima Ake onse, osati mu mphindi imodzi.

Mkuthwanima kwa diso, Iye adzasanduliza matupi a oyera mtima Ake, osati mkuphetira kwa diso ayi.

Iye adzaitana oyera mtima Ake kuchoka kumanda monga umo anaitanira Lazaro (Yoh. 11:43).

Iye adzawaukitsa iwo ndipo adzawapatsa matupi osaonongeka, amene sangawole.

Iwo amene ali ndi moyo adzalandira matupi osatha, amene ali osafa.

Matupi osavunda komanso osatha ndi matupi a uzimu.

Mopitiliza, pali kukwaniristidwa kwa Lemba limeneli: “Iye wameza imfa ku nthawi yonse” (Yes. 25:8), -chipambano cha Mulungu.

Iye wagonjetsa ndipo anthu Ake ali paufulu.

Chidziwitso choterechi chikupangitsa mtumwi kukondwera kwakukulu mwa Mulungu.

Iwe imfa mbola yako ili kuti? Chili kuti chipambano chako?’

Uthenga ulionse wa imfa, dongosolo lililonse la maliro ndi chikumbutso chabe kuti tchimo ndilo mbola ya imfa (ululu waukulu umene imfa imapereka).

Imfa imatikumbutsanso kuti lamulo ndi mphamvu ya tchimo.

Koma kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, Mulungu wathu wapambana ndi chigonjetso chachikulu pa tchimo, imfa ndi manda.

Ndipo chipambano chimenecho ndi chathu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Ulemelero onse kwa Iye.

15:58 Chilimbikitso

Kodi mtumwi akugwiritsa mfundo zokoma zanji pamene akulankhula mau olimbikitsa amenewa kwa oyera mtima okondedwa a ku Korinto pamene akutseka ndime imeneyi!

Iwo analidi okondedwa a Mulungu Atate, Ambuye Yesu komanso mtumwi.

Kusoweka chidziwitso mbali ina, komanso chiphunzitso chonyenga mbali inayi, chiphunzitsochi chimafunika pamenepa.

Chiphunzitso chimenechi chikuonetsa momwe Mulungu anapambanira kudzera mwa Ambuye Yesu pa mdani wina aliyense.

Chikuonetseranso momwe Iye amadikililira mwa chikondi kukhala ndi chifundo pa munthu chilengedwe Chake.

Komanso munjira ya mphamvu yaikulu chiphunzitsochi chimalimbikitsa wokhulupilira kudzikika mwa Ambuye.

Wokhulupilira wotere ali ngati nyumba yomangidwa pa thanthwe.

Iye ali ngati mtengo wookedwa pa madzi, osagwedezeka ndi mphepo yolimba yoononga.

Chimatilimbikitsanso ife kukhala opezeka, ndi kuchita ntchito ya Ambuye, -imene Ambuye amatipatsa ife kugwira.

Iye ali ndi ulamuliro; Iye amapereka ntchito.

Iye amatilimbikitsa kukagwira ntchitoyo mokondwera, kuitsiriza, mwachilungamo komanso mokhulupirika.

Choonadi cha kuuka kwa thupi chimatipangitsa ife kudziwa kuti kuyetsetsa kumeneku, machitidwe athu pa ntchito ya Ambuye sali opanda phindu.

Zikathera mu madalitso ndi ulemelero wochokera kwa Mulungu wathu.

Kwa Iye kuli Ulemelero onse, Amen.

GAWO 8 16:1-24 ZOLANGIZA ZOTSIRIZA NDI MALONJE

16:1-3 Chopereka cha Oyera mtima

Mtumwi akupereka malangizo otsiriza kwa oyera mtima okondedwa ku Korinto, kuyambira ndi malangizo okhudza chopereka cha oyera mtima.

Choncho ndi kofunika kutchera khutu ku malangizo amenewa.

Monga aliyense amakhala ndi malingaliro osiyanasiyana pa chopereka cha oyera mtima kusiyana kumeneku kuliponso ngakhale tsopano.

Ena samapereka; pomwe ena samafuna kuphonya nthawi ya kupereka.

Ifetu tikhoza kutsimikizika pa chinthu chimodzi: malangizo amenewa sakutsutsana ndi mfundo ya m’Malemba kapenanso kukhala kunja kwa malire a ntchito ya chikondi.


Monga mtumwi komanso wokhala ndi ulamuliro wa Mulungu, Paulo pamenepa akupereka kwa oyera mtima malangizo omwewo amene anapereka ku mpingo wa ku Galatiya.

Ndondomeko zimenezi ndi zosavuta; palibe kalikonse kokhudza chikhalidwe mu ndondomekozi.

Pokhudza chopereka, kupereka kuchitike mwa dongosolo, tsiku loyamba la sabata.

Iye sakupereka chilolezo cha tsiku lina lililonse.

Chachiwiri, kupereka timakonzekera komanso tipereke monga mwa kupindula.

Imeneyi ndi ndondomeko ya zachuma ya kumwamba, kupatula monga Ambuye watidalitsira ife.

Chopereka chokonzekera chikuyenera kuchotsa chikhumbokhumbo cha chopereka chapadera.

Paulo akulewa mchitidwe wa chopereka chapadera pakuti kupezeka kwake kumapangitsa iwo kupereka munjira yotsutsana ndi malemba.

Chachitatu, chopereka chimakhudza mtima wa munthu.

Kupereka kumatengera momwe Mulungu watidalitsira, osati monga momwe amzathu akuperekera; osatinso monga mwa kulamula kwa bungwe la zachuma.

Kumeneku ndiko kupereka kokondwera, machitidwe amene amapangitsa wopereka kubwera chifupi ndi Mulungu.

Kodi nanga mphatso zosankhika?

Pa mfundo yakuti dzanja lanu lamanja lisadziwe chimene dzanja lamanzere likuchita, kupereka mphatsoyo chindunji kwa woyilandira ndi njira yabwino kwambiri.

Mfundo zimenezi, zimene mtumwi Paulo anaziyala sizikungokhudzana ndi nyengo izi zokha, koma zikuperekanso ndondomeko zabwino za malemba ku mpingo lerolino.

Kuonjezera apa, mongodutsa pa chopereka kwa oyera mtima amene asankhidwa kulandira mphatsozo, mpingo usankhe atumiki amene mpingo uli nawo chikhulupiliro.

Paulo sakutenga nawo gawo mu chisankho chimenechi, ngakhale iye anali mtumwi.


Iye akupereka kwa iwo dzanja lamanja la chiyanjano, kudzipereka iye kukhala nawo pamodzi ngati ndi chifuniro cha Mulungu.

16:5-9 Ndondomeko Zapadera za Mtumwi

Mtumwi akuulula kuti ndondomeko zake zimene iye anali nazo zikuphatikizirapo kupita ku Korinto atadutsa kaye ku Makedoniya.

Ulendo umenewu ukhoza kukhala wopitilira cholinga kuti chisamaliro chawo chikhoza kumutumiza kulikonse kumene Ambuye angamutsogolere.

Iye sawayendera iwo nthawi yomweyo atawatumizira kalata.

Mwina mpata umenewu umaperekedwa kuwalola kuti iwo achite monga mwa malangizo a mu kalata yake.

Komabe iye akuyembekezera kuti akafika, akakwanitse kukhala nawo kanthawi.

Mu zonsezi, iye ali pansi pa chitsogozo cha Ambuye.

Kwa nthawi ino, iye akhalabe ku Efeso kufikira tsiku la Pentekoste.

Atazindikira kuti Ambuye watsegula khomo la utumiki wamphamvu ndi wacholinga (Chiv. 3:7, 8), iye akukonza dongosolo kugwiritsa ntchito mwayi umenewu ndi chiyembekezo chachikulu mwa machawi ali mwa iye pa Ambuye.

Kuti pali adani ochuluka zikungosonyeza poyera kuti ndi mwayi waukulu wa Ambuye kuti amugwiritse iye ntchito mwapamwamba

Limeneli ndi phunziro lofunikira kwa iwo amene agwiritsidwe ntchito ndi Ambuye: mwayi ukakula, mdani amabweretsanso kulimbana kwakukulu.28

16:10-12 Kufika kwa Abale Otumikira

Mtumwi akuona za abale awiri amene akuwayendera amene ali ndi zolinga ziwiri zosiyana.Timoteo, mtumiki mzake wa Paulo wachichepere anali munthu wa mzimu wachidziwitso.

Mu makalata ake kwa iye, Paulo akufuna kumulimbikitsa kulimbika m’moyo mwake komanso mu ntchito (1 Tim. 4:12; 2 Tim. 1:4-7).

Iwo onse akudzipereka ku ntchito ya Ambuye ndi chidwi chofanana (Afil. 2:20).

Timoteo akufuna kuyendera mpingo wa ku Korinto.

Podziwa momwe oyera mtima kumeneko amamuonera iye, Paulo akanamvetsetsedwa akanayesera kumuletsa Timoteo.

Iye sakumutumiza iye, koma akumulimbikitsa za ulendo wake, kumuonetsera dzanja lamanja la chiyanjano.

Kuonjezera apa iye akuwalimbikitsa oyera mtima kuti akhale chilimbikitso komanso kumuthandiza Timoteo pamene iye ali nawo pamodzi kumeneko, komanso pamene ali kuchoka pakati pawo.

Mbali inayi Apolo anali m’bale wodziwika bwino kwambiri amene khalidwe lake linafika ku Korinto (1:12; 3:4).

Zimene iye amadziwika nazo (Mach. 18:24, 25) zinapangitsa oyera mtima kumeneko kumusilira.

Koma kulankhula kwake konse kwa nzeru, chidziwitso chake pa malemba, komanso uzimu okhala nawo umboni, iye sakuvomerezana ndi pempho la Paulo kuti apite ku Korinto.

Paulo sakumulamula koma akuvomereza maganizo ake.

Zikuonetsa kuti chiyembekezo cha munthu chimasiyana ndi chitsogozo cha Ambuye.

M’bale wa manthayu akuchita dongosolo kupita ku Korinto; m’bale wopanda mantha alibe dongosolo lopita.

M’bale wodziwa kulankhula sali wokonzeka kupita koma m’bale wachidziwitso akuchita chisankho chopita ku mkumano umene umakhulupilira machitachita a munthu ndi kupezeka kwake.

Chitsogozo cha Ambuye ndi chimene chimaonetsa kusiyana pakati pa iwo ndi ife.

Paulo akuona za ubwino wa Mulungu ndi mfundo yofunika iyi: Apollo adzabwera akadzakhala ndi mpata wabwino.


Umenewu ndi mpata woperekedwa ndi Ambuye, osati woperekedwa ndi mtumwi.

16:13-18 Chilimbikitso

Chifukwa iye sanafune kuti iwo adalire kwambiri pa m’bale owayendera, mtumwi akuwalimbikitsa iwo, poyambilira, kukhala tcheru pokhudzana ndi mdani (1 Pet. 5:8) amene machenjelero ake ndi zida zake sizidziwika kwa ife.

Chachiwiri, iwo akuyenera kuzikika ndi kulimba mu choonadi cha Mulungu.

Kukhala tcheru kumafunika chidziwitso cha choonadi.

Chachitatu, iwo akufunika kukhala okhwima.

Pachiyambi, khalidwe lawo, linaonetsedwa m’kalatayi, linali monga la mwana wosamvera.

Mwa mau ake owunikira kwa iwo, iye akuwalimbikitsa kuti akule.

Zonse zingathe kupangidwa mwa dongosolo, ngati zipangidwa mwa chikondi –chikondi chimene chaperekedwa kuti chionetsedwe kwa ana Ake.

Zili kwa iwo kuonetsera kukhwima ndi kupereka malo ku chikondi chimenecho.

Pamene atsogozedwa ndi chikondi, oyera mtima adzalandira chilimbikitso kukhala omvera onse amene adzipereka okha kutumikira oyera mtima.

Banja la Stefana, pakati pa otembenuka oyambilira ku Akaya ndi chitsanzo cha atumiki odzipereka.

Paulo akuonetsa kudzipereka kumeneku ndi chitsanzo chake chomwe, kusangalala pamaso pa Stefana, Fortunato ndi Akayiko.

Mathandizo awo ndi mphatso zawo kwa iye, akudzilandira mwa chisomo ndi chiyamiko m’malo mwa zimene oyera mtima sanathe kuchita.

Machitidwe awo ndiwo chiyambi cha madalitso atsopano kwa iye komanso oyera mtima.

Oyera mtima amachita bwino ngati amayamikira m’bale amene amatumikira munjira yodzichepetsa chonchi.


16:19-24 Malonje

Iye anamaliza ndi malonje kupita kwa oyera mtima ku mipingo yonse ya ku Asiya.

Akula ndi Priska, komanso mpingo wa mnyumba zawo akupereka malonje; komanso abale ena onse.

Anali malonje a munthu payekha komanso a gulu lonse.

Komanso Paulo mwini anapereka malonje ake.

Kulonjera abale kukuyenera kuchokera mu mtima wa chikondi.

Chipsopsono chikhale chisonyezo cha chiyero cha chikhalidwe cha umulungu.

Iwo amene sakonda Ambuye akhoza kupereka chipsopsono cha Yudase cha mangawa.

Komanso kuchokera mu mtima wa chikondi kwa iwo akuwachenjeza onse: Aliyense osakhala nacho chikondi cha Ambuye Yesu atembereredwe; Ambuye akubwera.

Iye anapempherera kupezeka kwa chikondi ndi chifundo cha Ambuye Yesu pa iwo komanso chikondi chake.

Chomwecho mtumwi akumaliza kalata yake, imene ili ndi fungo lonunkhira la chikondi cha Mulungu kwa anthu Ake.

Mu kalata imeneyi Mzimu Woyera akumutsogolera iye kugawa moleza mtima chidziwitso cha njira za Mulungu kwa osadziwa koma ndi mtima wodzichepetsa, kulanga kwa khalidwe la mwana ndi dzanja la chikondi la atate, komanso nthawi yomweyo kulimbikitsa kukhwima kwa Akhristu.

Iye akudzudzula mosanyengelera machitidwe a chidetso ndi kuwalimbikitsa kukhala oyera mtima; komanso akudzudzula kunyada ndi kudzikonda nthawi yomweyo akuwalimbikitsa machitidwe a chikondi cha umulungu mwa anthu a Mulungu.

Mu kalata yonseyi Mzimu Woyera akulankhula mwa Paulo ndi cholinga chimenechi: kuti umboni wa ulemelero wa Khristu upite kwa Mulungu mwa kusangalala kuchokera padziko Lake lapansi.

Pakuti pamene iwo apereka uthenga womveka bwino wa nzeru ya mitundu mitundu ya Mulungu ku akulu ndi amaulamuliro m’zakumwamba (Aef. 3:10), ndipo pamene awonetsera maonekedwe a Ambuye Yesu kudziko lapansi limene linamukana ndipo likumukanabe Iye, iwo amakwaniritsa udindo opatsidwa ndi Mulungu monga mwa kukhutitsidwa Kwake.

Mtima wokhutira wa Mulungu ukhale chiyambi cha zochita za anthu Ake.

Kwa iye kukhale ulemelero ndi ulemu, Amen.