ZINTHU ZIMENE ZIMATSATIRA CHIPULUMUTSO



MALONJE



Mau odabwitsa amenewa, “zinthu zimene zimatsatira chipulumutso,” amene ndi mutu wa bukuli akugwiritsidwa ntchito ndi zolembedwa zouziridwa mu Kalata yopita kwa Aheberi.Iye amalembera iwo amene anatuluka mu chipembedzo cha Chiyuda, ndipo anavomereza kukhala otsatira Khristu ndipo anatenga malo awo pakati pa Akhristu.Koma pakupita kwa nthawi, ena anayamba kusiya Chikhristu chawo ndi kubwerera m’mbuyo, kuonetsera kuti iwo sanatembenuke zenizeni kupita kwa Khristu ndi kupulumutsidwa.



Mlembi akuwauza ku Ahebri 6 kuti iwo amene anaunikiridwa ndi kulawa mphatso za kumwamba ndipo anatengapo gawo la Mzimu Woyera nalawa Mau a Mulungu Abwino komanso mphamvu ya nthawi ili nkudza, anagwa m’chisokero, nkosatheka kuwakonzanso kuti atembenuke mtima, chifukwa adzipachikiranso okha Mwana wa Mulungu (ndime 4-6).



Mosiyana ndi awa amene anangolawa zinthu zabwino za Mulungu, iye akupitilira kulankhula za dziko lapansi limene limamwa mu mvula imene imagwa ndi kubweretsa chipatso komanso kulandira mdalitso kuchokera kwa Mulungu (ndime 7) chimene chili chithunzithunzi cha Mkhristu weniweni.



Iwo analandira Khristu m’mitima mwawo ndipo anamwa mu madalitso a kumwamba, osati kungowunikiridwa wamba zokhudza Iye ndi kulawa monga enawo, koma amabereka chipatso cha Mulungu.“Koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang’ono ikadatembereredwa; chitsiriziro chake ndicho kutenthedwa” mlembi akupitilira kulemba (ndime 8).



Ngati nthaka ibweretsa zinthu zopanda phindu ngati minga ndi mitungwi, zimaonetsera poyera kuti nthakayo silibwino.



Chipatso chomera chimaonetsera momwe nthaka ilili.







Choncho iwo amene amavomereza kuti ndi Akhristu ndipo ali ndi chipulumutso mwa Khristu, koma samabereka chipatso cha Mulungu, koma amabereka chimene chimaoneka ngati minga ndi mitungwi, pamenepo amaonetsera poyera kuti iwo sanasinthike m’mitima mwawo kapenanso kutembenukira kwa Khristu.Nkhani yake imakhala yakale yomwe ija ya thupi la uchimo mwa iwo, limene silingathe kubereka chipatso chovomerezeka ndi kusangalatsa Mulungu (Aroma 8:7,8).Mlembi wouziridwa akutembenukira kwa Akhristu enieni otembenuka mtima pakati pa gulu la Ahelene ndi kunena, “Koma okondedwa takopeka mtima kuti za inu zili zoposa ndi zophatikana chipulumutso” (ndime 9).



Ndipo mu ndime yotsatira iye akulankhula za ntchito yake ndi chikondi chimene iwo adaonetsera padzina la Mulungu, zimene Iye sadzaiwala, komanso momwe iwo adatumikilira kwa oyera mtima a Mulungu.

Mwa iwo munapezeka chipatso cha Mulungu, chipatso chatsopano, chikhalidwe cha umulungu, chimene iwo anali nacho, zinthu zimene zimatsatira chipulumutso mwa Khristu.

1. MTENDERE NDI MULUNGU



Chipulumutso chimatanthauza kumasulidwa, kuwomboledwa kapena kuchotsedwa ku chinthu choopsa kwambiri kapena chosautsa.



Chipulumutso cha Mulungu, chimene ndime yathu ku Ahebri ikulankhula, ndicho chipulumutso cha wokhulupilira mwa Khristu kuchokera ku mkwiyo ndi chiweruzo cha Mulungu, chimene chinatiyenera chifukwa cha machimo athu, komanso kuchoka ku chiopsezo chachikulu cha kusokonekera kwamuyaya mu nyanja ya moto.



Kudzera mu chikhulupiliro chenicheni cha mwa Yesu Khristu komanso ntchito yake ya chiombolo m’malo mwathu pa Kavale, Malemba amatitsimikizira ife kuti tinapulumutsidwa kuchoka ku chiweruzo cha uchimo ndipo tinapeza chipulumutso chodabwitsa cha Mulungu ku thupi, moyo ndi mzimu (Yoh. 3:16; 5:24). Ife “tinapulumutsidwa ku mkwiyo ulinkudza” (1 Ates. 1:10) pa chifukwa chimenechi tili ndi mtendere wopambana ndi Mulungu pokhudza machimo athu komanso pa nkhani yokhudza malo athu ofikira kwamuyaya (Aroma 5:1,2).



Moyo utavutika komanso kusautsika pa kutsutsidwa ku uchimo ndi kuzindikira nyengo yake ya kusochera, imene imadutsira mu kuvomereza Khristu ndi chidziwitso cha chipulumutso mwa Iye, chisangalalo cha mtendere wodabwitsawu ndi chachikulu kwambiri.



Nkhani yaikulu ya chipulumutso cha moyo yatha tsopano, ndipo kuvutika ndi kusautsika kwa moyo, kwapuma ndipo mtima wadzadzidwa ndi kudekha kokoma kwa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa chikhulupiliro cha mwa Yesu Khristu.



Mtendere umenewu “umene umaposa chidziwitso chonse,” ndiwo chinthu choyamba chimene chimatsatira chipulumutso cha Mulungu, komanso chisonyezo chenicheni cha Mkhristu weniweni.



Wokondeka muwerengi, kodi uli nawo mtendere wodabwitsawu ndi Mulungu?



Mungathe kunena kuti ndinu Mkhristu, koma kodi mulidi pa mtendere ndi Mulungu pansi pa mtima wanu?



Kumbukirani kuti Mkhristu ali ndi chipulumutso cha Mulungu, ndipo mtendere ndi Iye umatsatira pa chipulumutso chachikulu chimenechi, ndipo chimenechi ndi chizindikiro kuti iye ndi mwana wa Mulungu.

Kodi chilipo chinthu china chabwino padziko lapansi kuposera kukhala pa mtendere ndi Mulungu pokhudza machimo athu ndi kukhala pa mtendere komanso mpumulo monga kumalo athu ofikira amuyaya?



Ngati inu simuli pa mtendere ndi Mulungu, “muzolowerane ndi Iye, nimukhale pa mtendere: mukatero zokoma zidzakuzerani” (Yobu 22:21).



Khristu wakukonzerani inu mtendere mwa mwazi wa mtanda wake (Akol. 1:20).



Vomerezani Iye ngati Mpulumutsi wanu ndipo mudzakhala pa mtendere ndi Mulungu.



Komatu pali zambiri zoposa mtendere ndi Mulungu kwa Mkhristu.



Iye akhoza kukhala ndi “mtendere wa Mulungu” komanso “Mulungu wa mtendere” mwa iye.



Paulo akutiuza kuti, ngati ife tibweretsa zonse zimene zimatisautsa kwa Mulungu mu pemphero ndi chiyamiko, mtendere wa Mulungu udzasunga mitima yathu ndi malingaliro athu mwa Khristu Yesu (Afil. 4:6,7).



Zimenezi zikutanthauza kuti ife tidzakhala ndi mtendere womwewu ndi Mulungu, mtendere umene umazungulira mpando wake wachifumu, ngati tchinga kuzungulira mitima yathu ndi malingaliro athu mwa Khristu Yesu (Afil. 4:8,9).



Koma zinthu ziwiri zimenezi zili nazo zoti titsatire ndipo tingathe kusangalala nazo ngati tikwaniritsa zofunika kutsatirazo.



Moonjezerapo ife tikuuzidwa kuti “tilondole zinthu za mtendere” (Aroma 14:19) ndiponso ngati nkutheka “tikhale ndi mtendere ndi anthu onse” (Aroma 12:18).

Ndipo ku Aefeso 6:15 tikuuzidwa kuti “tiveke mapazi athu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere.”



Pamenepa tikuona momwe mtendere ukuyenera kuonekera mwa Mkhristu mwanjira ina iliyonse.



Iye amavomereza mtendere wa Khristu umene unapangidwa kwa iye ndi Mulungu pa mtanda, ndipo mwa chikhulupiliro mu ntchito ya Khristu iye ali nawo mtendere ndi Mulungu.



Pakubweretsa mavuto ake onse a m’moyo kwa Mulungu mu pemphero, iye ali ndi mtendere wa Mulungu mkati mwake, ndipo pakudzadzidwa ndi zinthu zabwino ndi kuzichita, iye ali naye Mulungu wa mtendere.



Kenako iye amachita zinthu zimene zimabweretsa mtendere (osati kukolezera vuto koma m’malo mwake kudzikaniza yekha pakusunga mtendere), ndi kuyetsetsa kukhala pa mtendere ndi anthu onse, mapazi ake atanyamula uthenga wabwino wa mtendere kulikonse kumene akupita.Mtendere wopezeka mkati ndi kunja komwe, ndi chimodzi mwa zinthu zimene zimatsatana ndi chipulumutso mwa Khristu ndipo ndi chimene chikuyenera kuoneka mwa onse amenedi ali ndi chipulumutso cha Mulungu.



Tiyeni tiganize za izi kawirikawiri, ndi kufunitsitsa kudziwika kwambiri ndi mtendere wa Mulungu munjira yeniyeni ndi yochita ntchitoyo: “Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m’mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m’thupi limodzi” (Akol. 3:15).



2. CHIMWEMWE



Pamene munthu ali ndi chipulumutso mwa Khristu ndipo wapeza mtendere ndi Mulungu, chimwemwe ndicho chinthu chotsatira chimene chimadzadza mu mtima monga chinthu chotsatira pa chipulumutso cha Mulungu.



Mtima umene wadzipereka kwa Khristu ndipo mwa chikhulupiliro wavomereza lonjezo m’Mau ake okhudza kupulumutsidwa mwa chikhulupiliro mu imfa yake ya chiombolo, ali ndi umboni mkatikati mwa Mzimu wa Mulungu wokhalira mwa ife, kuti iye ndi mwana wa Mulungu ndipo anapulumutsidwa kwamuyaya (Aroma 8:16; Aef. 1:13,14; 1 Yoh. 5:10-13).



Zotsatira ndi zakuti “pokhulupilira mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka ndi cha ulemelero” (1 Petro 1:8).



Tsopanotu pali, osati mtendere wokha wodabwitsa ndi wa bata mu mtima, komanso chimwemwe ndi chisangalalo chosaneneka kudzadza moyo wa iye wobadwa-kwatsopano.



Iye ali ndi chimwemwe chimene sanachionepo chikhalire, chimene dziko lapansi silingathe kupereka.



Chimenechi ndi “chimwemwe mwa Mzimu Woyera” chimene iye amene ali ndi chipulumutso mwa Khristu amasangalala nacho, chimwemwe chimene Mzimu amaika mu mtima wa wolapayo, wochimwa wokhulupilira. Aroma 14:17 akutiuza kuti chikhalidwe cha ufumu wa kumwamba sichili pa zinthu za thupi, koma “chilungamo ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.”



Zinthu zitatu zimenezi zimaonetsera iwo amene akupezeka mu ufumu wa Mulungu.



Iwo ali ndi chilungamo cha Mulungu mwa Khristu, ndipo amatsatira chilungamo, ndiponso ali ndi mtendere komanso chimwemwe m’mitima mwawo.



Gawo lodabwitsa limeneli!



Wokondedwa muwerengi kodi limeneli ndi gawo lako?



Kodi inu munapeza kale “chimwemwe chosasimbika” chimenechi, chimene chimatsatana ndi chipulumutso cha Mulungu?



Ngati simunapeze, ndi chifukwa chiyani?



Mwina mwake simunabwere ndi machimo anu motsimikizika kwa Khristu ndi kumufunsa moona mtima kuti akupulumutseni.



Ngati inu mwabweradi kwa Iye kuti mupulumutsidwe, ndipo mudakalibe mtendere wodabwitsa umenewu ndi Mulungu, ndi chimwemwe chotsatira, mwina ndi chifukwa chakuti inuyo simunakhulupilire mokwanira mu ntchito ya Khristu pa inu pa Kavale, ndi kusakhulupilira malonjezano mu Mau ake amene amatipatsa chitsimikizo cha chipulumutso kwa onse amene amavomereza Khristu ngati Mpulumutsi.



Kumbukirani, kuti “mukukhulupilira, inu mumasangalala ndi chimwemwe chosasimbika.”



Dziwaninso kuti ndi m’kukhulupilira kokha mu mtima – kuti chikhulupiliro chenicheni ndi cha moyo chimene chimadzipereka chokha kwa Khristu ndi kuvomereza Iye ndi chipulumutso chake – chimene chimabweretsa chipulumutso ndi chimwemwe ku moyo (Aroma 10:9,10).



Chikhulupiliro cha chidziwitso wamba chokhudza Khristu sichingakupulumutseni kapena kukupatsani chimwemwe chodabwitsachi.



Kwa inu, amene simunapulumutsidwe komanso simunalaweko chipulumutso, ndipo simudziwa chimwemwe cha chipulumutso, ndikhoza kunena kuti mulibe chisangalalo, kapena chimwemwe padziko lapansi chimene chimachokera ku chipulumutso cha Mulungu.



Zinthu za dziko lapansi sizingakwaniritse mtima wanu kapena kukupatsani chimwemwe chenicheni.



Zokondweretsa za zoipa” ndi “za nthawi” (Aheb. 11:25).



Zokondweretsa zimenezi ndi zachabe komanso zosakhazikika.



Zimakhala ngati thovu la sopo lowala limene limauluka mokongola, kenako ndi kuphulika ndi kusowa pamene muligwira.



Mau akuti “chimwemwe” akugwiritsidwa ntchito patalipatali ndi munthu wadziko, pakuti iye sakudziwa kuti mauwa ndi chiyani.



Chimwemwe chimadziwika ndi Mkhristu yekha ndipo chimapezeka mwa Khristu yekha.





Choncho mlembi wa nyimbo analondola pamene ananena, “ngati mukufuna chimwemwe, chimwemwe chenicheni, chimwemwe chodabwitsa, lolani Yesu alowe mu mtima mwanu.”



Mwina ena mwa inu mungathe kumanena pa inu nokha pamene mukuwerenga mau amenewa, “poyamba ndinali ndi chimwemwe cha chipulumutso komanso chimwemwe mwa Ambuye, koma chinanditayika. Inetu sindili wokondwanso tsopano monga ndinalili kale nditangopulumutsidwa kumene.”



Zimenezi ndi zothekadi, pakuti Mfumu Davide nthawi ina anapemphera, “Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu” (Mas. 51:12), kuonetsa kuti iye anakumananso ndi nyengo yotereyi.



Iye anataya chimwemwe cha chipulumutso cha Mulungu ndipo masalmo omwewa akutiuza chifukwa chimene anatayira chimwemwechi.



Iye anachimwa ndipo anakhumudwitsa Mulungu kwambiri (ndime 1-4).



Chimenechi ndi chifukwa chake timataya chimwemwe mwa Ambuye, chifukwa timachimwa munjira ina.





Mzimu wa Mulungu wokhala mwa ife amakhumudwitsidwa ndipo amasiya kutipatsa ife chimwemwe mkati mwathu ndipo timakhala osakondwa ngakhale tili ana a Mulungu.



Mungathe kuona kuti, Davide sanapempherere kubwenzeretsedwa kwa chipulumutso, koma chimwemwe cha chipulumutso.



Pamene ife tachimwa ngati wokhulupilira, timataya chimwemwe cha chipulumutso, osati chipulumutsocho, pakuti chimenechi ndi chotetezeka mwa Khristu.



Chomwecho ife tikupemphedwa kuti, “Tisamvetse chisoni Mzimu Woyera” (Aef. 4:30).



Kodi ndi zotheka kupenzanso chimwemwechi mwa Ambuye?



Inde; Davide anali ndi chikhulupiliro mwa Mulungu kuti abwenzeretsa chimwemwe kwa iye chotero anavomereza machimo ake kwa Mulungu ndipo anasweka mtima ndi kudzichepetsa pamaso pake ndipo anapemphera kuti ayeretsedwe ndi kubwenzeretsedwa chimwemwe (Mas. 51).



Ambuye amatitsimikizira ku 1 Yohane 1:9 kuti “Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.”



Kuvomereza machimo, kudzichepetsa wekha pamaso pa Mulungu ndi kupemphera kwa Iye ndiyo njira ya kuyeretsedwa kuchoka ku kumvetsa chisoni Mzimu, ndi kupita kunjira ya kubwenzeretsedwa kwa chimwemwe cha chipulumutso.



Zimenezi tikuyenera kuchita kawirikawiri, ngati tikufuna kusungidwa mu chimwemwe cha Ambuye, pakuti timamvetsa chisoni Mzimu munjira zosiyanasiyana ndipo tikuyenera kudziweruza tokha pa zimenezi.



Chomwecho ngati inu mwataya chimwemwe cha chipulumutso, chitani monga anachitira Davide, ndipo pamenepo mudzakhalanso wosangalala, ngakhale kuti kubwenzeretsedwa kwa chimwemwecho kumakhala kochedwerapo kusiyana ndi kutaya chimwemwecho.



Potseka lingaliro lathu lochepa lokhudza chimwemwe, ndikufuna muone kuti Baibulo limalankhula za mitundu yosiyanasiyana ya chimwemwe cha Mkhristu pambali pa chimwemwe choyamba chimene timalandira pa nthawi ya kutembenuka mtima.



Inde, pali chimwemwe chowonjezera kwa wokhulupilira mwa Khristu ndipo chimapezedwa munjira zosiyanasiyana.



Santhulani Malemba ndipo muone kuti mupeza mitundu ingati.



Pano pali mitundu iwiri kungokuyambirani chabe.



Mtumwi Paulo akunena, “Chimene tidachiona, ndipo tidachimva, tikulalikirani inunso mukayanjane pamodzi ndi ife; ndipo chiyanjano chathu chilinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wake Yesu Khristu; ndipo izi tizilemba ife, kuti chimwemwe chathu chikwaniridwe” (1 Yohane 1:3,4).



Pamenepa pali chimwemwe chopezedwa pakukhala pachiyanjano, kapena kukhala mu zinthu zofanana ndi Atate komanso Mwana wake.



Yendani ndi Mulungu ndipo chimwemwe cha chiyanjano chimenechi chikhala chanu – chimwemwe chokwaniridwa.



Kenako ku Yohane 16:24, Ambuye akunena, “Pemphani ndipo mudzalandira kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.”



Pemphani mwa pemphero ndipo kulandira kwa mayankho a Mulungu pa zopempha zanu zidzakupatsani chimwemwe chokwaniridwa.



Chimenechi ndi chimwemwe cha pemphero loyankhidwa.



Onani ndime zimenezi zikukamba za chimwemwe chokwaniridwa.



Limeneli ndiye khumbo la Mulungu kwa ife – osangoti chimwemwe chochepa, koma mtima wodzala ndi wosefukira.



Kumbukira wokondedwa muwerengi, kuti ngati unapulumutsidwa, chimwemwe ndi chimodzi mwa zinthu zimene zimatsatira chipulumutso mwa Khristu ndipo chikuyenera kuonekera mwa Mkhristu.Chomwecho “kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse ndibwerezanso kutero, kondwerani” (Afil. 4:4).



Inu simungathe kukondwera nthawi zonse mu nyengo zanu, koma mungathe kukondwera nthawi zonse mwa Ambuye ngati mungachotse chidwi chanu pa nyengo zanu ndi kuyang’ana pa Iye.



Munjira imeneyi inu mungathe “kukondwera nthawi zonse” (1 Ates, 5:16).



3. MAYAMIKO NDI MATAMANDO



Tiyeni titembenukire ku zochitika zimene zalembedwa ku Luka 17:12-19, ndi kuona molondola chimene chimatsatira chipulumutso ndi kumasulidwa.



Pamenepa pali nkhani ya akhate khumi amene anakweza mau awo ndi kulilira chifundo kwa Yesu ndipo Iye analowa m’mudzi, komanso momwe onse anayeretsedwera ndi kuchiritsidwa pamene anachita mwa chikhulupiliro pa mau a Ambuye.



Koma mfundo yaikulu mu nkhani imeneyi ndi iyi: “Ndipo m’modzi wa iwo, pakuona kuti anachiritsidwa, anabwerera m’mbuyo, nalemekeza Mulungu ndi mau akulu; ndipo anagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye” (ndime 15,16).



Kodi chimenechi sichinali chinthu chabwino ndi choyembekezeka kuchitika?



Inde, zinali zoyenera kuti wakhate ameneyu abwerere pambuyo ndi kuyamika komanso kulemekeza Mulungu chifukwa cha chipulumutso chake ku matenda oopsya a khate, amene anali osachiritsika ndi munthu.



Zinali zoyenera kuti iye anagwa nkhope yake kumapazi a Yesu, nampatsa Iye mayamiko a mtima wake pakuyankha kulira kwake kwa chifundo ndi kumuchiritsa iye.





Komatu izi sizinali zoyenera ndi zabwino kuchitika ndi wakhate m’modzi yekha; zinayenera kuchitika ndi akhate khumi onse aja, pakuti onse anachiritsidwa ku nthenda yawo.



Zimenezi ndi zomwe Yesu amayembekezera kuti onse achite, pakuti Iye anafunsa, “Kodi sanakonzedwa khumi? Koma ali kuti asanu ndi anayi aja? Akubwera kulemekeza Mulungu sanapezeka m’modzi kodi, koma mlendo uyu?” (Luka 17:17,18).



Ndi ndime imeneyi, ife tingathe kunena kuti kuyamika, kuthokoza ndi kulemekeza Mulungu zikuyenera kupezeka mwa iwo amene apulumutsidwa ndi Khristu ndipo ali ndi chipulumutso chake chodabwitsa.



Zimenezi ndi “zinthu zimene zimatsatira chipulumutso” ndipo zimapereka umboni wa kusinthika kwa mtima ndi kutembenukira kwa Khristu.



Kodi simukuganiza choncho, muwerengi wanga?



Ngati timavomereza kuti ndife opulumutsidwa ndi kunena kuti ndife Akhristu, kuyamika kwa mtima kopita kwa Khristu kumeneku ndi matamando opita kwa Iye komanso omuyenera zikuyenera kuchokera kwa ife ndiponso mwa umboni.



Tikuyenera kumuyamika ndi kumutamanda chifukwa cha nsembe yake yaikulu, pa kudzipereka yekha kutipulumutsa ife;unali udindo wake ndipo ngongole yathu ya chikondi chovomerezeka iperekedwe m’malo mwake.



Izi ndi zomwe Yesu akuyembekezera kuchokera kwa ife, monga tinaonera ku Luka 17.



Ndipo Iye ali ndi ufulu kuona zimenezi kwa ife.



Bwanji nanga tikhala osayamika ngati akhate asanu ndi anayi aja amene analandira chifundo chachikulu chotere, koma mapeto ake osayamika Mulungu.

Muwerengi, kodi uli ngati asanu ndi anayiwa, kapena uli ngati m’modzi amene anathokoza ndi kulemekeza Khristu?



Tikawerenga ku Masalmo 40, timapeza nkhani yomweyi ya kulemekeza ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha chipulumutso.



Wolemba Salimo moonetsera anali mu chipsinjo chachikulu ndipo analilira kwa Mulungu, pakuti anati: “Ndipo anandilola, namva kufuula kwanga. Ndipo anandikweza kunditulutsa m’dzenje la chitayiko, ndi mthope la pachithambwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga. Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m’kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona” (Mas. 40:1-3).



Ine ndili ndi chikhulupiliro kuti Ambuye amaikanso nyimbo yatsopano ya malemekezo ndi mayamiko mu mtima komanso m’kamwa mwa wina aliyense lerolino amene Iye anamutulutsa m’dzenje la uchimo namuika pa thanthwe la Iye yekha, pakuyankha kulira kwa kulapa ndi chikhulupiliro.



Umenewu ndi umboni wakuti munthu wapulumutsidwa, kuonetsa kuti ntchito ya Mulungu yachitika mu mtima.



Ngati mtima wasinthika, mau a pamlomo amasinthikanso.



M’malo mwa malankhulidwe opusa ndi opanda nzeru a dziko lapansi komanso nyimbo zopanda pake za chisangalalo zochoka pa milomo, nyimbo yatsopano ya mayamiko kupita kwa Mulungu ndi mau a umboni wa Khristu amatuluka kuchoka mu mtima ndi mkamwa mokonzedwanso.



Pamene mtendere wodabwitsa ndi Mulungu komanso chimwemwe mwa Mzimu Woyera zidzadza mtima, matamando ndi mayamiko ndizo zotsatira zake.



Ngati wina aliyense anena kuti ndi Mkhristu, ndipo nyimbo imeneyi ya matamando ndi mayamiko kwa Mulungu sili pa mtima pake ndi pa milomo pake, china chake chikulakwika.



Munthu wotere ali nako kuvomereza kopanda pake kosakhala nacho chipulumutso, kapena sali pa chiyanjano ndi Mpulumutsi wake ndipo akuyenda monga mwa thupi osati Mzimu.



Mtima wake ukhoza kukhalabe ngati nthaka imene imabereka minga ndi mitungwi imene ikunenedwa ku Aheb. 6:8, imene takamba kale mu malonje athu.



Mukhozanso kuona kuti matamando ndi mayamiko opita kwa Mulungu amenewa akuperedwa pagulu komanso ndi mseri momwe.



Panali pagulu pamene wakhate anagwa pansi pamapazi a Yesu ndi kumpatsa Iye mathokozo; ndipo mlembi wa salmo akunena zokhudza nyimbo yake ya malemekezo kwa Mulungu, “ambiri adzaiwona.”



Ambuye akufuna ife timvomereze pamaso pa anthu (Mat. 10:32), ndipo zimenezi tingathe kuchitika m’njira zambiri, munthu payekha komanso ngati gulu.



Chomwecho, abwenzi okondeka, tikuyenera kukhalabe mu mathokozo ndi malemekezo kwa Mpulumutsi wathu wodalitsika pakutipulumutsa ndiponso kutidalitsa ife modabwitsa nthawi ino ndi kwamuyaya.



Tikuyenera kumuthokoza tsiku ndi tsiku komanso kumulemekeza Iye pafupipafupi, kuseri ndi pagulu pomwe.



Pamene anthu a Mulungu asonkhana pamodzi kulemekeza ndi kulambira Ambuye, tikuyenera kukhala nawo pamodzi, ndipo pamene asonkhana kulalikira uthenga, tisonkhane nawo pamodzi ndi kulola mau athu amveke mwa kulemekeza ndi kuchitira umboni wa Khristu, cholinga kuti “ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupilira Yehova” (Mas. 40:3)

Chimakhala chisonyezo choipa ngati anthu amene amati ndi Akhristu akusowa mu misonkhano ngati imeneyi, ndipo ali otanganidwa ndi zinthu za dziko lapansi kapena kungokhala kunyumba.



Ambuye atipatse tonse kuti tikhale othokozabe kwa Iye pa zonse zimene watichitira komanso akutichitira ife, ndipo kuti tikamangilirikebe mu malemekezo ndi matamando kwa Iye.Tiyeni tipange mau a mlembi wa salimo kukhala chotitsogolera “Koma ine …… ndipo ndidzaonjeza kukulemekezani” (Mas. 71:14).



4. WOLENGEDWA WATSOPANOMutu wa phunziro lathuli ukupezeka m’mau awa: “Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano” (2 Akor. 5:17).



Ndime imeneyi ikutanthauza kuti iye amene walandira Khristu monga Mpulumutsi wake ndipo ali ndi chipulumutso cha Mulungu mwa Khristu monga mwa kuima ndi kupezeka kwake pamaso pa Mulungu.



Iye anavomerezedwa ndi Mulungu mwa Khristu, wokondedwayo (Aef. 1:6), ndipo ali “odzadzidwa mwa Iye” (Akol. 2:10).



Mulungu amaona wotereyu monga wangwiro mwa Khristu ndi wovekedwa chilungamo cha Mwana wake (Aroma 3:22; Afil. 3:9).



Limeneli ndilo tanthauzo lake lakukhala “mwa Khristu.”



Amenewa ndiwo malo atsopano pamaso pa Mulungu.



Tisanavomereze Khristu ndi kupulumutsidwa, Mulungu anationa ife m’machimo athu pansi pa Adamu wakugwa monga mutu wathu, ndi kukhala pansi pa kutsutsika mwa iye.



Tsopano pakukhala mwa chikhulupiliro mwa Khristu, malo athu pamaso pa Mulungu ndi osinthika.



Ife sitikuonekanso m’machimo athu, koma mu chilungamo changwiro cha Khristu.



Amenewa ndiwo maimidwe athu atsopano pamaso pa Mulungu.

Komatu chipulumutso cha Mulungu chimabweretsa zambiri kwa ife koposa kuima kwatsopano kwangwiro pamaso pa Mulungu mwa Khristu – zodabwitsa zimenezi.



Chomwecho ndime yathu ikunena, “Ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano”



Inde, ife tapulumutsidwa, tasanduka anthu osinthika – ife takhala anthu atsopano.



Muli chilengedwe chatsopano mwa ife komanso malo atsopano pamaso pa Mulungu.



Chimenechi ndi chimodzi mwa zinthu zodabwitsa zimene zimatsatira chipulumutso chimene munthu amalandira kuchokera kwa Khristu.



Wokhulupilira mwa Khristu amapangidwa kukhala wolengedwa watsopano mwa Iye.



Iye wasandulidwa ndi kukonzedwa, kutanthauza kusinthika ndi kupangidwa watsopano.



MOMWE KUSINTHA KUMACHITIKIRA





Mwina mungathe kukhala odabwa momwe kusintha kumeneku kumachitikira, komanso momwe kulili, kuti pamene munthu akhala mkhristu, iye ndi wolengedwa watsopano, pakuti kunja amakhalabe chimodzimodzi m’maonekedwe monga analili asanatembenuke mtima.



Chilengedwe chatsopano ndi chinthu chimene chimachitika mkati komanso mwa uzimu, osati kunja komanso mwa thupi, ngakhale kuti kusintha kwa mkati tsopano kumaonekera kunja ndi m’chikhalidwe.



Zimenezi zikuoneka kuchokera m’mau a Ambuye ku Ezekieli kumene kutembenuka kwa fuko la Israeli kukuloseredwa, ndipo akuperekanso mfundo ya kutembenuka kwa munthu payekha: “Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga mkati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wa mwala mthupi, ndi kukupatsani mtima wa mnofu. Ndipo ndidzaika mzimu wanga mkati mwanu, ndi kukuyendetsani m’malemba anga; ndipo mudzasunga maweruzo anga ndi kuwachita” (Ezek. 36:26,27).



Umu ndi momwe timakhalira wolengedwa watsopano mwa Khristu.



Mulungu amamupatsa wochimwa wolapa mtima watsopano komanso mzimu watsopano; Iye amaika mwa ife Mzimu wake ndi kulemba malamulo ake m’mitima mwathu (Aheb. 10:16), kotero kuti tikakhale ndi chikhumbokhumbo chabwino mkati mwathu kuchita chifuniro cha Mulungu ndi kumusangalatsa Iye.



Monga mtumwi Petro akutiuzira ife, tinapangidwa “kukhala oyanjana nawo umulungu wake” (2 Pet. 1:4).



ife timalandira chilengedwe chatsopano pa kutembenuka, kapena kubadwa kwatsopano, ndipo chimenechi ndi chikhalidwe cha Mulungu – chikhalidwe cha umulungu.



Chikhalidwe chakale cha uchimo chimakhalabe pomwepo, pamene timapeza (Aroma 7:20-23), chikhalidwe china chikuperekedwa kwa ife chimene chimakonda Mulungu ndi kudana ndi uchimo.



CHISONYEZO CHA KUSINTHA KOWONEKA NDI MASO



Kunena kuti zakale zapita ndipo zonse zasanduka zatsopano pa kutembenuka.



Zikhumbokhumbo zakale za uchimo, maganizo komanso zizolowezi tsopano zimatsutsana ndi chikhalidwe chatsopano chokhala mkati, ndipo zikuthetsedwa ndi chikhalidwe chatsopano komanso maganizo amene amauka m’moyo kuchokera mu chikhalidwe chatsopano ndi cha umulungu.



Zinthu zimene mumazikonda tsopano mumadana nazo, ndipo zinthu zimene mumadana nazo tsopano mumazikonda.



Chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m’mitima mwathu mwa Mzimu Woyera amene wapatsidwa kwa ife” (Aroma 5:5), ndipo ife timukonda amene anatikonda poyamba ndipo sitilinso okopeka ndi dziko lapansi limene limakana wachikondi wathu watsopano.



Amenewa ndiwo magwiridwe ntchito a chikhalidwe chatsopano cha umulungu, komanso chisonyezo cha kubadwa cha iye amene wasanduka chilengedwe chatsopano mwa Khristu; chimenechi ndi chomwe chimatsatira chipulumutso mwa Iye.



Tsopano, wokondeka muwerengi wachinyamata, kodi sukuganiza kuti pamene ife tavomereza kuti tapulumutsidwa ndi kudzitchula tokha Akhristu, nkhani yathu yakukhala wolengedwa watsopano ikuyenera kutsutsa mitima yathu, ndi kutipangitsa ife kufufuza ndi kuona ngati miyoyo yathu ikuonetsera kuti ndifedi otero?



Ngati munthu wapulumutsidwadi, iye ndi wolengedwa watsopano, ndipo chisonyezo chotsatira cha chipulumutso cha Mulungu chidzaonekera m’moyo mwake.



Tiyeni tionetsetse kuti miyoyo yathu ikuonetsera mfundo yakuti ndife olengedwa atsopano, anthu atsopano, komanso Akhristu enieni.



Ngati wina anena kuti ndi Mkhristu ndipo palibe chisonyezo cha kusintha kwa mtima ndi moyo wake, popanda umboni wakuti iye ndi wolengedwa watsopano, popanda kusiyanitsidwa ndi anthu a m’dziko osapulumutsidwa, umboni wake ulibe phindu ndipo choonadi chake chikhoza kukhala chokaikitsa.



Ngati munthu ali ndi chipulumutso mwa Khristu, pali zinthu zooneka ndi maso zimene zimatsatana nacho chipulumutsocho.



Tiyeni tikumbukire mfundo yodabwitsa imeneyi m’malingaliro mwathu, potero, kuti ife tinapulumutsidwa ndi Khristu, ndife olengedwa atsopano ndipo pamenepo chimakhalira ife kuonetsera zimenezi m’mayendedwe athu, m’malankhulidwe athu, ndi mnjira zathu, kukumbukira kuti kwa ife zinthu zakale za kuthupi ndi za m’dziko lapansi zinapita ndipo zonse zasanduka zatsopano. 5. KUKHAZIKIKA KWA MZIMU WOYERA



ife timalankhula za mfundo ya munthu aliyense wopulumutsidwa kukhala wolengedwa watsopano mwa Khristu Yesu komanso momwe kusintha kumeneku kumachitikira ndi Mulungu kumupatsa wokhulupilira chikhalidwe chatsopano cha umulungu ndi kuika Mzimu wake mkati mwake.



Tiyeni tionenso mfundo yomalizayi mwatsatanetsatane, pakuti choonadi cha Mkhristu kuti mwa iye mukhale Mzimu wa Mulungu ndicho chimodzi mwa zinthu zosiyanitsa zimene zimatsatira ndi chipulumutso.



Ntchito yonse ya kutembenuka ndi kubadwa kwatsopano m’moyo imakonzedwa ndi Mzimu Woyera, ndipo zinthu zonse zimene zimatsatana ndi chipulumutso ndi zotsatira za ntchito ya Mzimu Woyera mkati mwathu.



Ali Iye amene anatifulumiza kapena kutitsitsimutsa ife pamene tinali akufa m’machimo athu ndi kusasamala zokhudza chipulumutso cha moyo wathu (Yoh. 6:63; Aef. 2:1).



Anali Mzimu amene anatitsutsa ife za machimo athu ndi kutipanga kuzindikira kuti tikufunika Mpulumutsi, analinso Iye amene anapangitsa mitima yathu yosautsika kuyang’ana Khristu pa mtanda monga Mpulumutsi, ndi kupeza mtendere ndi mpumulo mu ntchito yake yotsirizika ya chiombolo (Yoh. 16:7-15).

Mzimu yemweyu anatipangitsa ife kumvetsetsa Malemba ndi kutipanga ife kukhala obadwa kwatsopano “mwa Mau a Mulungu”, ndipo anatipatsa ife chitsimikizo cha chipulumutso kuchokera mu chinsinsi cha umulungu chomwecho (Yoh. 3:3-8; Yoh. 5:13).



Kugawira kwa chilengedwe chatsopano pa nthawi ya kubadwa kwatsopano kunakonzedwanso ndi Mzimu wa Mulungu (Tito 3:5).



Kenako, pamene uthenga wa chipulumutso chathu unakhulupiridwa ndipo Khristu anakhulupiridwa kwathunthu ngati Mpulumutsi, Mzimu anatenga malo ake m’mitima mwathu ndipo tinatsindikizidwa chizindikiro cha Mzimu Woyera wa lonjezano (Aef. 1:13).



Kukhala kwa Mzimu woyera mwa okhulupilira, m’modzi wa anthu atatu a umulungu, kunalonjezedwa ndi Ambuye ku Yohane 14:17 ndipo kunakwaniritsidwa patsiku la Pentekoste, monga mwa kulembedwa ku Machitidwe.



Kumene mtumwi Paulo anauza Akhristu ku Korinto, kuti matupi awo ndi kachisi wa Mzimu Woyera amene amakhalira mwa iwo (1 Akor. 3:16; 6:9).



KODI MZIMU AMAKHALA MWA IFE NTHAWI YANJI?

Anthu ena amaphunzitsa kuti ife sitikhala ndi Mzimu Woyera pamene tangotembenuka mtima kumene, koma tikuyenera kukhala ndi nthawi ina yapadera yolandira Mzimu Woyera.



Tiyeni tiganizire mfundo imeneyi mwa kamphindi.



Paulo analembera Agalatiya, “Mulungu anatumiza Mzimu wache alowe m’mitima yathu, wofuula Abba, Atate” (Agal. 4:6).



Ndime imeneyi ikuonetsera poyera kuti aliyense amene angaitane Mulungu Atate wake, umboni ulipo wakuti iye ali nawo Mzimu Woyera kukhalira mwa iye, pakuti munthu angathe kuchita izi mwa Mzimu.



Chomwechonso, munthu aliyense amene akudziwa motsimikizika kuti ndi mwana wa Mulungu, amawonetsera kuti Mzimu Woyera amakhalira mwa iye, chifukwa ndi mwa Mzimu yekha kuti chitsimikizochi chidziwike (Aroma 8:15,16; 1 Yoh. 5:10).



Ndipo tikaona ku Machitidwe 10 timapeza okhulupilira Amitundu oyamba akulandira Mzimu Woyera pamene amamvetsera Petro akulalikira zokhudza kukhululukidwa kwa machimo mwa chikhulupiliro cha mwa Yesu Khristu.



Panthawi imeneyo iwo anapulumutsidwa, ndipo analandira Mzimu Woyera popanda kuchedwa kulikonse pamene anakhulupilira uthenga wolalikidwa kwa iwo. (ndime 44,45).



Chotero zili chomwechonso lerolino.



Chomwecho mfundo inakhazikika kuti wokhulupilira mwa Khristu, Mzimu Woyera amakhalira mwa iye pamene wakhulupilira uthenga wa chipulumutso, ndipo kuti mphatso ya Mzimu Woyera ndi zotsatira zodabwitsa za chipulumutso cha Mulungu.



Ndime yodabwitsa yotani imene yaperekedwa kwa ife komanso ulemu ndi cholowa kukhala ndi mlendo wakumwamba wotere kukhalira mwa ife!

ZOTSATIRA ZA MZIMU KUKHALIRA MWA IFE



Pali zinthu zambiri zimene Mzimu Woyera amachita mkati mwathu komanso kwa ife, koma pano tikhoza kutchulapo zochepa.



Ambuye analankhula za Iye monga “Mtonthozi” ku Yohane 14, kapena “Parkletos” kutanthauza kuti “munthu wosankhidwa kuthandizira zochitika zathu.”



Zimenezi, Iye amafunitsitsa kutichitira ife, ngati tingamulore kutero.



Ifetu tikuyenera kumulola Iye kuti alamulire miyoyo yathu, ndi kutsogozedwa ndi Mzimu ndi kuyenda monga mwa kutsogolera kwake.



Imeneyi ndi njira yokhayo ya chisangalalo komanso ya moyo wa Chikhristu wopambana.



Mzimu Woyera ndi mphamvu ya njira ya Mkhristu.



Iye amatilimbikitsa ndi mphamvu mkati mwathu (Aef. 3:16), ndipo amatipangitsa ife kupha machitachita a chikhalidwe chathu cha uchimo ndi kukhala ndi chigonjetso pa mayesero a uchimo (Aroma 8:13; Agal. 5:16).



Komatu pa chimenechi ife tikuyenera “kuyenda mu Mzimu,” kapena kuchita monga Iye akutiuzira kuti tisamkhumudwitse, apo ayi sitidzaona mphamvu yake ya kupereka ndi kulimbikitsa.



Iye adzatipatsa mphamvu ndi kutilimbikitsa ife pakutumikira Khristu.



Ntchito ina yodabwitsa ya mzimu ndi kutulutsa mkati mwathu chipatso cha magawo asanu ndi anayi a chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiliro, chifatso ndi chiletso – zonsezi pamodzi zimatchedwa “chipatso cha Mzimu” ku Agalatiya 5:22.



Ngati ife tikhala pansi pa utsogoleri wa Mzimu umene ukhala mwa ife ndi kumvera Iye, adzapangitsa chisomo chodabwitsa kuonekera m’miyoyo yathu.



Komatu pa zonsezi, tikuyenera “kudzadzidwa ndi Mzimu,” monga akutiuzira ku Aefeso 5:18.



Zimenezi zikutanthauza kuti kulola Mzimu kupeza njira mwa ife, kuchotsa uchimo ndi kudzikonda mwa mphamvu yake cholinga kuti Iye akakhale mwa ufulu mbali zonse za umunthu wathu ndi kupezeka kwake kodalitsika.



Umenewu ndi moyo weniweni ndiponso woyenera wa Mkhristu.



ZISONYEZO ZOONEKERA



Kunena zoona mphatso ya Mzimu Woyera ndiyo chotsatira chachikulu ndi chabwino cha chipulumutso, sichoncho kodi?



Ndipo ngati ife tipeza mphatso yaikulu imeneyi, miyoyo yathu ikuyenera kuonetsera zisonyezo mu ntchito ndi umboni wa kupezeka kwake.



Ifetu tikuyenera kukhala miyoyo yodzadzidwa ndi Mzimu komanso yotsogozedwa ndi Mzimu, ndi kukhala ndi chipambano pa tchimo lokhala mkati mwathu.



Zisomo zisanu ndi zinayi zimene zimapanga chipatso cha Mzimu zikuyenera kuonekera mwa ife ndipo mayendedwe athu aperekere umboni kuti ife tikutsogozedwa ndi Mzimu amene amakhala mkati mwathu.

Tiyeni tionenso nkhani imeneyi motsimikizika ndi mwakhama.

Kodi sitikulemekeza mlendo wathu wakumwamba, wokhalira mwa ife posaganizira za Iye, kapenanso osadalira pa Iye kuti atitsogolere ndi kusamalira zinthu zathu komanso kutithandiza ife mu zinthu zonse?



Ngati ife tisamalira zinthu za chikhalidwe cha uchimo ndi kuyenda monga mwa thupi, kodi sitikuika Mzimu Woyera kumbali?



Pamene tidzimitsa chikhumbokhumbo chake ndi kutsamwitsa mau ake mkati mwathu, ndi kuchita zinthu zimene zili zosamusangalatsa Iye, kodi pamenepo ife sitimukhumudwitsa ndi kumunyozetsa Iye?



Pamenepodi timamukhumudwitsa ndi kumunyozetsa.



Chiyani?” mtumwi akunena, “kapena simudziwa kuti thupi lanu lili kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali, chifukwa chake lemekezani Mulungu m’thupi lanu.” (1 Akor. 6:19,20).



Onetsetsani mfundo imeneyi “ndipo simukhala a inu nokha” ikulumikizana ndi mfundo ya Mzimu Woyera kukhala mwa ife.



Zimenezi zikuonetsera kuti ife tilibe ufulu wakuchita monga tifunira, koma tizindikire kuti ndife ake a Mulungu ndipo tilole Mzimu Woyera atitsogolere.



Kodi inu muchita zimenezi?



Ambuye atithandize tonse kuchita zimenezi.



Ngati mukufuna kuphunzirabe kapena thandizo lokhudza mutu umenewu mukupemphedwa kuwerenganso buku lotchedwa “Umunthu ndi Ntchito za Mzimu Woyera,” limenenso tikupezeka nalo.

6. PEMPHERO



Mitu yapitayi takhala tikukamba za chilengedwe chatsopano komanso mlendo wakumwamba, Mzimu Woyera, amene wokhulupilira mwa Ambuye Yesu Khristu amalandira akapulumutsidwa.



Tsopano tiona phunziro lokhuza pemphero, kusefukira kwa chilengedwe chathu chatsopano komanso imodzi mwa ntchito ya Mzimu wa Mulungu wokhalira mwa ife.



Ndipo pakusungabe dzina lathu, tikhoza kunena kuti pemphero ndi chimodzi mwa zinthu zofunikira kwambiri zotsatira chipulumutso.



Ku Machitidwe 9 timawerenga za kutembenuka ndi chipulumutso cha Saulo wa ku Tariso.



Mulungu anauza Hananiya kupita ndi kukafufuza Saulo, “pakuti taona ali kupemphera” (ndime 11).



Chokhacho kuti Saulo amapemphera unali umboni wa kusintha kwakukulu mu mtima wa munthuyu wozunza otsatira Khristu.Zinaonetsera chikhalidwe chenicheni cha kutembenuka ndipo zikutchulidwanso ndi Ambuye mwini, kuonetsera pamenepo kuti pemphero ndi lamphamvu, chotsatira cha ntchito ya Mulungu ya chipulumutso mu mtima.



Tikunena za pemphero lenileni lochokera pansi pa mtima osati mapemphero wamba, mapemphero opanda moyo.

Chomwecho tikhoza kulankhula molondola kuti pemphero ndi chimodzi mwa zofunikira zimene zimatsatira chipulumutso mwa Khristu, ndipo likuyenera kuonekera mwa onse amene amavomereza kuti apulumutsidwa.



Kodi Pemphero ndi chiyani?



Funso ili lingathe kutipindulira ife mu kanthawi kochepa kakubweraka.



Pogwiritsa mau a munthu wina: “Pemphero ndi chisonyezo cha Mkhristu kudalira pa Mulungu. Ndiko kufooka kwa munthu pa kukangamirabe mu mphamvu yaikulu.”



Pemphero lenileni ndi chisonyezo chakukhala wopanda thandizo pawekha komanso kuzindikira mphamvu, chisomo ndi chikondi mwa Mulungu kubwerapo ndi kuthandizira.



Ndicho chisonyezo chakumva kusoweka, kaya kusoweka kwa ifeyo kapena ena, ndi kufunitsitsa Mulungu, wamphamvu yonse, kulowelera m’malo mwathu.



Zonsezi zikuoneka mu pemphero losweka mtima la Davide ku Masalmo 109: “Koma inu Yehova Ambuye, muchite nane chifukwa cha dzina lanu; ndilanditseni popeza chifundo chanu ndi chabwino. Pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi, ndi mtima wanga walaswa mkati mwanga…… Ndithandizeni Yehova Mulungu wanga: Ndipulumutseni monga mwa chifundo chanu” (ndime 21,22,26).



M’mau amodzi, pemphero ndiko kudalira pa Mulungu.



Zimenezi zikuoneka mu pemphero ili la Davide.



Ndipo chidaliro chotsamira pa Mulungu chimenechi ndi chibadwa cha chilengedwe chimene mwana wa Mulungu aliyense amakhala nacho.



Chomwecho pemphero ndi chikhalidwe chatsopano cha Mkhristu, chisonyezo chooneka ndi maso kusonyeza kudalira pa Mulungu.



Chikhalidwe chakale cha munthu wosakonzedwa ndi chodzidalira pachokha ndipo chimachita mosemphana ndi chikhalidwe chodalira cha chilengedwe chatsopano.



Chomwecho, pemphero lenileni ndi lachilendo ku zikhumbokhumbo za wosatembenuka mtima.



Pemphero Limafotokoza za Okhulupilira

Zoona zake, khalidwe la pemphero likuyenera kukhala loonekera kwa onse amene amadzitchula kuti ndi Akhristu obadwanso kwatsopano.



Chimenechi ndi chimodzi mwa zinthu zofunikira zimene zimatsatira chipulumutso.



Pemphero lakhala likutchulidwa kuti mpweya wa moyo wa uzimu.



Pamene mwana wabadwa m’dziko lino lapansi, timayembekezera kuti azipuma.



Ngati mwanayo sakupuma, timadziwa kuti mwa iye mulibe moyo.



Chimodzimodzi, ngati munthu anena kuti ndi wobadwa kwatsopano mu ufumu wa Mulungu, ife timaonera kupuma kumeneku kwa mpweya wa pemphero.



Ngati pemphero lisoweka, ifetu tili ndi zifukwa zonse kukaikira za kupezeka kwa moyo wa uzimu mwa wotereyu.



Pemphero ndiko kuyanjana ndi Mulungu.



Popanda chiyanjano chimenechi, moyo wa uzimu sungathe kusungika ndi kukonzedwanso.



Tikamapemphera, timalankhula ndi Mulungu, ndipo pamene tiwerenga Mau ake, Baibulo, Iye amalankhula ndi ife.





Zonsezi ndi zofunikira pa chiyanjano ndi Mulungu, zimene chilengedwe chatsopano chimafuna pa chakudya chake ndi chilimbikitso.





Pamene tikufunikirabe kupuma mpweya kuti tikhale ndi moyo wa kuthupi, chotero ife tikufunikira kupuma mpweya wa pemphero kuti tikhalebe ndi moyo wa uzimu.





Baibulo lonseli komanso mnyengo zonse zakale, pemphero lakhala likudziwika ndi anthu a Mulungu.



Mtumiki wamkulu wa Mulungu, Ambuye Yesu Khristu, anali munthu wa pemphero.



Iyeyo payekha anali pemphero (Mas. 109:4).



Nthawi yochuluka amakhala akuoneka m’mapemphero mu mauthenga, nthawi zina kupemphera usiku onse, ndiponso nthawi zina amauka m’bandakucha ndi kuyamba kupemphera.



Tsopano ngati Iye anafunikira kukhala m’pemphero pafupipafupi, nanga ife koposa kotani?



Mu zonsezi Iye anatisiyira chitsanzo, “kuti mukalondole mapazi ake” (1 Petro 2:21).



Pemphero la Chizolowezi



Pamene Baibulo likutiuza ife “kupemphera kosaleka” (1 Ates. 5:17), komanso kulimbikabe “chilimbikire m’kupemphera” (Aroma 12:12) – kutanthauza kuti tikhalebe m’chikhalidwe cha pemphero, ndipo tipemphere paliponse komanso nthawi zonse – Malemba akutiphunzitsanzo kukhala ndi nyengo zokhazikika za pemphero.



Mlembi wa Masalmo Davide analankhula, “Madzulo, m’mawa, ndi masana ndidzadandaula, ndi kubuula, ndipo adzamva mau anga” (Mas. 55:17).



Iye analankhulanso, “M’mawa Yehova mudzamva mau anga; m’mawa ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira” (Mas. 5:3).



Ndipo za Danieli, mneneri, kunalembedwa kuti iye “anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse” (Dan. 6:10).



Zimenezi ndi zitsanzo zabwino kwa ife, ndipo tidzichita chimodzimodzi kusamalira chizolowezi cha nyengo za pemphero komanso kuyamika ndi Mulungu wathu m’malo athu a mseri.



Ine ndikunena kuti “kusamalira chizolowezi” cha pemphero, pakuti ife tikuyenera kukonza chizolowezi chabwino cha uzimu – komanso zizolowezi zina zabwino – ndipo pemphero likhale chimodzi mwa izo.



Nthawi zokhazikika za pemphero tsiku lililonse, monga anachitira Davide ndi Danieli, ndi zofunikira ku moyo wathanzi wa Chikhristu, koma nyengo yofunikira kwa onsewa ndi nyengo ya pemphero la m’mawa.

Tionetsetse kuti tayamba tsiku ndi Mulungu mu pemphero, monga umo mlembi wa masalmo ananenera kuti iye atero.



Popanda pemphero la m’mawa limeneli, munthu sangathe kukhala moyo wa Chikhristu wachipambano.Pakati pa anthu ambiri amene amanena kuti ndi opulumutsidwa ndipo ali ake a Ambuye, pemphero la m’mawa limasoweka mwa iwo.



Anthu ambiri anandiuza nditafufuza za izi, kuti iwo amapemphera usiku okhaokha basi pamene akufuna kugona.



Nzosadabwitsa kuti iwo amagonjetsedwa pa moyo wawo wa Chikhristu ndipo sachita bwino, pakuti iwo samayang’ana kwa Mulungu mu pemphero kuti awathandize pamene tsiku likuyamba.Wokondedwa muwerengi, musaiwalire nthawi yanu ya kum’mawa ya pemphero.



M’buku lolemba zochitika za patsiku la mnyamata wina, amene patsogolo anakhala munthu wodziwika pa zochitika, anapezamo mau awa amene amamutsogolera tsiku lililonse: “Kusukusula, pemphero, Baibulo ndi chakudya cha m’mawa.”

Amenewa anali machitidwe ake a tsiku ndi tsiku.



Tiyeni amenewa akhalenso machitidwe athu.



Tiyeni tipange pemphero kukhala chizolowezi cha khalidwe la miyoyo yathu ndi kuyetsetsa kupezeka pa misonkhano ya mapemphero a Chikhristu ndi kupanga mau athu kumveka pa mapemphero a pagulu.



Zambiri zikhoza kunenedwa zokhudza pemphero, koma titseka nkhani imeneyi ndi ndime zotsatirazi kuchokera mu nyimbo yotchedwa “Kodi Munaganizako Kupemphera?”



Choyamba munatuluka mnyumba mwanu lero m’mamawa,

Kodi munaganizako kupemphera?

Mudzina la Khristu, Mpulumutsi wathu.

Kodi munapempha kukonderedwa,

Ngati chishango chanu lero?



Pemphero limapereka mpumulo kwa othodwa!

Pemphero lidzasintha usiku kukhala usana:

Pamene moyo ukuoneka wa mdima ndi wopweteka,

Musaiwalire kupemphera.

7. KUDYA PA MAU A MULUNGU



Kulumikizidwa chifupi ndi pemphero, monga chotsatira cha chipulumutso cha Mulungu, ndiko kukonda Mau a Mulungu ndiponso kudya mauwo.



Pemphero komanso kulingalira malemba zimayendera limodzi ndipo sizikuyenera kulekanitsidwa.



Pemphero lopanda Mau a Mulungu limatitsogolera ku chisokonekero, ndipo kuwerenga Baibulo popanda pemphero kumatitsogolera ku chidziwitso komanso mfundo yozizira.

Mtumwi Petro akutiuza kuti, “lirani monga makanda a lero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nawo kufikira chipulumutso, ngati mwalawa kuti Ambuye ali wokoma mtima” (1 Petro 2:2,3).



Ndichilengendwe kwa khanda kuti akafune mkaka kuti ukulitse moyo wake watsopano.



Mwachikhalidwe amafuna kena kake kuti adye, ndipo chikhumbokhumbo chake pa chakudya chimakhala chachikulu.



Chimenechi ndi chisonyezo cha moyo wa thanzi komanso chitsimikizo chotsatana ndi kubadwa kuthupi.



Pali chinthu chimodzi chokha chimene khanda limadya, ndipo chimenechi ndi mkaka umene nthawi zonse amaukakamira.



Chimodzimodzinso moyo wa uzimu.



Ngati talawa kuti Ambuye ndi wachisomo ndipo tabadwa kwatsopano, chilengedwe chathu chatsopano nthawi yomweyo chimakhumba chakudya kuti chikhale chathanzi ndi kukula.



Chilipo chakudya chimodzi chimene chimadyedwa, ndipo chimenechi ndi Khristu m’Malemba, mkaka weniweni wa Mau.



Mwana wakhanda wobadwa kumene m’banja la Mulunguyu amakhaladi ndi chikhumbokhumbo, ndipo ichi ndi chotsatira chotsimikizika cha moyo wa uzimu ndi chipulumutso.



Salmo lalitali m’Baibulo, Masalmo 119, likukamba za kufunitsitsa ndi kukhumba Mau a Mulungu kwa iye amene ali ndi moyo wakumwamba.



Iye amawabisa Mau mu mtima mwake, amakondwera ndi kulingalira pa iwo, amawatenga ngati uphungu wake, amalimbikitsidwa nawo, ndipo amalakalaka kuphunzitsidwa ndi kutsogozedwa nawo.



Yobu m’modzi wa atumiki akale akunena, “Ndasungitsa mau a pakamwa pake koposa lamulo langalanga” (Yobu 23:12).



Ndipo Mneneri Yeremiya akulemba: “Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine chikondwerero ndi chisangalalo cha mtima wanga” (Yer. 15:16).



Malemba amenewa, ndiponso ena ochuluka, akuonetsa kuti iwo amene ali a Mulungu nthawi zonse amapeza chisangalalo ndi chakudya cha uzimu pa kulingalira Mau ake.



Mau Ofunikira kuti Tikule

Ndime imene taona kumayambiliro yochokera ku Petro ikunena kuti tilire “mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nawo.”



Chikhumbokhumbo chokhazikika cha moyo, kaya wathupi komanso wauzimu, ndiko kukula ndi kutukuka, ndipo pa chifukwa chimenechi moyowu umafunika chisamaliro.



Chomwecho moyo wa umulungu wa mwana aliyense wa Mulungu umakhumba chisamaliro kuti ukule ndi kutukuka kukhala munthu wamkulu mwa Khristu.



Zimenezi zikupezeka m’Mau a Mulungu; mwa moyo wochokera kwa Mulungu umakula.



Ambuye akulankhula molunjika kuti moyo wa umulungu si mkate, “koma ndi mau onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu” (Mat. 4:4).

Chimenechi ndi chomwe Malemba Oyera ali, “Owuziridwa ndi Mulungu” (2 Tim. 3:16); komabe amachokera m’kamwa mwa Mulungu, ndipo amasamalira moyo wochokera kwa Mulungu ndi kupangitsa moyowo kukula.



Ife timafunikira malemba kuti chikhalidwe chathu chatsopano chikhale chochitachita ndi kukwaniritsa cholinga chake kuti chidye pa Mau a Mulungu ndi kuti pamenepo chikakule.



Tikuyenera mwachizolowezi chikhalidwechi kuchipatsa chakudya chakumwamba cha Khristu Yesu m’Malemba, monga umo timadyetsera pafupipafupi moyo wathu wathupi ndi chakudya chadziko lapansi.

Tionetsetse kuti tili ndi nyengo zoikika tsiku lililonse kusonkhanitsa chisamaliro cha miyoyo yathu kuchoka m’Baibulo, cholinga kuti moyo wa umulungu mkati mwathu ukhale ukukonzedwanso tsiku ndi tsiku, kulimbikitsidwa ndi kusamalidwa mwakukula mwa Khristu Yesu.



Kwa Israeli wakale, Mulungu anapereka chithunzithunzi chokongola komanso chitsanzo cha kudyetsa kwa uzimu kumeneku pa Khristu.



Iwo amadutsa m’chipululu momwe munalibe chakudya, ndipo Mulungu anawatumizira manna kuchokera kumwamba tsiku lililonse (Eks. 16).Iwo amatuluka kunja ndi kukatola manna m’mawa ulionse dzuwa lisanatenthe, munthu aliyense monga mwa njala yake.



Pa chakudya chakumwamba chimenechi iwo anadya, ndipo anasamalidwa m’nyengo yonse ya ulendo wa zaka makumi anayi wa m’chipululu.



Ifenso tikudutsa m’chipululu momwe mulibe chakudya cha miyoyo yathu, kupatula chimene chachokera kumwamba, chimene ndi Mau a Mulungu.



Zonse zimene zili m’dziko lapansili ndi chakudya cha munthu wathupi ndipo sichingadyetse moyo.



M’Malemba timapeza Khristu, mkate weniweni komanso wamoyo ukutsika “kumwamba iye wakudya mkate umenewu adzakhala ndi moyo nthawi zonse” (Yoh. 6:32-58).

Manna akumwamba amenewa amapezeka m’mawa ulionse, kuchokera kwa Mulungu, ngati ife tipita ku Mau okha ndi kuwasonkhanitsa mwa pemphero ndi kudalira pa Mzimu Woyera.

Ndipo m’mawa ulionse ife tikufunika kudya manna amenewa, ngati tikufuna “kukula m’chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu” monga 2 Petro 3:18 akutiuzira ife.



M’mawa ulionse chikhalidwe chathu chatsopano chimakhala ndi njala ya chakudya cha Mau a Mulungu ndipo chimafunitsitsa kulingalira pa Mauwo.

Chomwecho, ngati munthu wapulumutsidwadi, chikhumbokhumbo cha Malemba Oyera chikuyenera kuonekera m’moyo mwake; chimenechi ndi chimodzi mwa zinthu zimene zimatsatira chipulumutso mwa Khristu.





Zilakolako Zosemphana



Wokondedwa muwerengi wachinyamata, kodi chisonyezo cha zotsatira za chipulumutso chikuoneka ndi kuchitachita m’moyo mwako?



Kodi umakonda Mau a Mulungu, ndi kukhala ndi njala ya chakudya chake?



Ngati zimenezi zikusoweka m’moyo mwako, pali china chake chikulakwika.



Mwina mwake muli ndi chilakolako chosemphana, chosokonezedwa pakudyetsa dziko lapansi koposa Khristu, cholinga kuti tsopano mukangamire zinthu zimenezi koposa umo muchitira ndi zinthu za mtengo wapatali za Mulungu.



Inutu mumadziwa momwe chilakolako cha chakudya chabwino cholimba chimasokonezedwa pamene tidya maswiti ndi zotafunatafuna zimene zili ndi phindu lochepa la chakudya.



Zimenezi ndi zoonanso mu uzimu.



Petro akuti tisanalire mkaka woyenera, wopanda chinyengo wa Mau, titaye “choipa chonse, ndi chinyengo chonse ndi maonekedwe onyenga ndi kaduka ndi masiliro onse” (1 Pet. 2:1,2).



Zimenezi ndi zinthu zomwe zingachotse chilakolako ndi chisangalalo cha Mau a Mulungu ngati tingaziyike ndi kuzisunga mu mtima.



Ngati umu ndi momwe ulili pano, wokondeka mzanga, tembenukira kwa Mulungu m’kulapa ndi kudziweruza wekha ndi kumufunsa Iye kuti adyetse moyo wako ndi manna atsopano.

Bwerani kwa Iye m’Mau ake tsiku lililonse ndi kudya mu msipu wobiriwira kumadzi odikha ndipo muone kukondwa komanso kulimbika kumene mudzakhala nako mkati mwanu komanso m’moyo wanu wa Chikhristu.



Pomaliza, tiyeni tione mau a Yehova kupita kwa Yoswa, amenenso ndi mau opita kwa ife: “Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiliremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru” (Yos. 1:8).



8. UBATIZO

Tikamaona machitachita a umulungu m’Malemba a Akhristu oyambilira komanso a Mpingo wa atumwi, timaona kuti ubatizo wa madzi ukulumikizika pafupi ndi chipulumutso cha miyoyo.



Osati kuti zikukhuzana ndi chipulumutso cha munthu payekha, komatu zimatsatana kwambiri ndi kutembenuka kwa munthu payekha.



Chomwecho, ife tikhoza kulankhula molondola kuti ubatizo ndi chimodzi mwa zinthu zofunika zimene zimatsatana ndi chipulumutso.

Utumiki wa Ambuye

Poyamba, tikuona kuti pamene Ambuye anatsala pang’ono kukwera kumwamba, Iye anauza ophunzira ake kuti apite padziko lonse lapansi kulalikira uthenga wabwino kwa olengedwa onse; kenakonso analankhula, “Amene akhulupilira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupilira adzalangidwa” (Marko 16:15,16).



Pamenepa tikuona momwe Ambuye Mwini akutchulira ubatizo molunjika potsatira kukhulupilira Uthenga ndipo ubatizowu ukukhudzana ndi chipulumutso.

Kuchokera m’Malemba ndi zoonekeratu kuti ubatizo sumathandiza kalikonse pa chipulumutso; pakuti ndi mwachisomo komanso chikhulupiliro chokha kuti ife timapulumutsidwa osati mwa ntchito kapena chikonzero chathu (Aef. 2:8,9).



Koma ife tikapulumutsidwa, tibatizidwe monga Ambuye akutiuzira.



Mu nkhani yoperekedwa ndi Mateyu ya kukwera kwa Ambuye, ophunzira akuuzidwa kuti apange ophunzira a mitundu yonse, ndipo awabatize iwo m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera (Mat. 28:19).

Ubatizo umatsatira pambuyo pa iwo kukhala ophunzira a Khristu.



Ubatizo wa chikhristu umayamba ndi utumiki uli pamwambawu wa Khristu woukitsidwa, osati ubatizo wa Yohane, kapena ubatizo wa Ambuye umene unachitika ndi Yohane, monga ena amaganizira.



(Ubatizo wa Yohane unali oloza ku kulapa, pamene ubatizo wa Chikhristu ndi oloza ku imfa ndi chiukitso cha Khristu, monga tidzaona mtsogolomu ku Aroma 6.)



Ndipo ubatizo ukupitilirabe kufikira kubwera kwa Ambuye nthawi yakutseka nyengo ya chisomo cha Akhristu.



Pakulumikizana ndi utumiki wa Ambuye monga mwa ubatizo pali lonjezano ili, “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano” (Mat. 28:20), kuonetsa kuti lamulo la ubatizo silinali chabe lokhudza nyengoyi, koma kuti likapitilire kufikira mapeto a nyengo ya chisomo. Ndiponso silinali la okhulupilira a Chiyuda, monga amaphunzitsira ena lerolino, koma ya ophunzira a mitundu yonse mu nyengo yonse ya Chikhristu.

Akhristu Oyambilira



Mwachidule tiyeni tione zochitika za ena mwa otembenuka mtima oyamba m’buku la Machitidwe, ndi kuona momwe ubatizo unali chinthu chotsatira chipulumutso chawo.



Patsiku la Pentekoste, pamene otsatira Khristu anabatizidwa ndi Mzimu wa Mulungu m’thupi limodzi (1 Akor. 12:13), pachiyambi pa Mpingo wa Mulungu, Petro analalikira kuuka ndi kukwezedwa kwa Yesu wopachikidwa ndipo anaitana ochimwa kuti alape ndi kubatizidwa m’dzina la Yesu: “Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu” (Mach. 2:41).



Pamene Uthenga unalalikidwa kwa Asamaliya, ambiri anakhulupilira ndipo anabatizidwa, amuna ndi akazi omwe (Mach. 8:12).



Kenako mdindo wa ku Aitiopiya anapeza mtendere wa mumtima mwa Yesu Khristu ndipo anafunsa kuti abatizidwe.



Chomwecho analowa m’madzi ndi Filipo ndipo anabatizidwa (Mach. 8:35-38).



Ndipo posakhalitsa timawerenga za kutembenuka mtima kwa Saulo wa ku Tariso komanso kubatizidwa kwake (9:18).

Ku Machitidwe 10 kuli nkhani ya Amitundu oyambilira amene anapulumutsidwa, Korneliyo ndi banja lake, ndipo pa ndime 48 tikuona Petro akuwalamulira iwo kuti abatizidwe m’dzina la Ambuye.

Pamutu 16 pali nkhani ya kutembenuka mtima kwa Lidiya ndi Mdindo wa ku Filipi ndipo tikupeza iwo akubatizidwa pamodzi ndi mabanja awo.



Chomwecho zinachitikanso chimodzimodzi pamutu 18 monga kwa Akorinto amene mtumwi Paulo anagwira ntchito pakati pawo.



Iwo anamva, nakhulupilira, ndipo anabatizidwa (ndime 8).



Kuchokera pa nkhani ili pamwambayi kuchokera m’Malemba zimvetsetseke kwa ife kuti njira ya umulungu ya okhulupilira mwa Khristu ili mu ubatizo.



Mapazi a njira ya Mpingo wa atumwi akuonekera ndi kusungika m’Mau a Mulungu kwa ife.

Ndipo ngati ife tifuna kuyenda mosangalatsa Mulungu, tikuyenera kutsatira mapazi omwewo ndipo tipezeke tikuchita monga iwo amachitira mu zinthu zonse.



Iwo anakhulupilira mwa Khristu, napulumutsidwa, ndipo kenako anabatizidwa m’dzina lake.



Tanthauzo la Ubatizo

Ifetu tikhoza kukhala olondola kufunsa kuti ndi chifukwa chiyani tikuyenera kubatizidwa.



Pofuna kudziwa chifukwa chake, ndi kofunika kumvetsetsa bwino tanthauzo ndi cholinga cha ubatizo wa madzi; komanso zina zambiri, pakuti pali ziphunzitso zosokonekera zambiri m’dziko lapansi pokhudza nkhaniyi.



Ena amaphunzitsa kuti ubatizo umatikonza ndipo umapangitsa munthu kukhala obadwa kwatsopano.



Ena amatenga ubatizo ngati njira ya chipulumutso, ndipo ambiri amaganiza kuti ndi njira yoperekera kwa Ambuye ana ang’ono, pamene ena amatenga ubatizo kukhala njira yowathandizira kukalowa ufumu wa Mulungu pamene ali padziko lapansili.



Koma tikuyenera kufunsa, “kodi Malemba akuti chiyani?”



Mau a Mulungu ndiwo mlozo wathu wabwino.



Ku Aroma 6 chiphunzitso komanso tanthauzo la ubatizo wa madzi zikufotokozedwa bwino.



Kupatula ku Agalatiya 3:27, Akolose 2:12 ndi 1 Petro 3:21 kumene akufotokoza mwachidule za ubatizo, ku Aroma 6:3-7 ndi malo okhawo m’Baibulo kumene akutiphunzitsa tanthauzo ndi cholinga cha ubatizo wa madzi: “Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yake? Chifukwa chake tinaikidwa m’manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa mu imfa; kuti monga Khristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemelero wa Atate, chotero ifenso tikayende m’moyo watsopano. Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi Iye m’chifanizidwe cha kuuka kwake; podziwa ichi kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo; pakuti iye amene anafa anamasulidwa ku uchimo.”

Kuchokera mundime zimenezi tikuphunzira kuti ubatizo ndi chisonyezo cha pagulu cha Khristu ndi imfa yake kwa ife.



Ndiko kuikidwa m’manda ndi Iye.



Kulowa m’madzi ndi kumizidwa ndiko “kufanizira imfa yake.”



Ndicho chithunzithunzi ndi chisonyezo cha imfa, imfa ya Khristu kutifera ife.



Munthu wobatizidwa amasonyeza kuti iye, ndi wochimwa, anayenera kufa, ndipo amaziika yekha mu chifanizo cha malo a imfa amene Khristu anatenga m’malo mwake, kuvomereza poyera pamaso padziko lapansi chikhulupiliro chake mu imfa ya Khristu pa machimo ake.



Munthu wochimwa wakale amaikidwa pamalo a imfa ndipo munthuyo amavomereza kuti “anafa ndi Khristu” (Aroma 6:8).

Ndipo kutuluka m’madzi pa ubatizo ndi chithunzithunzi cha kuuka komanso chivomerezo, kumbali ya ubatizo, kuti iye ndi wolengedwa watsopano mwa Khristu Yesu ndipo tsopano ayenda mwatsopano m’moyo wa Chikhristu.



Agalatiya 3:27 akuvomereza zimenezi: “Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu.”



Mu ubatizo wa mwa Khristu iwo anavomereza poyera kuti anagwiritsitsa Khristu, ndipo tsopano akuima mu chovala chatsopanochi komanso malo atsopano pamaso pa Mulungu, ndiponso kukhala ndi cholinga kuyenda m’moyo watsopano wa Khristu.



Chimenechi ndi chiphunzitso komanso kufunikira kwa ubatizo wa madzi.



Tsopano, Akhristu amzathu, ndikukhulupilira kuti mwatitsatira bwino kufikira pano mu kulingalira kwathu pa mutu wa ubatizo ndipo mwamvetsetsa zonse zimene tafotokoza.



Ngati simunamvetsetse, onaninso mwa pemphero Malemba amene takhala tikuona ndipo Mulungu akupatsani kumvetsetsa.

Ngati inu mukudziwa kuti munapulumutsidwadi ndipo ndinu wake wa Khristu, koma simunabatizidwe mwa Iye ndi muimfa yake, ndikupemphera kuti muonetsedwe kuti chimenechi ndicho chifuniro chake pa inu, ndi kupatsidwa mphamvu ndi cholinga cha mtima kuvomereza Khristu mu ubatizo.



Inutu mupezeke ndi chisonyezo chotsatana ndi chipulumutso m’moyo wanu wa Chikhristu ndi kutsatira mapazi a iwo amene anamvera Mau a Khristu m’masiku a atumwi ndipo anabatizidwa m’dzina lake la mtengo wapatali.Kenako, pamene ife tabatizidwa mwa Khristu, tikuyenera kukumbukira zimene ife tavomereza ndi kuyenda moyenera.



Ngati ife tiyenda monga mwa chikhalidwe chathu chakale cha uchimo ndi cha dziko lapansi, timasemphana ndi zimene tinavomereza pa ubatizo wathu.

Pamenepo ife tinavomereza kuti tinaikidwa m’manda ndi Khristu ndipo tchimo tinathana nalo, kuti munthu wathu wakale anapachikidwa ndi Khristu ndiponso kuti ife tinaukitsidwa ndi Iye kukayenda m’moyo watsopano wa chiukitso wosiyanitsidwa ndi uchimo.

Ifetu tikumbukire zimenezi nthawi zonse ndi kuyenda moyenera.

9. KUDZIPEREKA NDI KUMVERA

Pamene Saulo wa ku Tariso anaimikidwa panjira ya ku Damasiko ndi kuwala kwa Mulungu kochokera kumwamba, iye anagwa pansi, ndipo mau ochokera kumwamba analankula naye nati, “Ndine Yesu amene umlondalonda.”



Iye anayankha, “Ambuye kodi mukufuna ine ndichite chiyani?” (Mach. 9:6).

Imeneyi inali nyengo yake ya kutembenukira kwa Khristu, ndipo machitidwe ake ndi mau ake pa nthawi ya kutembenuka kwa moyo wake zikuonetsera kugonja kwake, kudzipereka kwake komanso kufunitsitsa kwake kumvera.



Saulo anamulankhula Yesu ngati Ambuye, kumene kuli kuzindikira za ulamuliro wake komanso chisonyezo kuti anadzipereka kwa Iye ngati Ambuye wake ndipo anali wofunitsitsa kumvera ndi kumtumikira Iye.

Mtima woterewu ndi malingaliro amenewa akuonetsera uthunthu wake pakutha pamoyo wake ndi kusintha kwakuya monga mwa maumboni a m’makalata ake.



Kugonjera kwa Khristu monga Mpulumutsi ndi kudzipereka komanso kumvera Iye ndicho chikhalidwe cha Chikhristu, pakuti dzina lakuti “Mkhristu” limatanthauza iye amene wakhala wotsatira komanso wophunzira wa Khristu.



Chomwecho, kumvera ndi kudzipereka kwa Khristu ngati Ambuye kudzionekera m’moyo wa Mkhristu.



Zinthu zimenezi zomwe zimatsatana ndi chipulumutso zipezeke mwa onse amene amadzitchula kuti ndi Akhristu, monga zinalinso mwa Paulo, chitsanzo cha Chikhristu, amene analankhula mwachisomo cha Mulungu, “Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Khristu” (1 Akor. 11:1).



Umbuye wa Khristu

Kodi munaganizirako kuti sitikuyenera kungovomereza kokha Khristu ngati Mpulumutsi wa machimo athu ndi chiweruzo, komanso timvomerezenso ngati Ambuye?



Inde, Munthu, Khristu Yesu, amene anafa pamtanda chifukwa cha machimo athu, waukitsidwa kwa akufa ndipo wakwezedwa malo a pamwamba kumwamba: “Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu” (Mach. 2:36).



Ndipo kwa Iye bondo lililonse lipinde komanso lilime lililonse livomereze kuti Iye ndi Ambuye (Afil. 2:9-11).



Iye amene ife tinamuvomereza ngati Mpulumutsi woperekedwa ndi Mulungu, ali yemweyo Mulungu anamupatsa malo a Umbuye pamwamba pa zonse, ndipo kwa Iye tikuyenera kugonjera ndi kumvera moyo wathu wonse.



Kumutenga Khristu ngati Mpulumutsi wathu ndi kutenga phindu lonse la ntchito yake ya pamtanda kwa ife, kenako nkulephera kudzipereka kwa Iye monga Ambuye wathu mwa kumvera konse, ndiko kusayamika komanso kudzikonda.



Inetu ndili ndi chiyembekezo chonse, kuti inu simulephera kuzindikira za Umbuye wa Mpulumutsi wanu, ndipo kuti mukamutenga Iye ngati Ambuye wanu komanso Mpulumutsi wanu.

Pakuti chimenechi ndi chimodzi mwa zinthu zapadera zimene zimatsatana ndi chipulumutso mwa Khristu, ndipo ife tikufunika tikadziwike nacho.



Kodi zimatanthauza chiyani kukhala naye Khristu monga Ambuye, ndipo zimakhudza chiyani?



Kuvomereza Yesu ngati Ambuye zimatanthauza kuti ufulu wake ndi ulamuliro wake pa ine zikuonekera ndipo kuti ndapereka chifuniro changa kwa Iye ndipo ndi kuyetsetsa kumsangalatsa ndi kumtumikira Iye.



Chimenechi ndi chizindikiritso cha choonadi cha 1 Akorinto 6:19,20, kuti ine sindikhala mwa ine ndekha, pakuti ndinagulidwa ndi mtengo wake wapatali,ndipo ndikhala chifukwa cha Iye.



Kukhaladi naye Khristu ndiko kumvera Mau ake ndi kuchita zinthu zimene Iye akutifunsa.



Zimenezi umboni wake ukupezeka kuchokera m’mau a Ambuye, “Ndipo munditchuliranji Ine, Ambuye, Ambuye, ndi kusachita zimene ndizinena?” (Luka 6:46).

Ngati ife timutchula Iye Ambuye, amayembekezera kuti tichite zimene Iye akufuna, ndipo zofuna zake zimafotokozedwa bwino m’Baibulo.



Muone momwe Paulo ndi Timoteo anakhalira ndi Khristu ngati Ambuye wao; iwo anadzitchula okha “Akapolo a Yesu Khristu” (Afil. 1:1).



Iwo anali akapolo okondeka a Khristu, tanthauzo la Umbuye wake linali lakuya m’miyoyo yawo, ndipo chikondi chake chinawapangitsa iwo kudzipereka okha kwathunthu kwa Iye mosakakamizidwa, podzipereka ku utumiki.



Zimenezi zikhale zoona kwa ife tonse.



Iye akuyenera kulandira kudzipereka kwathu konse komanso kumvera kwathu kwathunthu, utumiki wosakakamizidwa.



Zotsatira Zake



Mfundo ya kudzipereka ndi kumvera kwa Khristu monga Ambuye ikugwira kwambiri pa mitu yambiri yokhudzana ndi moyo wa Chikhristu.

Nkhani yokhudza ubatizo imene takhala tikuona pa mutu wapitawu, ndiko kuzindikira ulamuliro wa Ambuye pa ine komanso chisonyezo cha cholinga cha kumvera ndi kutumikira Iye.



Mafunso ochuluka amene amabwera, ngati tikuyenera kuchita ichi kapena icho ngati Akhristu, amayankhidwa mosavuta ndi mwachangu ngati tigwiritsa ntchito mfundo imeneyi ku mafunsowa.



Nkhani yokhudza kusokonezedwa, funso la kavalidwe, kagwiritsidwe ntchito ka nthawi yake ya munthu, luso komanso chuma cha kuthupi zonsezi zimapeza mayankho tikaziganizira mogwirizana ndi kudzipereka ndi kumvera Khristu Ambuye wathu.



Pakuseka nkhani yokhudza kudzipereka ndi kumvera kwa Ambuye, pali nkhani ina imodzi imene ndikufuna kuti muidziwe.



Chimenechi ndi chinthu chimodzi chimene Ambuye ndi Mpulumutsi wathu anafunsa za Iye mwini asanapachikidwe pa mtanda.



Timachipeza m’Mauthenga Abwino komanso ku 1 Akorinto 11:23-26.



Luka 22:7-20 akutionetsa momwe Iye anasonkhanitsira ophunzira usiku uja wa kuperekedwa kwake, komanso atamaliza kudya mgonero ndi iwo, ndipo anakhazikitsa chimene chimatchedwa “Mgonero wa Ambuye.”



Iye anatenga mkate, nayamika, naunyema, ndipo anawapatsa iwo, nanena, “Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa.”



Koteronso Iye anatenga chikho, nanena, “Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga; chitani ichi, nthawi zonse mukamwa, chikhale chikumbukiro changa. Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye” (1 Akor. 11:25,26).

Limeneli ndi lamulo la chikondi limene Ambuye akutifunsa ife kuchita pakukumbukira Iye ndi imfa yake ya chiombolo ya pa mtanda kufera ife.



Kodi ife tikumumvera Iye ndi kukwaniritsa lamulo limeneli?



Iye akufunitsitsa kuti ife tidye nawo Mgonero wa Ambuye nthawi zonse pakumvera lamulo lake lomaliza pakukumbukira chikondi chake cha kuimfa kwa ife.



Kodi ife tikuchita zimenezi?



Ngati Yesu ndi Ambuye wathu, tikuyenera kuchita monga mwa pempho lake ndipo limeneli ndi pempho lofunikira la Ambuye ndi Mpulumutsi wathu.

Malo sakutilola kulankhula mwatsatanetsatane za chikumbutso chodabwitsa chimenechi cha mgonero, chomwecho titseka ndi pemphero kuti tonse tichuluke m’kudzipereka ndi kumvera Yesu monga Ambuye wathu wokondedwa.



10. KUTUMIKIRA AMBUYE

Ife talankhula za kudzipereka ndi kumvera Khristu ndi kukhala naye ngati Ambuye wathu, kutanthauza kuchita zinthu zimene Iye akutifunsa ife kuchita ndi kumtumikira komanso kumsangalatsa Iye.



Tsopano tikaonjezera pa mutu wa kutumikira Ambuye ndi cholinga chofuka kuonetsera kuti ndi chimodzi mwa zinthu zofunikira zimene zimatsatana ndi kupeza chipulumutso mwa Khristu.



Kunena kuti imeneyi ndi mfundo ya Malemba zikuoneka ngakhale munthu atayang’ana mwachangu m’Chipangano Chatsopano.

Pamene Ambuye anaitana Simoni ndi Andreya, anati, “Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu” (Marko 1:17).



Pakumtsata Iye, iwo akhala naye Yesu ngati Ambuye wao, komatu Ambuye sakutanthauza kuti iwo akakhala naye popanda china chilichonse chochita.



Iwo anayenera kukhala antchito a Mbuye wao ndi kuweza miyoyo ya anthu.



Kutumikira Ambuye, kukhala asodzi ake, imeneyi inayenera kukhala ntchito yawo tsopano.



Iye asanakhomedwe pa mtanda, anauza ophunzira ake kuti “Monga ngati munthu wa paulendo, adachoka kunyumba kwake, nawapatsa akapolo ake ulamuliro, kwa munthu aliyense ntchito yake, nalamulira wa pakhomo adikire” (Marko 13:34).



Pa zimenezi Iye amatanthauza kuti akubwerera kupita kumwamba ndipo akusiya zinthu zake m’manja mwa anthu ake amene Iye amayembekezera kukhala antchito ake ndipo kuti aliyense akuyenera kugwira ntchito yake imene anapatsidwa ndi Mbuye wake pamene akudikira kubweranso kwake.



Chomwechonso, pamene Khristu anauka kwa akufa, anauza ophunzira ake, “Monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu” (Yoh. 20:21) komanso “Mukani kudziko lonse lapansi lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse” (Marko 16:15).



Kodi nanga Khristu anatumizidwa padziko lapansi kudzatani?



Iye anati, “Mwana wa Munthu sanadza kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la kwa anthu ambiri” (Marko 10:45).



Nthawi yina Iye analankhula, “Tiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine” (Yoh. 9:4).



Chomwecho ngati ife tatumizidwa padziko lapansi monga anatumidwa Khristu, tikuyenera ife titumikire ndi kugwilira ntchito Mulungu monga anachitira Iye.



Nthawi yomweyo atangotembenuka mtima, mtumwi Paulo analalikira Khristu m’sunagoge, kuti Iye ali Mwana wa Mulungu (Mach. 9:20).

Nthawi yomweyo, iye anayamba kugwilira ntchito ndi kuchitira umboni za Iye amene anampulumutsa, ndipo zitatha izi moyo wake wonse unakhala wodzipereka, kutumikira Khristu wosatopa.



Taonani chitsanzo china ndi kuganizira za otembenuka mtima a Khristu oyambilira ku Atesalonika.



Chimodzi mwa zinthu zitatu zikuluzikulu chimene amadziwika nacho ndicho “chikondi chochitachita” pa Ambuye ndi kumtumikira Mulungu wamoyo komanso weniweni amene anatembenukirako kuchoka ku mafano awo (1 Ates. 1:3,9).

Zoonadi ndime zimenezi za Malemba zikutionetsa ife kuti ntchito ya Ambuye ndi chimodzi mwa chisonyezo cha zinthu zimene zimatsatana ndi chipulumutso.



Mau a Ambuye akutionetsa ife kuti zimenezi ndi zomwe Iye amayembekezera kwa onse amene ali ake ndipo anavomereza chipulumutso chake, ndiponso taona kuti zimenezi ndi zomwe Paulo ndi Atesalonika anachita pamene anapulumutsidwa.Tsopano funso ndi lakuti: kodi ife tikuchita chiyani?



Kodi ife tikumtumikira Ambuye, tikumgwilira Iye ntchito, tikukhala mwa chifuniro chake?



Kapena ife tikuzitumikira tokha ndi dziko lapansi ili loipa?



Kutumikira Ambuye komanso kukhala chifukwa cha Iye ikhale ntchito yathu yoyamba komanso maitanidwe tsopano.



Ambuye sanangotipulumutsa ife chabe kuti tikhale pabwino ndi otetezeka kumwamba.



Zikanakhala kuti ndi choncho, Iye akanatitenga kale ku ulemelero pa nthawi imene tinangopulumutsidwa kumene.



Iye anatisiya ife kuti tigwire ntchito komanso kuzitanganidwitsa tokha chifukwa cha Iye ndi kukhala mboni zake, kuwala ndi kumuimira padziko lapansili limene Iye anakanidwa ndi kukhomedwa pamtanda.



Iye anatipanga ife kuti tikhale manja ake, mapazi ake, mtima komanso milomo yake padziko lapansi.



Iye akufunitsitsa kuti ife tinyamule uthenga wake ndi kumgwilira ntchito, kupita kukachita zabwino monga Iye ankachitira adakali padziko lapansi.



Iye chikondi chake chasefukira kwa anthu osauka, ovutika kudzera m’mitima yathu, ndipo Iye akanalankhula kwa abambo ndi amai ndi ana pogwiritsa milomo yathu.



Mwayi wathu waukulu umenewu!



Angelo sanapatsidwe utumiki umene anatikhulupilira nawo ife.



Kodi ife timawerengera kukonderedwa kwakukulu kumeneku?



Kufuna kuchita kanthu kena kake pa Ambuye chikhale chikhumbokhumbo cha aliyense amene analawa chikondi chachikulu ndi chisomo cha Khristu.



Ife tikazindikira pang’ono za gehena woopsa amene Iye anatipulumutsako komanso gawo lodabwitsa limene Iye watibweretsako, komanso mazunzo amene anawapeza kuti atipezere chipulumutsocho, ife tidzakopeka ndi chikondi chake ndi kuyetsetsa kumuchitira Iye kenakake, kuonetsera kuyamika ndi kuthokoza kwathu.



Posachedwapa tinakumana ndi munthu wina amene anachiritsidwa modabwitsa ku matenda ake ndi mphamvu ya Ambuye.



Tinalankhula naye, “Ambuye wachita zambiri pa iwe pokuchiritsanso; uli nazo zambiri zoti umuthokozere Iye.”



Iye anayankha, “Inde ndikudziwa za ichi, ndipo ndili wothokoza pa zimene wandichitira, komanso ndikufuna kuonetsera chimenechi.”



Iye anafunitsitsa kupereka chisonyezo chooneka ndi maso cha kuthokoza kwake Ambuye, ndipo mkazi wake anatiuza za moyo wake wosinthika komanso za ntchito imene amagwilira Ambuye tsopano.Chomwechonso zikhale ndi ife tonse.



Tionetsere kuthokoza kwathu pa zimene Ambuye watichitira pa kukhala kwathu ndi kumgwilira Iye ntchito.



Pamene tikuyenera kumtumikira ndi kumgwilira ntchito Ambuye, Iye amatilonjeza kutipatsa mphoto pa zonse zimene tikumchitira Iye.



Iye amatipulumutsa popanda mtengo wina ulionse wolipira, kenako amatilipiranso pa zonse zimene ife timamuchitira!



Chisomo chodabwitsadi!



Iye akulonjeza mphoto ngakhale kwa iye wakupereka chikho cha madzi m’dzina lake (Marko 9:41).



Makolona osiyanasiyana adzaperekedwa kwa iwo otumikira Ambuye.



Zimenezi zimasungidwira kwa ife ngati chilimbikitso mu zokhoma ndi zokhumudwitsa zopezeka pamene tikutumikira Iye pansi pano.

Tiyeni tifunitsitse kuchitira kenakake Ambuye ndi kukhala otanganidwa pa Iye.



Zimatithandiza kupewa mayesero ndi kuchita zinthu komanso kupita kumalo amene ali osasangalatsa Mbuye wathu.



Tikakhala kuti tikugwilira Iye ntchito, sitimatanganidwanso ndi zinthu zina.



Kenakonso, chimwemwe cha kutumikira Ambuye chimalimbikitsa miyoyo yathu ndi kutikweza ife pamwamba pa zokopa za dziko lapansi komanso zilakolako za thupi, pakuti ife tapeza chinthu china chabwino koposa zonse.

Kodi unakumanako nazo zoterezi, wokondedwa mzanga?



Ngati ayi, kodi sungayeseko?

Komatu wina akhoza kulankhula, “Kodi ndingachite chiyani kwa Ambuye? Ndilibe kuthekera kochuluka, nthawi kapena ndalama.”Pamene amalembera kalata kwa iwo amene anali atumiki, mwinanso akapolo, mtumwi akulankhula, “chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye ………mutumikira Ambuye Khristu mwa ukapolo” (Akol. 3:23,24).



Inutu mungathe kugwira ntchito yanu ya tsiku ndi tsiku kwa Ambuye ndi kumtumikira Iye mu ntchitomo.



Kuonjezera apo, Ambuye analankhula za Mariya, “Iye wachita chimene wakhoza” (Marko 14:8), ndipo zimenezi ndi zomwe Iye akuyembekezera kwa wina aliyense wa ife.

Pamene Mose ananyinyirika kusachita zimene Ambuye anamuuza kuti achite, Mulungu anati kwa iye, “Icho nchiyani m’dzanja lako?” (Eks. 4:2).



Iye anagwiritsa ntchito ndodo imene Mose anali nayo m’manja mwake chomwechonso Ambuye adzagwiritsa ntchito chimene ife tili nacho, ngakhale chitachepa bwanji; koma tikuyenera kupereka chinthucho kwa Iye, ndipo Iye adzadalitsa chithuncho ndi kutipatsa zina zochuluka pamene tigwiritsa ntchito kwa Iye.

Pita kwa Ambuye, m’bale wokondeka, ndipo umfunse zimene Iye akufuna kuti umchitire.



Khalani m’chiyanjano ndi Iye, ndipo adzakuonetsani ntchito yanu, ndipo adzakulimbikitsani pa ntchitoyo.

Pomaliza, ganizirani mau awa a m’Malemba: “Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe ya moyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera” (Aroma 12:1).



Mulungu athandize aliyense wa ife tichite chomwechi.



11. KUFUNITSITSA AMBUYE

Kupulumutsidwa ndi kupeza chipulumutso mwa Khristu sinkhani ya mfundo yozizira.



Zikhumbokhumbo za mtima zimatengapo gawo chimodzimodzi malingaliro.



Chipulumutso chimaimikika pa munthu wamoyo, wa umulungu, komatu ndi munthu wa kuthupi, amene chikondi chake chakufa cha m’mbuyomu, komanso chikondi chake cha moyo tsopano, zakopa mtima kwa Iye ndi kutenga chikondi chake kwa Mpulumutsi wodalitsika ameneyu.



Pali kuvomereza kwa chikondi cha Khristu, komanso chikondi chake, chotsanulidwa m’mitima mwathu ndi Mzimu woyera(Aro. 5:5), chikondi chopezedwa ndi lingaliro pa Iye.



Zimenezi ndi zomwe zimachitika pamene munthu wabadwadi kwatsopano.



Chikhumbokhumbo cha Mkwati pa Mkwatibwi

Ubale wa Khristu ndi iwo amene anavomereza chipulumutso chake ukuonetsedwa m’Malemba pansi pa chithunzithunzi cha Mkwati ndi mkwatibwi wake.



Ubale waukulu wa dziko lapansi umenewu ukugwiritsidwa ntchito kuonetsa kulumikizana kwa chikondi chimene chilipo pakati pa mtima wa Khristu ndi Mkhristu.



Zimenezi zikuonetsedwa bwino mwa mtundu ku Nyimbo ya Solomo.



Malemba otsatirawa akutionetsera ife ubale umenewu.



Ku Mateyu 25:1-13 Ambuye akudzionetsera yekha ngati Mkwati amene wabwerera Mkwatibwi wake.



Ku Aefeso 5:23-32, Mpingo, umene ukupangidwa ndi onse opulumutsidwa, ukuoneka monga mkwatibwi wa Khristu.



Ubale umenewu ukusungidwabe ndi mtumwi Paulo pamene amalembera okhulupilira a ku Akorinto, kuti iye anawakwatitsa, kapena anawapalitsa ubwenzi ndi mwamuna m’modzi, kuti iye akalangize iwo ngati namwali kwa Khristu (2 Akor. 11:2).



Kenako ku Chivumbulutso 18:7-9 timamva za ukwati wa Mwanawankhosa kumwamba, ndipo pa mutu 21 tili ndi mafotokozedwe a mkwatibwi ngati mkazi wa Mwanawankhosa, kutsika kuchokera kumwamba.



Munthu aliyense wopulumutsidwa, ali ngati munthu wopalidwa ubwenzi kwa Khristu ndi chikhumbokhumbo cha mkwatibwi komanso kumfunitsitsa Iye, monga umo mtima wa namwali umakhala ndi chikhumbokhumbo pa wokondedwa wake.



Mtima wake sumakhutitsidwa ndi kulumikizana kumene kumakhalapo komanso mphatso zochokera kwa wokondedwa wake, kapenanso kuyenderana kumene kumakhalapo, koma iye amayembekezera tsiku la ukwati wake limene adzakhala pamodzi ndi iye.

Ngati zimenezi ndi zoona molingana ndi chikondi cha dziko lapansi, kodi zikhoza kukhala zoona bwanji ndi ife amene tavomereza chikondi cha umulungu kuchokera kwa wokondeka wamkulu mwa onse, Ambuye Yesu Khristu!



Chilengedwe chatsopano mkati mwathu chimafunitsitsa zoposera pa chisangalalo cha chikondi cha Khristu ndiponso chiyanjano ndi Iye mwa chikhulupiliro.



Chilengedwechi chimakhumba Iye, ndi kuyang’anira za lonjezano la kubweranso kwake kudzatilandira ife kwa Iye yekha cholinga kuti tikakhale naye kwamuyaya mu ulemelero (Yoh. 14:3).



Mwadongosolo, kunalembedwa, “Ndipo Mzimu ndi Mkwatibwi anena Idzani ……… Idzani Ambuye Yesu” (Chiv. 22:17,20).



Kumeneku ndiko kulira kwa mtima wokonzedwanso.



Chikhumbokhumbo cha kufuna Ambuye ndi kubweranso kwake ndi chimodzi mwa zinthu zimene zimatsatana ndi chipulumutso.



Zimenezi zinadzalidwa mwa umulungu m’moyo mwa wobadwanso kwatsopano, ndipo zikuyenera kupezeka mwa onse amene amanena kuti ali ndi chipulumutso chachikulu chimenechi mwa Khristu ndi kumkonda Mpulumutsi wodabwitsayu.



Zimenezinso ndi zomwe Mkwati wathu wokondedwa amakondwera kuona mwa ife, pakuti Iyenso, akudikilira nyengo imene mkwatibwi wake akonzeke, ndipo kuti akamulandire kwa Iye yekha ndi kukhala naye kwamuyaya kumbali yake mu ulemelero.



Atate, amene mwandipatsa Ine ndifuna kuti kumene kuli Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang’anire ulemelero wanga” (Yoh. 17:24).



Limeneli ndilo khumbo lake komanso pemphero lake.



Kutumikira Pamene Tikudikira

Phunziro lapitali taona nkhani ya kutumikira Ambuye ngati chimodzi mwa zinthu zotsatana ndi chipulumutso.



M’Mau a Mulungu, timapeza nthawi zonse kulumikizana ndi chikhalidwe chimenechi cha kuyang’ana ndi kufunitsitsa kwa Ambuye kubweranso kwa ife.



Otembenuka mtima kumene a ku Atesalonika sanangotumikira Mulungu wamoyo ndi woona, koma anadikilira Mwana wake kuchokera kumwamba (1 Ates. 1:10).



Iwo sanangokhala ndi chikhulupiliro komanso chikondi chokha chimene anachivutikira, komatu chiyembekezo, chimene chimayang’anira za kuthekera kwa kubweranso kwake.



Iwo anafunitsitsa Iye ndi malingaliro enieni a ukwati.





Mau a Ambuye kwa ophunzira ake akuvomerezana ndi izi.



Iye anawauza kuti agwire ntchito, apemphere ndi kuyang’anira za kubweranso kwake (Marko 13:33-37).



Ndipo Luka akulemba kuti Iye anati, “Khalani odzimangira m’chuuno (pa utumiki), ndipo nyali zanu zikhale zoyaka (pa umboni); ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera Mbuye wao.”

Ndipo Iye akuonjezera, “Odala akapolowo amene Mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira” (Luka 12:35-37).



Zimenezi zidzapangitsa mtima wake kusangalala kupeza wokondedwa wake akudikira Iye.

Ndiponso pamene ife tikudikira ndi kuyang’anira kubwera kwake, tikuyenera kumgwilira Iye ntchito; zinthu ziwirizi zimayendera limodzi.



Pamene Mpulumutsi wathu wokondedwa adzabwerera ife, tidzamuona Iye monga ali (1 Yoh. 3:2).



Kenako chikhulupiliro chidzasintha kukhala zooneka ndi maso komanso chiyembekezo kukhala chipatso cha chisangalalo ndi chizindikiritso.



Ife tidzaona nkhope yake ya mdalitso ndi kusangalala nacho kwathunthu chikondi chonse ndi ulemelero wake wokongola ndi ungwiro wa Mkwati-Mpulumutsi wathu, ndi kukhala kwamuyaya ndi Iye.

Amenewa ndi mapeto odalitsika ndi kutsiriza kwa kuthekera kwathu konse, ntchito yathu ndi kuyendayenda pansi pano.

Chomwecho chikhumbokhumbo chilichonse cha malingaliro a mitima yathu chidzakwanitsidwa; chimenechi ndicho chiyembekezo ndi chokhumba chathu – kuona ndiponso kukhala ndi Iye kwamuyaya.



Pakuti chimenechi ife tikuyenera kukhumba kwamuyaya, ndi kukhutitsidwa nacho.



Mlembi wa nyimbo waonetsera izi pakunena:





Pa nkhope yanu tikhumba kuonapo:

Pa mau anu tifuna kumva:

Pakuti ndi Inu tifuna kukhala

Pakuti ndiko kufanana kumene tikhale nako.

Bwerani mudzatenge Mkwatibwi wanu wakumwamba:

Mwa Inu, Ambuye Yesu,

Ife tidzakhala okhutitsidwa kwamuyaya.”



Pamenepo ife tilole Mzimu wa Mulungu akonze mwa ife zikhumbokhumbo zozikika ndi kufunitsitsa Mkwati wathu komanso kuyang’anira ndi kudikira mwachidwi za kubweranso kwake.



KUTSIRIZA

Mitu yosiyanasiyana yaikidwa monga “zinthu zimene zimatsatira chipulumutso” mwa Khristu.



Ife taona kuti ngati munthu wapulumutsidwadi, iye:

  1. ali ndi mtendere ndi Mulungu;

  2. ali ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera;

  3. ali ndi mayamiko komanso matamando mu mtima mwake

  4. ndi wolengedwa watsopano mwa Khristu – munthu watsopano;

  5. mkati mwake Mzimu Woyera wakhazikika, ndipo chipatso cha Mzimu chikuonekera m’moyo mwake;

  6. amapemphera ndi kuyanjana ndi Mulungu

  7. amadya pa Mau a Mulungu monga chakudya chokhacho cha moyo wake;

  8. pagulu amavomereza kuti ndi otsatira Khristu pakubatizidwa m’dzina lake;

  9. amaphunzira kudzipereka ndi kumvera Khristu monga Ambuye ndi Mpulumutsi;

  10. amatumikira Ambuye ndi kukhala chifukwa cha Iye; ndiponso

  11. amafunitsitsa Ambuye kuti abwere adzamulandire mwa Iye yekha kwamuyaya.



Mosakaika konse, zinthu zina zingathe kutchulidwa ngati zinthu zotsatira chipulumutso, koma zimene talembazi ndizo zikuluzikulu zimene Mau a Mulungu akunena kuti zikupezeka mwa iwo opulumutsidwa.



Kulingalira kwathu pa zimenezi kutakase ndi kukhudza mitima yathu.



Tionetsetse kuti pamene tikunena kuti tinapulumutsidwa, pali zinthu zambiri zimene zikuyenera kuoneka m’miyoyo yathu ngati zotsatira za chipulumutso chimene ife tikunena kuti tili nacho, ndipo kupezeka kwake ndi kusoweka kwake m’miyoyo yathu zikhale umboni wa choonadi kapena bodza la kuvomereza kwathu.



Zingathe kukhala mwa chifooko pamene zikuonekera, ndipo osati mopitilira, komabe pakuyenera kukhala umboni wa chisonyezo cha kupezeka kwake m’miyoyo yathu.



Ndipo pamenepo tifunefune thandizo kuchokera kwa Mulungu kutipatsa chisonyezo chachikulu ndi chokhazikika m’miyoyo yathu za “zinthu zimene zimatsatana ndi chipulumutso.”