MAKHALIDWE AWIRI A OKHULUPIRIRA
Mwana aliyense wa Mulungu, mwachibadwidwe anapangidwa kukhala wotenga nawo gawo mu chikhalidwe cha umulungu.
Chikhalidwe chatsopano cha umulungu chimenechi chodzalidwa mwa wokhulupirira ndiwo machitachita amphamvu a Mulungu mwa Mzimu wake kudzera m’Mau.
Chotero wokhulupirira ali nacho chikhalidwe mwa iye monga chili mwa Mulungu.
Monga umo anatengera nawo gawo mwa chikhalidwe chakugwa molingana ndi chibadwidwe, momwemonso monga mwa kubadwa kwatsopano akutenganso nawo gawo mu chikhalidwe chake cha Mulungu.
Pano pali zimene Baibulo likunena zokhudza momwe wokhulupirira amapezera chikhalidwe chatsopano chakumwambachi:
“Chobadwa mthupi chikhala thupi (chikhalidwe chimene timakhala nacho monga mwa chibadwidwe); ndipo chobadwa mwa Mzimu, chikhala mzimu (chikhalidwe chimene chimakhala mwa ife tikabadwanso mwatsopano). Usadabwe chifukwa ndinati kwa iwe, uyenera kubadwa mwatsopano” (Yohane 3:6-7).
“Mwa chifuniro chake mwini anatibala ife ndi mau a choonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoundukula za zolengedwa zake” (Yakobo 1:18).
“Inu amene munabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa” (1 Petro 1:23).
“Mwa izi anatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi akulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nawo umulungu wake, mutapulumuka ku chivundi chili padziko lapansi m’chilakolako” (2 Petro 1:4).
Chikhalidwe chatsopano cha umulungu chimenechi choikidwa mwa wokhulupirira chinamangika mosalekanitsidwa ndi Umunthu wa Khristu amene ali chiyambi chake.
Chotero timawerenga kuti “Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umenewu uli mwa Mwana wake. Iye wakukhala ndi mwana ali nawo moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo” (1 Yohane 5:11-12).
Ndiponso “Moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu ……. Khristu ndiye moyo wathu” (Akolose 3:3-4).
Chikhalidwe cha moyo watsopano umenewu chikuchokera mwa Khristu.
Ameneyo ndiye kasupe wake ndipo chikhalidwechi chili ndi maonekedwe komanso makhalidwe ofanana ndi omwe ali mwa Khristu – zokhumba ndi zolakalaka zake ndi zofanana.
Chotero chikhalidwe chimenechi chimakhala ndi ufulu pokhapokha ngati chichita mwa wokhulupirirayo monga umo chinachitira mwa Khristu pamene Iye anali padziko lapansi.
Ena angathe kunena kuti lero lino tikukhala moyo wozunguliridwa ndi zinthu zosiyana ndi zimene zinali mu nthawi ya Khristu.
Tikatengera ku tekinoloje ndi zinthu zina zosokoneza za makono, zimenezi ndi zoona ndithu.
Komatu chilengedwe cha munthu ndi ma ubale a umunthu sizinasinthe konse ayi, ndipo ndi kudzera mu zimenezi pamene chikhalidwe cha umulungu chinaonekera pamene Iye amalumikizana ndi anthu ena.
Kudzera mu ma ubale amenewa ndi momwe chikhalidwe cha umulungu chimaonekera mwa ana a Mulungu pamene agwira ntchito yotumikira Mulungu ndi anthu.
Popanda kubadwa mwatsopano – popanda kukhala ndi chikhalidwe cha umulungu chimenechi – palibe kuthekera kulikonse kuti munthu angathe kukhala moyo wa chisangalalo chamuyaya.
Mphutsi za kutsutsika zimadya mizu ya zinthu za ulemelero wosakhalitsa wa munthu wosatembenuka mtima, ndipo ulemerero wao wonse ukunga udzu ungofota ndi duwa lake lingogwa (1 Petro 1:24).
“Pakuti kuseka kwa chitsiru kunga minga ili kuthetheka pansi pa mphika; ichinso ndi chabe” (Mlaliki 7:6).
Ngakhale minga ikuthetheka ikunyekanso, ndipo kuthethekako sikudzamvekanso.
Komatu iye wakubadwa mwa Mulungu alowetsedwa mchiyanjano chamuyaya ndi Mulungu.
Iye amapangidwa kukhala wotenga nawo gawo mu chikhalidwe cha umulungu ndi moyo wake wosatha (Aefeso 2:5).
Tsopano moyo wa umulungu umenewu wokhala mwa wokhulupirira ukuyenera kuchitachita monga mwa chikhalidwe chake, monga mwa zilakolako zake ndi zokhumba zake kuti ukasangalale.
Moyo wa umulungu umadziwika ndi chiyero komanso chikondi.
Moyowu umapeza zosowa zake ndi zokhumba zake zazikulu pa kukwaniritsa kutumikira Mulungu komanso anthu mwa phindu.
Wokhulupirira amakhala wosangalala pokhapokha ngati akhala moyo woterewu, pakuti ndi kudzera m’moyo umenewu wokha pamene chikhalidwe cha umulungu mwa wokhulupirira chimakhala nawo machitachita mogwirizana ndi makomedwe ake komanso cholinga chake.
Kodi ndi chifukwa chiyani Mulungu anatiombola pa mtengo woterewu, wa nsembe ya Mwana wake?
Kodi ndi chifukwa chiyani Khristu anali wofunitsitsa kulipira mtengo wa chiombolo chathu kudzera m’mwazi wake?
Sichinalitu chifukwa cha kukakamizidwa ndi mphamvu yochokera kunja, pakuti palibe mphamvu iliyonse yochokera kunja yoposa Mulungu imene ikanabwera kudzamnyamuliza Iye.
Komatu chinali chifukwa cha kukakamizika kwa chilengedwe chake chimene chimapeza chisangalalo mu chikondi chosadzikudza ndi kutumikira wena.
Ana a Mulungu anapezako chikhalidwe cha umulungu chimenechi kotero kuti moyo wachikondi komanso kutumikira mosadzikonda kumawapangitsa kukhala osangalala.
Koma moyo wodzikonda umapsinjiriza chikhalidwe cha umulungu mwa wokhulupirira ndipo zimamupangitsa kukhala wodzimvera yekha chifundo.
Mfundo ina yofunika kuidziwa ndi yakuti wokhulupirira alinso ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa iye kulimbikitsa ndi kukonza chikhalidwe chatsopano chimenechi.
Pamene tikudya mau a Mulungu ndi mtima womvera komanso ndi mzimu wapemphero, Mzimu Woyera amationetsera ife zinthu za Khristu (Yohane 16:14).
Chilengedwe chatsopano, chimene wokhulupirira wakonzedwera kuti akhale wotengako gawo mwa kubadwa mwatsopano, ndiko kukhala mwa umulungu, kusangalala mwa Mulungu ndi m’chifuniro chake mwa munthu komanso m’chikondi chake pa munthu.
Kotero palibe chikhumbokhumbo cha kudzikonda pakutumikira munthu, komanso nthawi yomweyo chikhumbokhumbo cha kusangalatsa Mulungu pa zonse zimene chikhalidwechi chimachita.
Wokhulupirira amapeza ufulu wonse m’chilengedwe chake chatsopano, pamene zonse zimene akuchita zikugwirizana ndi m’kuwala kwa chifuniro cha Mulungu;
pakuti chikhumbokhumbo cha chikhalidwe cha umulungu chopezeka m’chifuniro cha wokhulupirira zimalumikizana ndi cha Mulungu pakuti zonse zikuchokera malo amodzi.
Chikhalidwe cha umulungu chopezeka mwa Mulungu ndicho chiyambi cha chifuniro chake;
ndipo chifukwa chakuti mwa wokhulupirira muli Mzimu wa Mulungu amene amamupatsa mphamvu, chikhalidwe chake cha umulungu chimatulutsa chikhumbokhumbo mwa iye chogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.
Pakuomba mkota, tingathe kunena kuti Mulungu amakhumba zimene Iye afuna chifukwa chimenechi chimakondweretsa chikhalidwe chake;
ndipo pakuti wokhulupirira anapangidwa kukhala wotenga nawo gawo pa chikhalidwe chomwechi cha umulungu iyenso amapeza chisangalalo m’chifuniro cha Mulungu.
Kusangalala m’chifuniro cha Mulungu kumeneku ndi kwa mphamvu komanso kochitachita monganso mlingo omwewo chikhalidwe cha umulungu mwa wokhulupirira chili cha mphamvu ndi chochitachita.
Chisangalalo chake ndi chogwirizana ndi momwe iye amalolera kuti chikhalidwe chake cha umulungu chikule ndi kukhala chochitachita.
Pamene iye aperekabe mpata ku zikhumbokhumbo za chikhalidwe chake chakugwa, iye amakhalabe munthu womvetsa chisoni ndi wosasangalala chifukwa cha zotsatira zokhumudwitsa zimene zimakhala pa chilengedwe chake cha umulungu.
KODI NDI CHIFUKWA CHIYANI KAWIRIKAWIRI TIMAKHALA OSAKONDWA?
Munthu wosasinthika alibe chikhalidwe cha umulungu;
okhawo amene anabadwa mwa Mulungu chikhalidwe chimenechi ali nacho.
Koma munthu wosakonzedwa ali nacho chikumbumtima.
Iye amadziwa kudzera m’chikumbumtima chakecho kuti akuyenera kukonda, kulemekeza ndi kumvera Namalenga.
Koma malingaliro amenewa ndi opanda phindu kwa iye chifukwa akufuna kuyenda mnjira yakeyake komanso kukhala mbuye wa tsogolo lake lomwe.
Iye amakana kuganiza zokhudza Mulungu.
“Koma oipa ali ofanana ndi nyanja yowinduka; pakuti siingapume, ………… ‘palibe mtendere,’ ati Mulungu wanga, ‘kwa oipa’” (Yesaya 57:20-21).
Tchimo limaononga mtendere wa munthu amene anabadwa mwatsopano.
Tchimo limaponya moyo wake mkulimbana.
Chikumbumtima chake chimamutsutsa, ndipo chikhalidwe cha umulungu chimadana ndi tchimolo ndiponso chimakhumudwa nalo tchimolo.
Tchimo limabweretsa kugonjetsedwa pa moyo wathu.
Ukamachita chinthu chimene mtima wako sukuvomereza ndipo chikumbumtima chako chikukudzudzula, ndiwe munthu womvetsa chifundo.
Ukhoza kuyesetsa kuiwala kapena kukana kulingalira za chinthucho chifukwa kuti chinthucho ndi chosasangalatsa, komatu imeneyi sinjira yabwino yothetsera vuto lanu.
Kenako malingaliro okhumudwitsa okhudza chipulumutso amayamba kubwera pamene munthu wayambapo kuganiza bwino, “ngati ndine wopulumutsidwa, ndi chifukwa chiyani ndili chonchi?” Kodi yankho la mnyengo yosautsayi ndi lotani?
Pali zinthu ziwiri zimene mukuyenera kudziwa musanamasulidwe:
choyamba, momwe mungatsimikizire za chipulumutso chanu; chachiwiri, m’mene mungakhalire ndi mphamvu ya chigonjetso pa tchimo la m’moyo mwanu.
Tiyeni tione mfundo ziwiri zimenezi mwa tsatanetsatane.
KODI TINGATSIMIKIZIKE BWANJI ZA CHIPULUMUTSO CHATHU?
Kuti tiyankhe bwino funso lokhudza chitsimikizo cha chipulumutso, tiyeni tione nyengo ziwiri za anthu osiyana amene ali ndi chikaiko komanso mayankho a mafunso awowa.
Phunziro la munthu woyamba: Kuchotsa chikaiko
“Ine ndinalandira Ambuye monga mpulumutsi wanga pamene ndinali ndi zaka 13.
Ndinakwatiwa ndili ndi zaka 18.
Mwamuna wanga si Mkhristu chimodzimodzinso makolo anga.
Ndinatalikirana kwambiri ndi komwe kuli akhristu amzanga chomwecho moyo wanga wauzimu unazizira ndipo ndinabwerera m’mbuyo.
Satana amayesetsa kundiuza kuti ine sindinapulumutsidweko chiyambire.
Funso langa ndi ili: Kodi ndingadziwe bwanji mosakaika konse kuti ndine wopulumutsidwa?
Ndipo ngati ndine wopulumutsidwa kodi ndingabwererenso kwa Mulungu?
Ndayetsetsa kupemphera koma ndimaona ngati mapemphero anga sadutsa ngakhale denga la nyumba yanga.
Ine ndikufuna kukhala Mkhristu ndi kukhala chifukwa cha Mulungu, koma moyo wanga waonongeka!
Ndili wokonzeka kupereka china chilichonse kuti ndidziwe ngati ndine wopulumutsidwa kwamuyaya ndi kuti kumwamba ndiko kwathu.
Kodi mungandithandizeko?”
Inetu ndikumvetsetsa kukhumudwa kwanu ndipo ndine wokondwa kuti Ambuye wakutsitsimutsani kuti muzindikire chosoweka chanu.
Ine ndikukutsimikizirani kuti Ambuye akufunitsitsa kukumana ndi chosoweka chanu ndi kukupatsani, kudzera m’chikhulupiriro mwa Iye, chitsimikizo cha chipulumutso cha muyaya komanso mtendere umene umaposa chidziwitso chonse.
Inu mwanena kuti, “Ndayetsetsa kupemphera koma ndimaona ngati mapemphero anga samadutsa ngakhale denga la nyumba yanga.”
Kuchokera mu mfundo imeneyi, kwa ine zikuonetsa kuti pali zinthu ziwiri zimene zikuyambitsa vuto lanu:
inu mukuyang’ana kwambiri chizindikiro osati kukhulupirira Mulungu;
kapena mwina inuyo moona mtima simunavomereze tchimo lanu ndi kugwa kwanu pamaso pake.
“Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse” (1 Yohane 1:9).
Limeneli ndi lonjezano lotsimikiza la Mulungu.
Kodi mwavomereza kwa Iye machimo anu komanso kugwa kwanu?
Ngati ndi choncho khulupirirani kuti Iye wakukhululukirani molingana ndi Mau ake.
Inu mukuyang’ana zimene mungamve mkati mwanu pokhudza chikhululukiro;
kodi zakumva mkati mwanu zikukhudzana bwanji ndi chikhululukiro?
Chikhululukiro cha Mulungu ndi zomwe Iye mwini Mulungu amamva mkati mwake zokhudza inuyo, osati zimene inuyo mukumva mkati mwanu.
Iye ngati wakhululuka amamva mkati mwake kuti zili bwino, kapenanso sakanakhululukira.
Musamadziyang’anire pa inu nokha;
yang’anirani pa zimene Mulungu akulankhula:
“Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire.”
Mutatha kuvomereza machimo anu kwa Iye, khulupirirani kuti Iye wakhululukira machimo anu monga Iye ananenera kutero.
Mkhulupirireni Iye kuti ndi woona ku malonjezano ake.
Musamupangitse Iye kukhala wabodza pakukayikira zimene Iye akunena.
Taonani ndimeyi ikunena kuti Mulungu “wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire.”
Wokhulupirika komanso wolungama kwa ndani?
kwa Khristu! Khristu anasenza machimo athu mthupi mwake pa mtanda (1 Petro 2:24).
Pamene mwavomereza machimo anu kwa Mulungu, kukhulupirira kuti Iye anasenza machimowo pa mtanda, Mulungu sakanakhala wokhulupirika ndi wolungama pa Khristu akanapanda kukukhululukirani.
Zikanakhala ngati Mulungu walankhula kuti,
“Ine sindinakhutitsidwe ndi zomwe Khristu anachita pamene anafera machimo anu ndipo ndi kuyenera kuwasungabe machimowo motsutsana nanu.”
Tangoganizirani Mulungu kukhala wosalungama pa Khristu, Khristu atamaliza kulipira dipo, koma Iye kukutenganibe kukhala wochimwa?
Onongani malingaliro amenewo! ntchito ya Khristu ndi yokwanira ndipo Mau a Mulungu akutsimikiza.
Mwanena kuti munapulumutsidwa muli ndi zaka 13.
Kodi ndi mtundu wanji wa chipulumutso umene Khristu anatigulira ndi mwazi wake?
Chinthu chosakhalitsa chimene chikuyenera kuchotsedwa pamene talakwitsa?
Kapena mwazi wake unali wa mtengo wapatali pamaso pa Mulungu kukatigulira chipulumutso chamuyaya?
Indedi unali wotero!
Mwana wamkulu wa Mulungu anakhala Munthu, kupatula kuti sanachimwa, ndipo anakhetsa mwazi wake chifukwa cha ife pa mtanda paja.
Kodi m’mwazi umenewu mtengo wake unali wotani?
Monga kupambana kumene anali nako Iye amene anakhetsa mwaziwo, Mulungu wamkulu ndi wamuyaya, Mwana amene anadzionetsera yekha mthupi.
Chomwecho kupambana kwa mwazi wake ndi kwakukulu komanso kwa muyaya.
Ndipo zimenezi ndi zomwe Mau a Mulungu amatiuza:
“koma mwa mwazi wa Iye yekha, analowa kamodzi kumalo opatulika, atalandirapo chiombolo chosatha” (Ahebri 9:12).
Chiombolo chokhacho chimene Khristu anatigulira ndi cha muyaya.
Ngati mutakhala ndi chinthu lero chimene mawa mukhoza kuchitaya, chimenecho si chiombolo mwa Khristu Yesu, pakuti chiombolo chake ndi cha muyaya.
“Mwachifuniro chimenechi (chifuniro cha Mulungu) tinapatulidwa (kuikidwa pambali mwa Mulungu) kudzera mu chopereka cha thupi la Khristu Yesu kamodzi kokha.”
Sichingabwerezedwenso.
“Pakuti ndi chipereko chimodzi anawayesera angwiro chikhalire iwo oyeretsedwa” (Ahebri 10:10, 14).
Chimenechi ndicho chiphunzitso cha Mau a Mulungu chophweka ndi chomveka bwino.
Anali Mulungu mwini amene anatipatula ife kwa Iye yekha kudzera mu nsembe ya Khristu.
Khristu anafa kamodzi kokha pa machimo onse kwa muyaya;
chomwecho wokhulupirira aliyense amaima pamaso pa Mulungu wolungamitsidwa kwa muyaya kudzera m’machitachita a muyaya a nsembe imodzi yokhayo.
Palibe tchimo limene lidzabwera pamoyo wa wokhulupirira limene silinaomboledwe kale mwa nsembe imodzi yokhayo imene inaombolanso machimo onse a iwo akukhulupirira.
Kuima kwao kumakhala kwa ngwiro kwa muyaya pamaso pa Mulungu chifukwa Mulunguyo anawaika iwo pamalo a chiombolo chamuyaya chimene Khristu anawagulira.
Mulungu samalandira munthu aliyense pokhapokha kudzera mu nsembe ya Khristu.
Pakuti nsembe imodzi yokhayo inaperekedwa kamodzi kokha, okhulupirira onse amaima a ngwiro kwa muyaya kudzera mu nsembe ya ngwiro ya Khristu, amene anachotsa machimo awo onse – akale, atsopano ndi amtsogolo omwe – kamodzi kokha komanso kwa muyaya pamene Iye anadzipereka yekha wopanda banga kwa Mulungu.
Ena amanena kuti,
“ngati zimenezi ndi zoona, ndiye kuti palibe kusiyana kulikonse pa zimene wokhulupirira amachita.”
Zimenezi ndi zoona ndithu, makamaka tikatengera momwe iye akuimira pamaso pa Mulungu.
Palibe tchimo lidzabwera pa moyo wa wokhulupirira limene silinawerengedwe ndi nsembe yangwiro ya Khristu.
Koma tchimo limabweretsa kusiyana kwakukulu pokhudzana chisangalalo cha wokhulupirirayo ndi chiyanjano chake ndi Mulungu.
Kodi iye angathe kukhala bwanji wosangalala pamene akudziwa kuti akuchimwira Mulungu amene amamukonda kwambiri?
Mulungu amadana ndi tchimo;
Iye sangakhale m’chiyanjano ndi tchimolo, kapenanso kupangitsa wokhulupirira kusangalala pamene akukhalabe mu uchimo.
Kodi Mulungu angathe kuyenda naye bwanji mnjira yotereyi?
Kuonjezera apa, monga Atate amene amakonda mwana wake, Mulungu ali wokonzeka kupereka chilango ndi kumukonza pa ubwino wake womwe pamene iye sakumvera;
ndipo kulanga kumeneku sikosangalatsa ayi, koma kopweteka.
Komabe mapeto ake zimabereka chipatso cha mtendere kwa iwo amene amaphunzira kuchokera m’menemo pakudana komanso kusiya tchimo. (onani Ahebri 12:4-11).
Pamene wokhulupirira achimwa ndipo walephera kulapa ndipo wadziweruza yekha pamaso pa Mulungu, amataya chisangalalo cha chiyanjano chake ndi Atate, ndipo amadzipereka yekha ku kulanga kwake.
Iye amakhalabe mwana wa Mulungu.
Iye sanataye chipulumutso chake, chimene ndi chamuyaya, koma wataya chisangalalo cha chiyanjano chake ndi Atate wake.
Iye sangachibwenzeretse chisangalalochi kufikira atalapa machimo ake kwa Atate wake ndi mtima wokhazikika ndi cholinga cha kuwasiya machimowo.
Werengani Masalmo 32 ndipo muone nyengo yoipa imene Davide anali nayo pamene anakana kulapa tchimo lake.
Kenako werenganinso nyimbo ya chiombolo komanso chikhulupiriro mwa Mulungu zimene anali nazo pamene analapa tchimo lake.
Zimakhalira chonchi nthawi zonse.
Wokhulupirira akuyenera kulapa moona mtima kwa Mulungu, kukhulupirira kuti Khristu wakonza kale milandu yake ndi mwazi wake.
Ndipo akuyenera kukhala mbali imodzi ndi Mulungu motsutsana ndi tchimo, kumuyamika Iye pa kupereka Mwana wake kufera tchimolo pa mtanda, ndi kukhulupirira mu mtima mwake kuti Iye wakhululukira tchimolo chifukwa cha Khristu, molingana ndi Mau ake.
Ndipo Mulungu adzabwenzeretsa mtendere wake.
Ngati mudzipereka nokha mwatsopano kwa Mulungu kuti Iye akutengeni ndi kukupangani chimene Iye afuna kuti mukhale,
Iye adzakulimbikitsani ndi kukupatsani chimwemwe chakudziwa kuti ndinu wake kwamuyaya.
Lankhulanani naye pafupipafupi.
Khalani ndi nthawi yokwanira kuwerenga ndi kulingalira pa Mau ake.
Chimenechi chidzakhala chakudya cha moyo wanu, chimwemwe cha mtima wanu, chilimbikitso cha munthu wamkati mwanu komanso kuwala kwa panjira panu.
Phunziro la munthu wachiwiri: Kupezanso chimwemwe
“Ine ndikufuna kuti mundipempherere chifukwa zaka zapitazo ndinali ndi chitsimikizo kuti ndinali wopulumutsidwa, koma kenako ndinabwerera m’mbuyo ndipo ndimakhala moyo wa uchimo kwa zaka zingapo.
Miyezi ingapo yapitayo ndinatopa nalo tchimo komanso dziko lapansi ndipo ndinapemphera ndi kumufunsa Mulungu kuti andikhululukire chifukwa kuti ndinachoka pamaso pake.
Ndikhulupirira anandikhululukira, koma pazifukwa zina, ndilibe mtendere umene ndinali nawo pa chiyambi.
Chikaiko chikumandipeza kuti mwina sindinamkhulupirire Yesu kwathunthu.
“Izi ndi zomwe ndinakumana nazo.
Pamene ndimapemphera ndinaona dzanja likulemba dzina langa.
Ndinalekeza kaye kupempherako kufikira zimenezi zitatha.
Ndipo ndinalankhula mokweza mau, “zikomo Mulungu.”
Tsiku lotsatira ndinakhala nthawi yaitali kugwada pansi ndi kumuyamika Iye.
Ndinali ndi chikhulupiriro chonse kuti dzina langa linalembedwa m’buku lamoyo.
Ndinali wosangalala ndipo ndinauza wina aliyense kuti Mulungu wandipulumutsa.
Ndipo ndinayamba kuwerenga Baibulo langa ndipo kwa nthawi yoyamba ndinamuwona Yesu monga momwe Iye akuvumbulutsidwira m’Baibulo.
Ndinali wokondwa kwa kanthawi, koma kenako ndinayamba kudzilala ndi kuchoka pamaso pake.
Ndakhala ndili wodabwa kuti ndi chifukwa chiyani ndinachimwa ngatidi ndinali wopulumutsidwa.”
Pali zinthu ziwiri zimene mukuyenera kudzionetsetsa pofuna kumvetsetsa zimene inu munakumana nazo komanso chifukwa chimene munali wokayikira.
Choyamba inu mukutengera chitsimikizo chanu pa zimene mukuziona, m’malo mwa ntchito yakutha kale ya Khristu.
Zooneka ndi maso, zingakongole maka, sizingakhale maziko a chitetezo chathu cha muyaya kapenanso chiyambi cha chitsimikizo chenicheni.
Khristu anafera machimo athu;
chokhachi ndicho chiyambi cha chitetezo chathu.
Iye anafera machimo athu ndipo anatenga chitonzo ndi chiweruzo zimene zinatiyenera ife osati chifukwa cha machimo athu okha komanso chikhalidwe chathu cha uchimo.
Machimo, kaya m’kuganiza, m’kulankhula ndi m’kuchita, ndi zotsatira za chikhalidwe chathu cha uchimo.
Inu mukanakhala ndi chikhalidwe cha chiyero sibwenzi mukuchimwa chifukwa chikhalidwe chanu cha chiyerocho chikanalimbana ndi tchimolo kuti mukakane yesero lililonse la uchimo.
Zimenezi ndi zomwe timaona mwa Khristu.
Iye anali ndi chikhalidwe cha chiyero kotero kuti anagonjetsa yesero lililonse.
Chakudya chake chinali kuchita chifuniro cha Atate wake.
Iye sanafune kuchita chifuniro chake koma cha Atate amene anamutuma Iye (Yohane 4:34; 5:30).
Koma tili ndi chikhalidwe chakugwa chimene chimakonda kuchita chifuniro chake komanso chimafuna kukhala ndi njira yake posatengera kuti zikondweretsa Mulungu kapena ayi.
Khristu sanangofera machimo athu kokha, komanso chikhalidwe chathu cha uchimo chinayenera kutsutsidwa ndi kuweruzidwa mwa imfa.
Pamene Khristu anali pa mtanda chifukwa cha inu, machimo anu onse (akale, atsopano ndi amtsogolo) anali pamaso pa Mulungu.
Chowonjezera chi chiyani, chikhalidwe chanu cha uchimo ndi malingaliro onse a uchimo, zakumva komanso kuchita zonse zinali pamaso pake;
pakuti Mulungu amaona za mtsogolo ndi za m’mbuyo momwe.
Nthawi simawerengedwa ndi Iye.
Khristu anatenga malo anu ndipo Mulungu anachita naye m’malo mwa inu.
Iye anachita naye Khristu monga ngati ndi inuyo, ndipo wachita zimene inuyo munachita, mukuchitabe komanso zimene mudzachita mtsogolomo.
Zimenezi ndi zomwe 2 Akorinto 5:21 akutanthauza:
“Ameneyo sanadziwa uchimo anamyesera uchimo m’malo mwathu.”
Kuonjezera pamenepa, Iye anatsutsa chikhalidwe chathu cha uchimo ndipo anachiweruza ku imfa.
Mwa chisomo chake chachikulu ndi chikondi chake kwa ife, Mulungu anapereka chigamulo chake cha imfa chimene chinayenera kubwera kwa ife ndipo chinapita kwa Khristu.
Chimenechi ndi chifukwa chake analira mowawidwa,
“Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?” (Mateyu 27:46).
Iye anasiyidwa chifukwa cha zimene inuyo muli komanso zimene mumachita.
Iye anatenga malo anu natenganso machimo anu.
Mukamaona Khristu akupachikidwa pamenepo ndipo watenga chiweruzo cha Mulungu pa machimo anu, mukuyenera kunena,
“Imfa ndi chiweruzo zili kumbuyo kwanga.”
Kodi Khristu ali kuti tsopano?
Kodi ndi wakufa?
Ayi ndithu, Iye ali kudzanja lamanja la Mulungu.
Mulungu anaika machimo anu pa Iye ndipo anamuweruza m’malo mwanu.
Kodi zikanatheka Yesu kukapezeka mu ulemerero pakanakhala kuti pali tchimo lina limene latsalira limene Mulungu sanakhutitsidwe nalo?
Ayi ndithu!
Mulungu sakanalola kuti Iye apezeke pamaso pake machimo anu akanakhala kuti adakali pa Iye.
Kotero chimenechi ndi chinthu chachikulu kuchiona:
“amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, naukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama” (Aroma 4:25).
Pamene Khristu anapachikidwa pa mtanda anatenga machimo anu onse, koma pamene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, chinali chifukwa chakuti machimo anu onse ayeretsedwa kwathunthu ndi mwazi wake.
Palibenso tchimo lina limene lidzaweruzidwa pa inu tsopano pakuti mwakhulupirira mwa Khristu, chifukwa Mulungu waweruza machimo onse pa Khristu amene chilango chake anasenza Iye.
Khristu anasiya machimo onse ndi chiweruzo chake anazisiya m’mbuyo pamene Iye anauka kwa akufa nakhala kudzanja la manja la Mulungu.
Chomwecho tsopano mwalungamitsidwa ndi kuchotseredwa tchimo.
Ku Yohane 5:24 Khristu akulankhula,
“Indetu, indetu ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nawo moyo wosatha, ndipo salowa m’kuweruza, koma wachokera ku imfa, nalowa m’moyo.”
Chifukwa chiyani?
Chifukwa Iye anapezeka wolakwa naweruzidwa m’malo mwathu ndipo anatenga chilango chathu chonse pa mtanda.
Tsopano pakuti Iye wauka, onse okhulupirira mwa Iye achoka ku imfa nalowa m’moyo.
Mfundo yina yaikulu yofunika kuyiona ndi yakuti pamene mwalandira Khristu mumalandiranso moyo watsopano mwa Iye.
Inu “munakhala amoyo.”
Mzimu wa Mulungu amakupangani kutenga nawo gawo ku moyo umene Khristu analandira pamene anaukitsidwa kwa akufa.
N’chifukwa chake timawerenga ku Akolose 2:13,
“Ndipo inu, pokhala akufa m’zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, anakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, m’mene adatikhululukira ife zolakwa zonse.”
Mulungu anakupatsani moyo watsopano pamodzi ndi Khristu.
Munali akufa m’machimo anu.
Pamenepo panalibe moyo wa Mulungu, koma tsopano wakupangani kukhala ndi moyo kudzera m’moyo womwewo umene anapereka kwa Khristu pamene anamuukitsa kwa akufa.
Tsopano moyo umenewu, umene mwalandira pamodzi ndi Khristu, sungabwerenso pansi pa chiweruzo pakuti Khristu analandira moyo umenewu atadutsa kale m’chiweruzo ndipo zonse anazisiya m’mbuyo.
Timaima pamaso pa Mulungu wodziwika ndi Khristu amene analandiridwa kudzanja la manja atadutsa mu imfa ndi m’chiweruzo.
Amenewa ndiwo maziko a kuvomereza pamaso pa Mulungu ndipo pamenepa ndi pomwe mukuyenera kuyang’anira chitsimikizo chanu.
Inu muli mwa Khristu.
Imfa yake ndi yanu, moyo wake ndi wanunso ndipo malo ake wovomerezedwa kudzanja la manja la Mulungu ndi anunso.
Choncho sikuti muli ndi malo atsopano okha pamaso pa Mulungu mwa Khristu amene anaukitsidwa kwa akufa, komanso muli ndi moyo watsopano mwa Iye.
Chikhalidwe cha moyo watsopano umenewu ndiko kukonda Mulungu ndi kudana nalo tchimo.
Chimenechi ndi chifukwa chake mumakhala munthu womvetsa chisoni komanso wosakondwa pamene munabwerera m’mbuyo.
Ngakhale kuti munabadwa kwatsopano ndipo muli ndi chikhalidwe chatsopano, inutu mudakali ndi chikhalidwe chakale cha uchimo.
Zimenezi zikuwerengera kutsutsana konse kwa mkati mwanu.
Chikhalidwe chatsopano chimadana ndi tchimo, ndipo chikhalidwe chakale chimakonda tchimo.
Pambali pa zonsezi chikumbumtima chanu sichimagwirizana ndi tchimo ndipo Mzimu Woyera amakhalira mwa inu kukutsutsani za tchimo lanu ndi kukupangitsani kuti mukhale osasangalala chifukwa cha tchimolo.
Inu munawaona machimo anu ndi kuwakhudza ndipo munayamba kudzifunsa nokha:
“Ngati ndine wopulumutsidwa chifukwa chiyani ndi kupanga zinthu izi?”
Chokhacho chakuti inu munadzifunsa nokha funso limeneli mukuonetsa kuti mukufuna kudziwa ngati ndinu wopulumutsidwa kudzera mu ukadaulo wanu m’malo moyang’ana pa zimene Khristu anakuchitirani.
Chipulumutso chanu, kuvomereza kwanu, komanso chitetedzo chanu zimatengera pa Khristu ndi ntchito yake pa inu ya pa mtanda paja, osati pa zimene inu mukuchita.
Koma ngati mudzipereka nokha ku chikhalidwe chanu chakale ndi tchimo lanu, zimakupangitsani kukhala munthu wosasangalala.
Inutu simumataya chipulumutso chanu kapena chitetedzo chanu, koma mumataya chisangalalo chanu.
Kodi choyenera kuchita tsopano ndi chiyani?
Mukuyenera kuvomereza machimo anu kwa Mulungu, dziweruzeni nokha ndipo perekani chifuniro chanu kwa Iye;
pamenepo mudzakhalanso wokondwa.
Mwina simungakhale wokondwa monga munalili poyamba, komabe mudzakhala ndi mtendere weniweni wa mumtima.
Kodi mungathe bwanji kugonjetsa chikhalidwe chanu chakale kuti musadzabwererenso m’mbuyo?
Osati pa kulimbana nacho ayi kapena kumenyana nacho.
Ngati mungayetsetse kufuna kulimbana nacho pogwiritsa ntchito mphamvu zanu mulephera.
MPHAMVU YA CHIGONJETSO PA TCHIMO
Mphamvu ya chigonjetso pa chikhalidwe chathu chakale ili mwa Khristu.
Komatu tisanakonzekere kubwerera kwa Khristu kukapeza mphamvu tikuyenera kuphunzira kaye kuchokera mu zofooka zathu.
Kumvetsetsa zofooka zathu
Ku Aroma 7:15-25 Paulo akufotokozera za kusakondwa kwa munthu amene akuvutika ndi tchimo limene iye amadana nalo, ndipo mwa iye sakuipeza mphamvu yogonjetsera tchimolo.
Munthu aliyense wobadwa mwatsopano, asanaphunzire chinsinsi cha chigonjetso chimene chimapezeka mu mphamvu ya Khristu mwa Mzimu wake, amadutsa munyengo yokhumudwitsa imeneyi yopereka mpata ku tchimo.
Mkati mwake amadana ndi kuvutika nalo tchimolo, ndipo mwachisoni amaphunzira kuti mwa iye yekha alibe mphamvu yogonjetsera tchimolo ngakhale atayetsetsa mwa njira zake kuti asagwenso mu tchimolo.
Mafotokozedwe a Paulo pa kulimbana kumeneku akutitsogolera kupeza njira ya Mulungu ya mamasulidwe ndi chipambano mwa Khristu:
“Pakuti chimene ndichita sindichidziwa; pakuti sindichita chimene ndifuna, koma chimene ndidana nacho ndichichita ichi. Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, ndivomerezana nacho chilamulo kuti chili chabwino. Ndipo tsopano si ine ndichichita, koma uchimo wakukhalabe mkati mwanga ndiwo. Pakuti ndidziwa kuti mkati mwanga, ndiko mthupi langa simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza. Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna chimenecho ndichichita. Koma ngati ndichita chimene sindichifuna sindinenso amene ndichichita, koma uchimo wakukhalabe mkati mwanga ndiwo. Ndipo chotero ndipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna chabwino, choipa chiliko. Pakuti monga mwa munthu wa mkati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiwona lamulo lina mziwalo zanga lili kulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziwalo zanga. Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani mthupi la imfa ili? Ndiyamika Mulungu mwa Yesu Khristu Ambuye wathu” (Aroma 7:15-25).
Ndime zimenezi zikufotokozera za malamulo atatu:
lamulo la Mulungu, lamulo la mtima wanga komanso lamulo la uchimo.
Lamulo la Mulungu ndilo vumbulutso limene linapatsidwa kwa munthu mwa chifuniro cha Mulungu.
Lamulo la mtima ndilo kugwira ntchito kofanana kwa chikhalidwe cha umulungu mwa aliyense wobadwanso kwatsopano chimene chimakondwera mu chifuniro cha Mulungu ndi kudana nalo tchimo.
Lamulo la uchimo ndiyo ntchito ya chikhalidwe chakale chimene chimafunabe kuchita njira zake posaganizira chifuniro cha Mulungu.
Lamulo la uchimo pamenepa likufotokozedwa kuti likukhala “m’ziwalo zanga,” pamene chisangalalo chimene ali nacho mu lamulo la Mulungu (limene mu ndime 23 likutchulidwa “lamulo la mtima wanga”) likunenedwa kuti lili “mkati mwake.”
Chikhalidwe chatsopano cha umulungu chimene aliyense wobadwa kwatsopano ali nacho ndicho chiyambi cha chisangalalo chimenechi mu lamulo la Mulungu ndi kudana ndi tchimo, chimene chimamupangitsa kusautsika ndi tchimo logwirabe ntchito mu chikhalidwe chake chakale.
Chikhalidwe chatsopano chimenechi chimatengedwa kukhala mzoonadi zake umwini weniweni – “mkati mwake” – chimene iye ali tsopano mwakuya kapena mkatikati mwa umunthu wake wokonzedwanso.
Makhalidwe awiri amenewa – chikhalidwe chatsopano cha umulungu chimene m’Khristu aliyense analandira kuchokera kwa Mulungu pamene anabadwanso mwatsopano, komanso chikhalidwe chakale chimene chinatengedwa kuchokera kwa Adamu mwa chibadwidwe – zimasiyana china ndi chinzake ndipo ndi zotsutsana pa zokhumba zake ndi zolinga zake.
China chimakonda ndi kukangamila kuchimwa pamene chinacho chimakonda ndi kukangamila kuchita chifuniro cha Mulungu.
Chikhumbokhumbo chimenechi cha chilengedwe chatsopano kuchita chifuniro cha Mulungu chimalimbikitsa kulimbana ndi tchimo limene chikhalidwechi limadana nalo, komanso limampangitsa m’Khristu kukhala wotsutsika ndi wokhumudwa pamene wadzipereka yekha ku uchimo.
Chinthu china chofunika kuchiona pa kulimbana kumene kwafotokozedwa ku Aroma 7:15-25 ndi chakuti sakutchulapo zokhudza Khristu kapena Mzimu Woyera.
Wokhulupirira akuvutika ndi chikhalidwe chake chakale mwa mphamvu zake popanda kuyang’ana kwa Khristu kapena kuwerengera pa Iye kuti ampatse mphamvu mwa Mzimu Woyera kutsutsana ndi tchimo.
Machitidwe amenewa olimbanalimbana ndi kugonjetsedwa, amachitika kwa zaka ndithu, ndipo ndi wochititsa manyazi komanso wopweteka, koma pali maphunziro a mtengo wapatali amene akutchulidwa mu ndime 18 amene tikuwaphunzira:
“Pakuti ndidziwa kuti mkati mwanga, ndiko m’thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza.”
Mwanjira ina mukubwereza kwa kulimbana kumeneku, iye anafika pa mlingo wozindikira kuti mu chikhalidwe chake cha uchimo ndi chakugwa (chimene anachipeza mwachibadwidwe kuchokera kwa Adamu) mulibemo chabwino.
Chikhalidwe chimenechi chimakonda kuchimwa ndi kuchita zoipa.
Kuonjezera pamenepa, ngakhale kuti ali nacho chikhalidwe chatsopano chimene chimachita zosangalatsa Mulungu ndi kudana ndi uchimo, iye payekha alibe mphamvu yogonjetsera chikhalidwe chake chakale.
Choyamba, akuphunzira kuti mwa chilengedwe, mwa iye mulibe chabwino, ndipo chachiwiri ndi chakuti ngakhale kuti iye anapatsidwa gawo lakukhala chikhalidwe cha umulungu, alibe mphamvu mwa iye yekha kuchita chifuniro cha Mulungu chimene chikhalidwe chake chatsopano chikukhumba.
Atatha kuphunzira phunziro lowawa la chikhalidwe chake cha uchimo komanso kosoweka mphamvu kwake yogonjetsera tchimo mwa mphamvu zake, iye akulira mopanda chiyembekezo,
“munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani mthupi la imfa ili?”
Tsopano iye wamphunzira kuti ngati akufuna chigonjetso pa tchimo m’moyo mwake, mphamvu yake ikuyenera kuchokera kwina kwake osatinso mwa iye.
Munthu wina akuyenera kubwera mwa iye ndi kumupatsa mphamvu ya mamasulidwe ndi chigonjetso.
Pamene wokhulupirira wayamba kuyang’ana thandizo kuchokera kwina osati mwa iye yekha, maso ake amapenya mwa chindunji kwa Yesu Khristu amene amamutenga kukhala Ambuye.
Inde, Khristu ndiye yankho la kulira kwake uku kopanda chiyembekezo,
“adzandilanditsa ndani?”
kusintha kodabwitsa kuchoka ku kukhumudwa ndi kupita ku kuyamika!
Pamene iye awona zimenezi amalankhula kuti,
“Mayamiko apite kwa Mulungu – kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.”
Iye ali yekhayo amene akhoza kutimasula ife kuchoka ku kutsutsika ndi ku mphamvu ya uchimo.
Palibe kutsutsika
Kukhumudwa kwakukulu pamene tikudutsa munyengo ya kulimbana ndi tchimo kumabwera chifukwa cha chikumbumtima chowirikiza mwa m’Khristu chimene chimamutsutsa chifukwa cha kupereka mpata ku tchimo.
Ndipo ndi zololeka kuti chikumbumtima chake chidzimutsutsa ndithu, osati pa tchimo lokha limene wachita komanso chifukwa chakulephera kuchita chabwino pamene anayenera kutero.
Mfundo yaikulu komanso ya ulemerero wa uthenga wa chisomo cha Mulungu ndi yakuti, ngakhale kuti chikumbumtima cha wokhulupirira chikuyenera nthawi zonse kutsutsa tchimo ndi kulephera kwake, Mulungu samamutsutsa chifukwa cha chimenechi.
Mulungu nthawi zonse amamuona wokhulupirira mwa Khristu monga amene wadutsa kale, ndipo anamuchotsera kwamuyaya, kutsutsika kulikonse komanso chiweruzo chimene chinayenera pa iye chifukwa cha uchimo.
Chotero iye amakhala mfulu nthawi zonse kupyola pa kutsutsika ndi chiweruzo.
Zimenezi zikuoneka zabwino zitakhala zoonadi, choncho malingaliro oyamba amene timakhala nawo tikamva mfundo imeneyi ndi akuti,
“zimenezi sizingakhale zoona. Mulungu akuyenera kutsutsa tchimo basi.”
Indedi ndi zoona kuti Mulungu akuyenera kutsutsa tchimo, koma mfundo yodabwitsa ndi yakuti, Iye anaweruza kale tchimo lathu pamene Khristu anatenga malo athu pa mtanda paja.
Ifetu tinafa mwa Munthu dzina lake Khristu, amene anakhala Mlowam’malo wathu.
Imfa ya Khristu inatengedwa ngati yathu yomwe pamaso pa Mulungu.
Chotero ife sitilinso pansi pa kutsutsika chifukwa cha chikhalidwe chathu chakale komanso machimo athu:
“Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa” (Aroma 8:1).
Chiyambi chokhacho cha mphamvu
Khristu ndiye yankho lokhalo la kuvutika kwathu pokhudzana ndi tchimo.
Pa Iye yekha ndi mphamvu imene ife timaifuna pa chigonjetso.
Mpumulo wodabwitsa umene ife timaupeza kuchokera m’kukhumudwa kwathu, chigonjetso chodabwitsa chimene ife timachipeza pamene tidzipereka tokha kwathunthu kwa Iye pa kumulola kuti atimasule mwa mphamvu zake ku ukapolo wa tchimo.
Ngati takakamilabe pa kudzidalira tokha ndi kuvutika mwa mphamvu zathu, timamutsekereza Iye kugwira ntchito mwa mphamvu m’moyo mwathu kudzera mwa Mzimu wake.
Khristu anatipatsa chitsanzo chabwino cha momwe mphamvu imeneyi imagwirira ntchito ku Yohane 15 pamene anagwiritsa ntchito chithunzithunzi cha mpesa ndi nthambi zake:
“Monga nthambi singathe kubala chipatso pa yokha, ngati sikhala mwa mpesa; motero mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine. Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake; wakukhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kuchita kanthu” (Yohane 15:4-5).
Taonani maphava akuluakulu a mpesa amene amakhala pa nthambi.
Kodi nthambi imeneyo imatenga mphamvu kuti zoberekera zipatso zodabwitsa choncho?
Osatitu kudzera mu kuyetsetsa kwake ayi, koma pakukhalabe mophatikana ndi mpesawo, umene umapereka chakudya chokwanira ku nthambi imene ikubereka zipatsozo.
Chotero chimodzimodzinso ndi m’Khristu.
Iye pa yekha alibe mphamvu ya kubereka zipatso, ngakhale kuti mu chikhalidwe chake chatsopano amafunitsitsa kutero.
Kuyetsetsa kwake mu mphamvu zake kumakathera m’kulephera kokhumudwitsa.
Koma akazindikira za kusoweka kwa mphamvu zake, amasiya kuyetsetsa kwake ndipo amayang’ana kwa Ambuye, mphamvu imasefukira kuchokera mwa Iye kudutsira mwa Mzimu Woyera kupereka chigonjetso pa uchimo ndi kubereka chipatso m’moyo mwake, pamenepo chimwemwe ndi mtendere zimabwera.
Tili nacho chitsanzo china cha zimenezi pamene Petro anayenda pamadzi ku Mateyu 14:28-33.
Petro analibe mphamvu pa iye yekha ya kuyenda pamadzi ndipo iye anadziwa za chimenechi.
Koma pamene anaikabe maso ake pa Ambuye, Ambuyeyo anamugwiridzitsa mwa mphamvu yake m’kuyenda konse kumene iye amayenda.
Pamene Petro anachotsa maso ake pa Ambuye anayamba kumila.
Kodi iye anapanga chiyani?
Anayetsetsabe pa yekha kulimbana nazo?
Ayi ndithu.
Iye anachita chinthu chokhacho cha nzeru chimene anayenera kuchita.
Anaitanira pa Ambuye ampulumutse kuti asamile, pomwepo Ambuye anatambasula dzanja lake ndi kumunyamula.
Chomwechonso miyoyo yathu ya uzimu.
Ifetu patokha tilibe mphamvu ya kuyenda mwa ngwiro.
Koma tikapitilira kudalira pa Ambuye ifeyo nkupatukapo, Iye adzatipatsa mphamvu mwa Mzimu Woyera kukayendabe mwa ulemerero wake.
Ngati tilephera kuchita zimenezi ndi kuyamba kumila, kodi tikuyenera kuchita chiyani?
Tiyeni tililire thandizo kwa Iye monga anachitira Petro;
Iye adzatinyamulanso.
Tiyeni tisaiwalire kuti Khristu ndi yankho la china chilichonse chimene chimatisautsa.
Kopanda Iye sitingathe kuchita kanthu kalikonse (Yohane 15:5).
Pamene tipitilira kulumikizana ndi Iye timapeza chipambano, mtendere ndi chimwemwe zochuluka pa miyoyo yathu.
Makhalidwe Awiri a Wokhulupirira
Pamene tabadwanso kwatsopano, timakhala wotenga nawo gawo mu chikhalidwe chatsopano cha umulungu – chimene chimakonda Mulungu ndi kudana ndi tchimo.
Koma chimachitika ndi chiyani ndi chikhalidwe chathu chakale cha uchimo?
Funso lofunikira limeneli likuyankhidwa pamene tikuona maphunziro awiri okhudzana ndi chitsimikizo cha chipulumutso chathu, komanso pa kufotokozera za mphamvu imene imafunikira kuti tigonjetse tchimo.